PHUNZIRO 15

Kodi Yesu Ndi Ndani?

Kodi Yesu Ndi Ndani?

Yesu ndi mmodzi mwa anthu otchuka kwambiri. Anthu ambiri amadziwa dzina lake, koma sadziwa zambiri zokhudza iyeyo ndipo amafotokoza zosiyanasiyana akafunsidwa kuti Yesu ndi ndani. Kodi Baibulo limati Yesu ndi ndani?

1. Kodi Yesu ndi ndani?

Yesu ndi mngelo wamphamvu ndipo amakhala kumwamba. Yehova Mulungu analenga Yesu asanalenge zinthu zina zonse. Choncho, iye amadziwika kuti “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Baibulo limanena kuti Yesu ndi “Mwana . . . wobadwa yekha” wa Mulungu chifukwa ndi yekhayo amene Yehova anamulenga mwachindunji. (Yohane 3:16) Yesu ankagwira ntchito limodzi ndi Atate wake Yehova, powathandiza kulenga zinthu zina zonse. (Werengani Miyambo 8:30.) Yesu akupitirizabe kugwira ntchito limodzi ndi Yehova mosangalala. Iye amatumikira mokhulupirika monga woyankhula m’malo mwa Mulungu. Ndipo amatchedwa “Mawu,” kutanthauza kuti amapereka mauthenga ndi malangizo ochokera kwa Mulungu.​—Yohane 1:14.

2. N’chifukwa chiyani Yesu anabwera padziko lapansi?

Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Yehova anachita chozizwitsa. Iye anagwiritsa ntchito mzimu woyera posamutsa moyo wa Yesu kumwamba n’kuuika m’mimba mwa namwali wina dzina lake Mariya. Mwa njira imeneyi, Yesu anabadwa monga munthu. (Werengani Luka 1:34, 35.) Yehova anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzakhale Mesiya wolonjezedwa kapena kuti Khristu ndiponso kuti adzapulumutse anthu. a Maulosi onse a m’Baibulo onena za Mesiya anakwaniritsidwa mwa iye. Choncho, anthu sanavutike kuzindikira Yesu monga “Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”​—Mateyu 16:16.

3. Kodi panopa Yesu ali kuti?

Yesu ataphedwa padzikoli, Mulungu anamuukitsa monga mngelo ndipo anabwerera kumwamba. Kumwambako, “Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba.” (Afilipi 2:9) Panopa Yesu ali ndi udindo wapamwamba kwambiri ndipo ndi wachiwiri kwa Yehova.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti mudziwe zoona zake zokhudza Yesu komanso chifukwa chake kuphunzira za iye n’kothandiza.

4. Yesu si Mulungu Wamphamvuyonse

Baibulo limaphunzitsa kuti ngakhale kuti Yesu ndi mngelo wamphamvu kumwamba, iye amamvera Yehova Mulungu yemwe ndi Atate wake. N’chifukwa chiyani tikutero? Onerani VIDIYO kuti mudziwe zimene Baibulo limanena zokhudza kusiyana komwe kulipo pakati pa Yesu ndi Mulungu wamphamvuyonse.

Malemba otsatirawa akuthandizani kumvetsa kusiyana komwe kulipo pakati pa Yehova ndi Yesu. Pambuyo powerenga lemba lililonse mukambirane mafunso omwe ali pansi pake.

Werengani Luka 1:30-32.

  • Kodi zimene mngelo ananena zimasonyeza bwanji kuti Yesu ndi wosiyana ndi Yehova Mulungu “Wam’mwambamwamba”?

Werengani Mateyu 3:16, 17.

  • Pa nthawi yomwe Yesu ankabatizidwa, kodi kumwamba kunamveka mawu oti chiyani?

  • Kodi mukuganiza kuti mawuwo anali a ndani?

Werengani Yohane 14:28.

  • Pakati pa bambo ndi mwana, ndi ndani amene amakhala wamkulu komanso wa udindo waukulu?

  • Kodi Yesu ankatanthauza chiyani ponena kuti Yehova ndi Atate wake?

Werengani Yohane 12:49.

  • Kodi Yesu ankaona kuti iye ndi Atate wake ndi ofanana? Inu mukuganiza bwanji?

5. Umboni wosonyeza kuti Yesu anali Mesiya

M’Baibulo muli maulosi ambiri onena za Mesiya yemwe Mulungu anamusankha kuti adzapulumutse anthu. Maulosiwa anathandiza anthu kuti amuzindikire mosavuta. Onerani VIDIYO kuti muone mwachidule ena mwa maulosi okhudza Yesu omwe anakwaniritsidwa pa nthawi imene anali padziko lapansi.

Werengani maulosi a m’Baibulo otsatirawa, kenako mukambirane mafunsowa:

Werengani Mika 5:2 kuti mudziwe kumene Mesiya anayenera kubadwira. b

  • Kodi kumene Yesu anabadwira kunagwirizana ndi zimene ulosiwu unanena?​—Mateyu 2:1.

Werengani Salimo 34:20 ndi Zekariya 12:10 kuti muone zimene Baibulo linaneneratu zokhudza kuphedwa kwa Mesiya.

  • Kodi maulosiwa anakwaniritsidwadi?​—Yohane 19:33-37.

  • N’chifukwa chiyani sizikanatheka kuti Yesu achititse kuti maulosiwa akwaniritsidwe?

  • Ndiye zimenezi zikukuthandizani kuzindikira zotani zokhudza Yesu?

6. Kuphunzira zokhudza Yesu kumatithandiza kwambiri

Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyenera kuphunzira zokhudza Yesu komanso udindo umene Mulungu anamupatsa. Werengani Yohane 14:6 ndi 17:3, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi kuphunzira zokhudza Yesu n’kofunika chifukwa chiyani?

Yesu anatsegula njira yotithandiza kuti Mulungu akhale mnzathu. Iye anaphunzitsa choonadi chonena za Yehova komanso kudzera mwa Yesuyo tikhoza kudzapeza moyo wosatha

ZIMENE ENA AMANENA: “A Mboni za Yehova sakhulupirira Yesu.”

  • Kodi inuyo mungayankhe bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yesu ndi mngelo wamphamvu. Iye ndi mwana wa Mulungu ndiponso Mesiya.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani Yesu amatchedwa kuti “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse”?

  • Kodi ankachita chiyani asanabwere padziko lapansi?

  • Kodi timadziwa bwanji kuti Yesu ndi Mesiya?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Fufuzani kuti muone chifukwa chake Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu ndi Atate a Yesu.

“N’chifukwa Chiyani Baibulo Limati Yesu Ndi Mwana wa Mulungu?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani chifukwa chake Utatu si chiphunzitso cha m’Baibulo.

“Kodi Yesu Ndi Mulungu?” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2009)

Werengani kuti mudziwe mmene mayi wina anasinthira moyo wake pambuyo pofufuza zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu.

“Mzimayi Wachiyuda Anafufuzanso Mozama Zimene Ankakhulupirira” (Galamukani!, May 2013)

a Muphunziro 26 ndi 27 tidzakambirana chifukwa chake anthufe tikufunikira kupulumutsidwa komanso mmene Yesu amatipulumutsira.

b Onani Mawu Akumapeto 2 kuti mudziwe zokhudza ulosi umene unaneneratu nthawi yeniyeni yomwe Yesu adzaonekere padziko lapansi.