PHUNZIRO 23

Ubatizo Ungakuthandizeni Kukhala Ndi Tsogolo Labwino

Ubatizo Ungakuthandizeni Kukhala Ndi Tsogolo Labwino

Yesu anaphunzitsa kuti Akhristu ayenera kubatizidwa. (Werengani Mateyu 28:19, 20.) Koma kodi ubatizo n’chiyani? Nanga munthu ayenera kuchita chiyani kuti abatizidwe?

1. Kodi ubatizo n’chiyani?

Mawu akuti “batiza” amachokera ku mawu a Chigiriki amene amatanthauza kuviika m’madzi. Pamene Yesu ankabatizidwa, thupi lake lonse linamizidwa mumtsinje wa Yorodano ndipo kenako ‘anavuuka m’madzimo.’ (Maliko 1:9, 10) Mofanana ndi Yesu, masiku ano Akhristu akamabatizidwa, thupi lawo lonse limaviikidwa kapena kumizidwa m’madzi.

2. Kodi ubatizo ndi chizindikiro cha chiyani?

Munthu akabatizidwa, amasonyeza kuti anadzipereka kwa Yehova Mulungu. Koma kodi munthu amadzipereka bwanji? Asanabatizidwe, amapemphera kwa Yehova payekha n’kumuuza kuti akufuna kumutumikira kwa moyo wake wonse. Amalonjeza Yehova kuti azilambira Iye yekha, komanso kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wake ndi kuchita zimene Yehova amafuna. Iye amasankha ‘kudzikana yekha ndi . . . kutsatira zimene Yesu anaphunzitsa ndi kuchita mosalekeza.’ (Mateyu 16:24) Kudzipereka komanso kubatizidwa kumamuthandiza kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova komanso Akhristu anzake.

3. Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti abatizidwe?

Musanabatizidwe, muyenera kuphunzira zokhudza Yehova komanso kuyamba kumukhulupirira kwambiri. (Werengani Aheberi 11:6.) Mukapitiriza kuphunzira zambiri zokhudza Yehova komanso kumukhulupirira, m’pamenenso mudzayambe kumukonda kwambiri. Kenako mudzayamba kufuna kulalikira zokhudza Yehova komanso kuchita zimene Iye amafuna pa moyo wanu. (2 Timoteyo 4:2; 1 Yohane 5:3) Munthu akangoyamba ‘kuyenda mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti azimukondweretsa pa chilichonse,’ amasankha kupereka moyo wake kwa Mulungu kenako amabatizidwa.​—Akolose 1:9, 10. a

FUFUZANI MOZAMA

Onani zomwe tingaphunzire pa ubatizo wa Yesu komanso zomwe munthu angachite pokonzekera ubatizo.

4. Zimene tikuphunzira pa ubatizo wa Yesu

Werengani Mateyu 3:​13-17 kuti mudziwe zomwe zinachitika pa ubatizo wa Yesu. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi Yesu anabatizidwa ali wakhanda?

  • Kodi pamene ankamubatiza, anachita kungomuwaza madzi?

Yesu atangobatizidwa, anayamba kugwira ntchito yapadera yomwe Mulungu anamutuma padzikoli. Werengani Luka 3:21-23 ndi Yohane 6:38, kenako mukambirane funso ili:

  • Yesu atabatizidwa, kodi ndi ntchito iti yomwe ankaiona kuti ndi yofunika kwambiri pa moyo wake?

5. N’zotheka kukwaniritsa cholinga chanu choti mubatizidwe

Poyamba mukhoza kuchita mantha mukaganizira za kudzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa. Komabe, mukapitiriza kuphunzira zambiri zokhudza Yehova, n’kufika pomudziwa bwino, mantha akhoza kutheratu ndipo mungakwanitse cholinga chofunika kwambiri chimenechi. Kuti muone anthu ena amene anakwanitsa kuchita zimenezi, onerani VIDIYO.

Werengani Yohane 17:3 ndi Yakobo 1:5, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi munthu angatani kuti akonzekere kubatizidwa?

  1. Timadzipereka kwa Yehova pomuuza m’pemphero kuti tikufuna kumutumikira kwa moyo wathu wonse

  2. Pa tsiku la ubatizo timasonyeza anthu kuti tinadzipereka kwa Mulungu

6. Tikabatizidwa timakhala m’banja la Yehova

Tikabatizidwa, timakhala m’banja logwirizana lapadziko lonse. Ngakhale kuti timasiyana kochokera ndi zikhalidwe timakhulupirira zinthu zofanana ndiponso timayendera mfundo zamakhalidwe abwino zofanana pa moyo wathu. Werengani Salimo 25:14 ndi 1 Petulo 2:​17, kenako mukambirane funso ili:

  • Mogwirizana ndi mavesiwa, kodi ubatizo umathandiza bwanji munthu?

ZIMENE ENA AMANENA: “Ndidzabatizidwabe m’tsogolomu chifukwa ndikuopa kuchotsedwa ndikalakwitsa.”

  • Ngati inunso mukuganiza choncho, kodi mukuona kuti mukufunika kuyesetsabe kuti mubatizidwe?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yesu anaphunzitsa kuti Akhristu ayenera kubatizidwa. Munthu amene akufuna kubatizidwa, ayenera kukhulupilira kwambiri Yehova, kuyendera mfundo za Yehova pa moyo wake ndiponso kudzipereka kwa Yehova.

Kubwereza

  • Kodi ubatizo n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani anthu amayenera kubatizidwa?

  • Kodi kudzipereka ndi kubatizidwa n’zogwirizana bwanji?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene munthu ayenera kuchita asanafike podzipereka komanso kubatizidwa?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene ubatizo umatanthauza.

“Kodi Ubatizo N’chiyani?” (Nkhani yapawebusaiti)

Werengani nkhaniyi kuti muone mmene munthu wina anasankhira kubatizidwa chifukwa chomvetsa bwino mfundo za m’Baibulo.

“Ankafuna Kuti Ndione Ndekha Kuti Zoona Ndi Ziti” (Nsanja ya Olonda, February 1, 2013)

a Munthu ayenera kubatizidwanso ngakhale kuti anabatizidwa kale ku chipembedzo china. Tikutero chifukwa chipembedzocho sichinamuthandize kudziwa choonadi cha m’Baibulo.​—Onani Machitidwe 19:1-5 ndi Phunziro 13.