PHUNZIRO 22
Zimene Mungachite Kuti Muziuzako Ena Uthenga Wabwino
Mukamaphunzira mfundo zinazake za m’Baibulo, mungayambe kumaganiza kuti, ‘Zimenezi n’zofunika kuti aliyense azidziwe.’ Ndipo n’zoonadi, anthu akufunika kudziwa mfundo za choonadi. Komabe mwina mungamachite mantha kuuzako ena zimene mwaphunzira. Tiyeni tikambirane zimene zingakuthandizeni kuti muthetse mantha n’kuyamba kuuzako ena uthenga wabwino wa m’Baibulo.
1. Mungatani kuti muziuzako anthu amene mukuwadziwa zinthu zomwe mwaphunzira?
Ophunzira a Yesu ananena kuti: “Ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Machitidwe 4:20) Uwu ndi umboni wakuti ankakonda kwambiri choonadi ndipo ankafuna kuuza aliyense zokhudza choonadicho. Kodi ndi mmene inunso mukumvera? Ngati ndi choncho, ganizirani mipata imene mungaigwiritse ntchito kuti muuzeko achibale ndi anzanu zimene mwaphunzira, koma mwaulemu.—Werengani Akolose 4:6.
Mmene mungayambire
-
Mukamacheza ndi wachibale mukhoza kumuuzako mfundo inayake ya m’Baibulo ndipo munganene kuti: “Mlungu uno ndaphunzira mfundo inayake yosangalatsa.”
-
Ngati muli ndi mnzanu winawake amene akudwala kapena ali ndi nkhawa, mungamuuzeko lemba lolimbikitsa.
-
Anzanu akuntchito akakufunsani mmene moyo wanu ukuyendera, mungawauzeko zimene mwaphunzira pa phunziro la Baibulo kapena pamisonkhano ya mpingo.
-
Aonetseni anzanu webusaiti ya jw.org.
-
Mungapemphe anzanu kuti akhale nawo pamene mukuphunzira Baibulo kapena mungawaonetse mmene angapemphere munthu woti aziphunzira nawo pa jw.org.
2. N’chifukwa chiyani muyenera kukhala ndi cholinga cholalikira limodzi ndi mpingo?
Kuwonjezera pa anthu amene ankawadziwa, ophunzira a Yesu ankalalikiranso uthenga wabwino kwa anthu ena. Kuti zimenezi zitheke, Yesu ‘anawatumiza awiriawiri kuti atsogole kupita mumzinda’ uliwonse kuti akalalikire. (Luka 10:1) Kugwira ntchito motsatira njira imeneyi kunathandiza kuti anthu ambiri amve uthenga wabwino. Kunathandizanso kuti ophunzira a Yesu asangalale kwambiri chifukwa cholalikira ndi anzawo. (Luka 10:17) Kodi inunso mungakhale ndi cholinga cholalikira limodzi ndi mpingo?
FUFUZANI MOZAMA
Ganizirani zimene mungachite kuti musamachite mantha komanso mmene mungasangalalire chifukwa chogwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino.
3. Yehova adzakuthandizani
Anthu ena amachita mantha akaganizira zofuna kuyamba kulalikira chifukwa choopa mmene anthu ena angawaonere komanso zimene angakumane nazo.
-
Kodi mumachita mantha kuuzako ena zimene mwaphunzira? N’chifukwa chiyani mukutero?
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
-
N’chiyani chinathandiza achinyamata a Mboniwa kuti asiye kuchita mantha?
Werengani Yesaya 41:10, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi pemphero lingakuthandizeni bwanji mukamaopa kulalikira?
Kodi mukudziwa?
Pali a Mboni za Yehova ambiri omwe ankaganiza kuti sangalimbe mtima kuuza ena uthenga wabwino. Mwachitsanzo, a Sergey ankadziona kuti ndi osafunika ndipo zinkawavuta kulankhulana ndi anthu. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo. A Sergey akuti: “Ngakhale kuti ndinkachita mantha ndinayamba kuuzako ena zomwe ndinkaphunzira. Koma ndinadabwa kwambiri kuona kuti kuuza ena zokhudza Baibulo, kunandithandiza kuti ndisiye kudziona ngati wosafunika. Zimenezi zinandithandizanso kuti chikhulupiriro changa chilimbe.”
4. Muzichita zinthu mwaulemu
Mukamalalikira uthenga wabwino musamangoganizira zimene mukufuna kunena, koma muziganiziranso mmene mungazinenere. Werengani 2 Timoteyo 2:24 ndi 1 Petulo 3:15, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
-
Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo za m’mavesiwa pokambirana ndi anthu zokhudza Baibulo?
-
Mwina achibale anu kapena anzanu angakutsutseni. Ndiye kodi muyenera kuchita chiyani? Nanga simukuyenera kuchita chiyani?
-
N’chifukwa chiyani muyenera kufunsa mafunso omwe angawathandize kunena maganizo awo, m’malo mongowauza zoyenera kukhulupirira?
5. Anthu amene amauzako ena uthenga wabwino amasangalala
Yehova anapatsa Yesu ntchito youzako ena uthenga wabwino. Nanga Yesu ankaiona bwanji ntchitoyi? Werengani Yohane 4:34, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Tikamadya chakudya chabwino timakhala ndi thanzi labwino ndiponso timasangalala. N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti kuchita chifuniro cha Mulungu, komwe kumaphatikizapo kuuza ena uthenga wabwino kuli ngati kudya chakudya?
-
Kodi kuuzako ena uthenga wabwino kungakuthandizeni bwanji kuti muzikhala osangalala?
Zimene zingakuthandizeni
-
Pa nthawi ya misonkhano yamkati mwa mlungu, mukachite chidwi ndi mmene mungayambire kukambirana ndi anthu.
-
Lankhulani ndi mphunzitsi wanu kuti akuuzeni zomwe muyenera kuchita kuti muzipatsidwa nawo mbali za ophunzira pamisonkhano yamkati mwa mlungu. Mbali zimenezi, zingakuthandizeni kuti musavutike kuyamba kuuza ena zimene mukuphunzira.
-
M’bukuli muli chigawo chakuti, “Zimene Ena Amanena” komanso chakuti, “Munthu Wina Angakufunseni Kuti.” Yesani kugwiritsa ntchito zigawozi poyeserera kuyankha mafunso amene anthu amakonda kufunsa komanso zimene amakonda kunena ngati sakufuna kukambirana nawo mfundo za m’Baibulo.
MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Zikukuyenderani bwanji anzathu?”
-
Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mpata umenewu pomuuza mfundo zimene mwapeza pophunzira Baibulo?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Tikamauza ena uthenga wabwino timakhala osangalala ndipo musamaganize kuti kuyamba kukambirana ndi anthu n’kovuta.
Kubwereza
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kuuzako ena uthenga wabwino?
-
Kodi mungachite bwanji zinthu mwaulemu mukamauza ena uthenga wabwino?
-
Kodi mungatani kuti muthetse mantha mukaganizira zofuna kuyamba kulalikira?
ONANI ZINANSO
Onani njira 4 zomwe mungagwiritse ntchito polalikira ndi khadi lodziwitsa anthu za jw.org.
Chitsanzo cha Ulaliki wa Khadi Lodziwitsa Anthu za JW.ORG (1:43)
Onani makhalidwe 4 omwe angakuthandizeni kuti muzilalikira uthenga wabwino.
“Kodi Ndinu Okonzeka Kukhala Msodzi wa Anthu?” (Nsanja ya Olonda, September 2020)
Onerani vidiyo yosonyeza chitsanzo cha m’Baibulo chomwe chingathandize munthu kulalikira molimba mtima ngakhale atakhala wamng’ono.
MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE—KUPHUNZIRA BAIBULO MOKAMBIRANA