PHUNZIRO 13

Zipembedzo Zonyenga Zimaphunzitsa Zabodza Zokhudza Mulungu

Zipembedzo Zonyenga Zimaphunzitsa Zabodza Zokhudza Mulungu

Zipembedzo zimene zimati zimachita zinthu ndi kulankhula m’dzina la Mulungu, zakhala zikuchita zinthu zoipa zambiri. N’chifukwa chiyani zipembedzozi zimachita zimenezi? Zoona zake n’zakuti zipembedzozi ndi zabodza. Zimene zimaphunzitsa ndi kunena zimachititsa anthu kukhulupirira zabodza zokhudza Mulungu. Kodi zipembedzozi zimachita bwanji zimenezi? Kodi Mulungu amamva bwanji akamaona zimene zipembedzozi zimachita? Nanga adzachita chiyani?

1. Kodi zimene zipembedzo zimaphunzitsa zimachititsa bwanji anthu kukhulupirira zabodza zokhudza Mulungu?

Zipembedzo zonyenga zakhala ‘zikusinthanitsa choonadi cha Mulungu ndi bodza.’ (Aroma 1:25) Mwachitsanzo, zipembedzo zambiri sizimaphunzitsa anthu dzina la Mulungu. Komatu Baibulo limaphunzitsa kuti tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. (Aroma 10:13, 14) Atsogoleri ena azipembedzo amanena kuti chinachake choipa chikachitika, chimakhala kuti ndi cholinga cha Mulungu. Koma limeneli ndi bodza. Mulungu si amene amachititsa zinthu zoipa. (Werengani Yakobo 1:13.) N’zomvetsa chisoni kuti mabodza amene zipembedzozi zimaphunzitsa amachititsa kuti anthu asamakonde Mulungu.

2. Kodi zimene zipembedzo zonyenga zimachita zimachititsa bwanji anthu kukhulupirira zabodza zokhudza Mulungu?

Zipembedzo zonyenga zimachitira anthu zinthu zoipa zambiri pomwe Yehova sachita zimenezi. Baibulo limanena kuti “machimo ake [azipembedzo zonyenga] aunjikana mpaka kumwamba.” (Chivumbulutso 18:5) Kwa zaka zambiri, zipembedzo zakhala zikuchita nawo ndale, kulimbikitsa nkhondo ndiponso kuchititsa kapena kuvomereza kuti anthu ambirimbiri aphedwe. Atsogoleri azipembedzo ena amafuna kulemera kwambiri ndipo amauza anthu a m’zipembedzo zawo kuti aziwapatsa ndalama. Zimene amachitazi ndi umboni wakuti Mulungu samudziwa ngakhale pang’ono choncho alibe ufulu wonena kuti ndi atumiki ake.​—Werengani 1 Yohane 4:8.

3. Kodi Mulungu amamva bwanji akamaona zimene zipembedzo zonyenga zimachita?

Ngati inuyo mumakhumudwa ndi zimene zipembedzo zonyenga zimachita, mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji? Yehova amakonda anthu koma amadana ndi atsogoleri azipembedzo amene amaphunzitsa anthu zabodza zokhudza iyeyo komanso kuchitira zoipa anthu amene ali m’chipembedzo chawo. Choncho akulonjeza kuti zipembedzo zonyenga zidzawonongedwa ndipo ‘sizidzapezekanso.’ (Chivumbulutso 18:21) Posachedwapa, Mulungu adzawononga zipembedzo zonse zonyenga.​—Chivumbulutso 18:8.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene Mulungu amamvera akaona zimene zipembedzo zonyenga zimachita. Phunzirani zambiri zokhudza zimene zipembedzozi zachita komanso chifukwa chake zimenezi siziyenera kukuchititsani kusiya kuphunzira za Yehova.

4. Kodi Mulungu amavomereza zipembedzo zonse?

Anthu ambiri amakhulupirira kuti zipembedzo zonse zili ngati njira zosiyanasiyana zimene zimafikitsa anthu kwa Mulungu. Koma kodi zimenezi n’zoona? Werengani Mateyu 7:13, 14, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi Baibulo limanena zotani zokhudza njira yotsogolera anthu kumoyo?

Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

  • Kodi Baibulo limanena kuti pali zipembedzo zambiri zimene zimasangalatsa Mulungu?

5. Zimene zipembedzo zonyenga zimachita sizisonyeza kuti Mulungu ndi wachikondi

Zipembedzo zakhala zikuchita zinthu zoipa zambiri zomwe zimachititsa anthu kuona kuti Mulungu alibe chikondi. Mwachitsanzo, zimalimbikitsa nkhondo komwe n’kulakwa kwakukulu. Kuti muone mmene zimachitira zimenezi, onerani VIDIYO. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

  • Kodi matchalitchi ambiri anachita zotani pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse?

  • Kodi mukumva bwanji mukaganizira zimene anachitazi?

Werengani Yohane 13:34, 35 ndi 17:16. Kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji zipembedzo zikamathandiza nawo pa nkhondo?

  • Zipembedzo zonyenga zimachita zinthu zoipa zambiri. Ndi zinthu ziti zimene mwaonapo zomwe zikusonyeza kuti zipembedzo zalephera kusonyeza chikondi cha Mulungu?

Zimene zipembedzo zonyenga zimachita sizisonyeza kuti Mulungu ndi wachikondi

6. Mulungu akufuna kuti anthu atuluke m’zipembedzo zonyenga

Werengani Chivumbulutso 18:4, a kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mumamva bwanji mukaganizira zoti Mulungu akufuna kuthandiza anthu amene akhala akunamizidwa ndi zipembedzo zonyenga?

7. Pitirizani kuphunzira zokhudza Mulungu woona

Zinthu zoipa zimene zipembedzo zonyenga zimachita, zisakuchititseni kuti musiye kukhulupirira Mulungu n’kuyamba kumuona kuti ndi woipa. Taganizirani za mwana amene sakufuna kumvera bambo ake ndipo akusankha kuchoka pakhomo n’kukayamba kuchita makhalidwe oipa ambiri. Bambowo sakugwirizana ndi zochita za mwana wawoyo. N’chifukwa chiyani kungakhale kulakwa kuimba mlandu bambowo chifukwa cha zochita za mwanayo?

  • Kodi zingakhale zomveka kuimba mlandu Yehova n’kusiya kuphunzira za iyeyo chifukwa cha zoipa zimene zipembedzo zonyenga zimachita?

ZIMENE ENA AMANENA: “Sindikufuna kuphunzira za Mulungu chifukwa zipembedzo zayambitsa mavuto ambirimbiri.”

  • Kodi inunso mumaona choncho?

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kukhulupirira Yehova chifukwa cha zochita za zipembedzo zonyenga?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Zipembedzo zonyenga zakhala zikunamiza anthu ponena za Mulungu mwa kuphunzitsa zinthu zabodza komanso kuchita zinthu zoipa kwambiri. Mulungu adzawononga zipembedzo zonse zonyenga.

Kubwereza

  • Kodi mumamva bwanji mukaganizira zimene zipembedzo zonyenga zakhala zikuphunzitsa ndi kuchita?

  • Kodi Yehova amamva bwanji ndi zimene zipembedzo zonyenga zimachita?

  • N’chiyani chimene Mulungu adzachite ndi zipembedzo zonyenga?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani njira ziwiri zosonyeza mmene zipembedzo zambiri zimachitira zinthu zosasangalatsa Mulungu.

“Kodi Zipembedzo Zonse N’zofanana Ndipo Zimathandizadi Anthu Kudziwa Mulungu?” (Nkhani yapawebusaiti)

N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizisonkhana limodzi ndi anzathu?

Kodi Pali Vuto Ngati Munthu Atakhala Kuti Sali M’chipembedzo Chilichonse? (Nkhani yapawebusaiti)

Wansembe ankakayikira zimene chipembedzo chake chimachita. Koma zimenezi sizinamuchititse kusiya kuphunzira choonadi chokhudza Mulungu.

“N’chifukwa Chiyani Wansembe Anasiya Chipembedzo Chake?” (Galamukani!, February 2015)

Kwa zaka zambiri, zipembedzo zakhala zikuphunzitsa mabodza omwe amachititsa anthu kuona ngati Mulungu satikonda, ndiponso ndi wankhanza. Dziwani zoona zake pa atatu mwa mabodza amenewa.

“Mabodza Amene Amalepheretsa Anthu Kukonda Mulungu” (Nsanja ya Olonda, November 1, 2013)

a Buku la Chivumbulutso limanena kuti mkazi yemwe amatchedwa Babulo Wamkulu amaimira zipembedzo zonyenga. Kuti mudziwe chifukwa chake, onani Mawu Akumapeto 1.