PHUNZIRO 07
Kodi Yehova Ndi Wotani?
Kodi inuyo mumaganiza kuti Yehova Mulungu ndi wotani? Kodi mumaona kuti ndi wogometsa kwambiri ndipo ali kutali ndi inu ngati mmene ziliri nyenyezi kumwamba? Kapena kodi mumaona kuti ndi wamphamvu kwambiri ngati mabingu ndipo alibe makhalidwe abwino alionse? Koma kodi Yehova ndi wotani? Yehova amafotokoza makhalidwe ake m’Baibulo, ndipo amasonyeza kuti amakukondani.
1. N’chifukwa chiyani sitingathe kumuona Mulungu?
“Mulungu ndiye Mzimu.” (Yohane 4:24) Yehova alibe thupi ngati lathuli. Iye ndi Mzimu ndipo amakhala kumwamba kumene sitingaoneko.
2. Kodi ndi makhalidwe ena ati amene Yehova ali nawo?
Ngakhale kuti Yehova sitingamuone, iye alipo ndithu ndipo ali ndi makhalidwe amene amatichititsa kuti tizimukonda kwambiri. Baibulo limanena kuti: “Yehova amakonda chilungamo, ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.” (Salimo 37:28) Limanenanso kuti iye ndi “wachikondi chachikulu ndi wachifundo,” makamaka kwa anthu amene akuvutika. (Yakobo 5:11) “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.” (Salimo 34:18) Kodi mukudziwa kuti zomwe anthufe timachita zimakhudza Yehova? Munthu amene amasankha kuchita zoipa amachititsa kuti Mulungu azikhumudwa ndiponso kumva chisoni. (Salimo 78:40, 41) Koma munthu amene amachita zabwino amasangalatsa Mulungu.—Werengani Miyambo 27:11.
3. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amatikonda?
Khalidwe lalikulu kwambiri la Yehova ndi chikondi. Ndipo Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Timaona umboni wakuti Yehova amatikonda tikamawerenga Baibulo komanso tikamaona zimene analenga. (Werengani Machitidwe 14:17.) Chitsanzo ndi mmene anatilengera. Mwachitsanzo, anatilenga kuti tizitha kuona kukongola kwa mitundu yosiyanasiyana ya zinthu, kumva nyimbo zabwino, ndiponso kumva kukoma kwa chakudya. Zimenezi zikusonyeza kuti amafuna kuti tizisangalala ndi moyo.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe chimene Yehova amagwiritsira ntchito kuti apange zinthu zodabwitsa. Kenako onani mmene Yehova amasonyezera makhalidwe ake ochititsa chidwi.
4. Mzimu woyera ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito
Yehova amagwiritsa ntchito mzimu woyera ngati mmene ifeyo timagwiritsira ntchito manja athu. Baibulo limasonyeza kuti mzimu woyera si munthu, koma ndi mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito. Werengani Luka 11:13, ndi Machitidwe 2:17, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
-
Mulungu ‘amatsanulira’ mzimu wake woyera kwa anthu amene amamupempha. Kodi inuyo mukuganiza kuti mzimu woyera ndi munthu kapena ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito? N’chifukwa chiyani mukutero?
Yehova amagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti apange zinthu zodabwitsa kwambiri. Werengani Salimo 33:6 ndi 2 Petulo 1:20, 21, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi Yehova anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera m’njira zina ziti?
5. Yehova ali ndi makhalidwe abwino
Mose ankatumikira Mulungu mokhulupirika, koma ankafuna kumudziwa bwino Mlengi wakeyu. Choncho Mose anapempha kuti: “Ndidziwitseni njira zanu, kuti ndikudziweni.” (Ekisodo 33:13) Poyankha, Yehova anathandiza Mose kudziwa makhalidwe ake ena. Werengani Ekisodo 34:4-6, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
-
Kodi Yehova anathandiza Mose kuzindikira makhalidwe ati?
-
Nanga ndi makhalidwe ati a Yehova amene amakusangalatsani kwambiri?
6. Yehova amakonda kwambiri anthu
Aheberi, omwe anali anthu a Mulungu anali akapolo ku Iguputo. Ndiye kodi Yehova ankamva bwanji iwowo akamavutika? MVETSERANI ndipo muzitsatira, kapena werengani Ekisodo 3:1-10. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
-
Kodi nkhaniyi ikusonyeza kuti Yehova amamva bwanji anthu akamavutika?—Onani vesi 7 ndi 8.
-
Kodi inuyo mukuganiza kuti Yehova amafunadi kuthandiza anthu ndipo angawathandizedi? N’chifukwa chiyani mukutero?
7. Zinthu zam’chilengedwe zimasonyeza makhalidwe a Yehova
Yehova amasonyeza makhalidwe ake kudzera m’zinthu zimene analenga. Onerani VIDIYO. Ndipo werengani Aroma 1:20, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi ndi makhalidwe ati a Yehova amene mumaona m’zinthu zimene iye analenga?
ZIMENE ENA AMANENA: “Mulungu si munthu, koma wangokhala mphamvu imene imapezeka paliponse.”
-
Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
-
Nanga n’chifukwa chiyani mukuganiza choncho?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yehova ndi Mzimu ndipo sitingamuone, ali ndi makhalidwe abwino ambiri ndipo khalidwe lake lalikulu ndi chikondi.
Kubwereza
-
N’chifukwa chiyani sitingathe kumuona Yehova?
-
Kodi mzimu woyera n’chiyani?
-
Tchulani makhalidwe ena amene Yehova ali nawo.
ONANI ZINANSO
Dziwani zambiri zokhudza Yehova pophunzira makhalidwe 4 ochititsa chidwi amene ali nawo.
“Kodi Mulungu Ali Ndi Makhalidwe Otani?” (Nsanja ya Olonda Na. 1 2019)
Onani umboni wotsimikizira kuti Yehova samangopezeka paliponse nthawi ina iliyonse.
“Kodi Mulungu Amangopezeka Pena Paliponse?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani chifukwa chake Baibulo limayerekezera mzimu woyera ndi manja a Mulungu.
Munthu wina wa vuto losaona ankaganiza kuti Mulungu samamukonda. Taonani zimene zinamuthandiza kuti asinthe maganizo akewa.
“Panopa Ndimaona Kuti Ndingathe Kuthandiza Ena” (Nsanja ya Olonda, October 1, 2015)
MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE—KUPHUNZIRA BAIBULO MOKAMBIRANA