PHUNZIRO 11

Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikuthandizani Kwambiri?

Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikuthandizani Kwambiri?

Kodi munayamba mwapatsidwapo ntchito yaikulu koma munkachita mantha kuyamba kuigwira? N’kutheka kuti ntchitoyo munaigawa pang’onopang’ono kuti mukwanitse kuigwira. Ndi mmenenso mungachitire kuti mukwanitse kuwerenga Baibulo. Mwina mungadzifunse kuti, ‘Ndiye ndingayambire pati?’ M’phunziroli tikambirana njira zosavuta zimene zingakuthandizeni kuti muzisangalala mukamawerenga ndi kuphunzira Baibulo.

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuwerenga Baibulo tsiku lililonse?

Munthu amene amawerenga Baibulo kapena kuti “chilamulo cha Yehova” tsiku lililonse amakhala wosangalala komanso zinthu zimamuyendera bwino. (Werengani Salimo 1:​1-3.) Kuti zimenezi zitheke, mungayambe ndi kuwerenga Baibulo kwa maminitsi ochepa tsiku lililonse. Zimenezi zidzakuthandizani kuti muwadziwe bwino Mawu a Mulungu ndipo kuwerenga Baibulo kudzayamba kukusangalatsani kwambiri.

2. Kodi mungachite chiyani kuti kuwerenga Baibulo kuzikuthandizani?

Kuti kuwerenga Baibulo kuzitithandiza kwambiri, tiziima kaye n’kuganizira zimene tikuwerengazo. Tiziwerenga ndi “kusinkhasinkha.” (Yoswa 1:8) Choncho, mukamawerenga Baibulo muzidzifunsa mafunso monga awa: ‘Kodi zimene ndikuwerengazi zikundiphunzitsa zotani zokhudza Yehova Mulungu? Kodi ndingazigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanga? Kodi mfundo za m’mavesiwa ndingazigwiritse ntchito bwanji pothandiza ena?’

3. Kodi mungatani kuti muzipeza nthawi yowerenga Baibulo?

Kodi zimakuvutani kuti mupeze nthawi yowerenga Baibulo? Ambirife zimativuta. Muziyesetsa ‘kugwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.’ (Aefeso 5:16) Kuti mukwanitse kuchita zimenezi, muzisankha nthawi yoti muziwerenga Baibulo tsiku lililonse. Anthu ena amakonda kuwerenga Baibulo m’mamawa. Ena amakonda kuwerenga chakumasana, mwina pa nthawi yopuma. Pomwe ena amakonda kuwerenga chakumadzulo asanakagone. Nanga inuyo mungakonde kumawerenga nthawi yanji?

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani zimene mungachite kuti muzisangalala kwambiri mukamawerenga Baibulo. Phunzirani zimene mungachite kuti muzikonzekera bwino n’cholinga choti kuphunzira Baibuloku kuzikuthandizani kwambiri.

Mofanana ndi mmene tingachitire kuti tiyambe kukonda zakudya zosiyanasiyana, n’zotheka kuyamba kukonda kuwerenga Baibulo

4. Muzikonda kuwerenga Baibulo

Tingavutike kuti tiyambe kuwerenga Baibulo. Komabe, titha kukhala ndi mtima ‘wolakalaka’ kuliwerenga ngati mmene munthu amachitira kuti ayambe kukonda chakudya chimene sanadyepo. Werengani 1 Petulo 2:​2, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mukuona kuti kuwerenga Baibulo tsiku lililonse kungakuthandizeni kuti muyambe kulikonda kwambiri n’kumalakalaka kuwerenga zambiri?

Onerani VIDIYO kuti muone mmene anthu ena anayambira kukonda kuwerenga Baibulo. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

  • Muvidiyoyi, kodi achinyamatawa anakwanitsa kuthana ndi mavuto ati?

  • Ndi zinthu ziti zimene zinawathandiza kuti asasiye kuwerenga Baibulo tsiku lililonse?

  • Nanga ankachita chiyani kuti kuwerenga Baibulo kuziwasangalatsa?

Zokuthandizani kuti muyambe kuwerenga Baibulo:

  • Sankhani Baibulo lomasuliridwa molondola komanso lomveka bwino. Yesani kuwerenga Baibulo la Dziko Latsopano ngati lilipo m’chinenero chanu.

  • Yambani ndi kuwerenga buku limene limakusangalatsani kwambiri. Kuti muchite zimenezi, onani tchati chakuti “Yambani Kuwerenga Baibulo.”

  • Muzichonga machaputala omwe mwawerenga. Gwiritsani ntchito tchati chakuti “Chongani Machaputala Omwe Mwawerenga” chomwe chili m’bukuli.

  • Gwiritsani ntchito pulogalamu ya JW Library®. Pulogalamuyi ingakuthandizeni kuti muziwerenga ndi kumvetsera Baibulo kulikonse pogwiritsa ntchito foni kapena zipangizo zina.

  • Muzigwiritsa ntchito zakumapeto mu Baibulo la Dziko Latsopano. Mupezamo mapu, matchati ndi matanthauzo a mawu ena. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzisangalala powerenga Baibulo.

5. Muzikonzekera zomwe mutaphunzire

Werengani Salimo 119:34, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani muyenera kupemphera musanayambe kuwerenga Baibulo kapenanso musanayambe kukonzekera phunziro la Baibulo?

Kodi mungatani kuti muzipindula kwambiri ndi phunziro lililonse? Mukamakonzekera phunziro lililonse, yesani kuchita izi:

  1. Werengani ndime zoyambirira.

  2. Werengani malemba amene aikidwawo ndipo yesani kuona kugwirizana kwake ndi nkhaniyo.

  3. Chekenirani yankho la funso lililonse; kuchita zimenezi kukuthandizani pamene mukukambirana phunziroli ndi mphunzitsi wanu.

Kodi mukudziwa?

A Mboni za Yehova akhala akugwiritsa ntchito Mabaibulo osiyanasiyana. Komabe, timakonda kugwiritsa ntchito Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika chifukwa ndi lolondola, lomveka bwino ndiponso limagwiritsa ntchito dzina la Mulungu.​—Onani nkhani yapawebusaiti yakuti, Kodi a Mboni za Yehova Ali Ndi Baibulo Lawolawo?

ZIMENE ENA AMANENA: “Kuwerenga Baibulo ndi chintchito chotopetsa. Sindingakwanitse chifukwa ndimatanganidwa kwambiri.”

  • Inuyo mukuganiza bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Kuti muzipindula ndi kuwerenga Baibulo, muzipeza nthawi yoliwerenga, muzipemphera kuti mulimvetse bwino ndiponso muzikonzekera musanayambe kuphunzira.

Kubwereza

  • N’chiyani chingakuthandizeni kuti muzipindula kwambiri powerenga Baibulo?

  • Ndi nthawi iti imene mungasankhe kuti muziwerenga ndi kuphunzira Baibulo?

  • N’chifukwa chiyani mukufunika kumakonzekera phunziro lililonse?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Pezani mfundo zina zimene zingakuthandizeni kuti muzipindula kwambiri powerenga Baibulo.

“Kodi Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikusangalatsani?” (Nsanja ya Olonda Na. 1 2017)

Anthu amene akhala akuwerenga Baibulo kwa nthawi yaitali angakuthandizeni kudziwa njira zinanso zowerengera Baibulo.

Kuphunzira Mwakhama (2:06)