PHUNZIRO 24

Kodi Angelo Ndi Ndani, Nanga Amachita Chiyani?

Kodi Angelo Ndi Ndani, Nanga Amachita Chiyani?

Yehova amafuna kuti tidziwe zokhudza banja lake lakumwamba. M’banja limeneli mulinso angelo, omwe amatchedwa “ana . . . a Mulungu.” (Yobu 38:7) Kodi Baibulo limanena zotani zokhudza angelo? Kodi angelo amachita zotani? Kodi angelo onse ali m’banja la Mulungu?

1. Kodi angelo ndi ndani?

Asanalenge dziko lapansi, Yehova analenga angelo. Mofanana ndi Mulungu, angelo samaoneka ndipo amakhala kumwamba. (Aheberi 1:14) Angelo alipo mamiliyoni ambirimbiri ndipo mngelo wina aliyense ndi wosiyana ndi mnzake. (Chivumbulutso 5:11) Iwo ‘amachita zimene Yehova wanena, mwa kumvera mawu ake.’ (Salimo 103:20) Kale Yehova ankatumiza angelo padziko lapansi kuti adzapereke mauthenga ndi kuthandiza komanso kupulumutsa anthu ake. Masiku ano angelo amatsogolera Akhristu kuti akalalikire kwa anthu amene akufuna kudziwa za Mulungu.

2. Kodi Satana ndi ziwanda zake ndi ndani?

Angelo ena anasankha kusiya kumvera Yehova. Mngelo amene anayambirira kuchita zimenezi ndi amene amatchedwa kuti “Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Satana ankafuna kuti azilamulira ena, choncho anapusitsa Adamu ndi Hava ndipo kenako anadzapusitsanso angelo ena kuti asiye kumvera Mulungu. Angelo amene anasankha kupandukira Mulunguwa amatchedwa ziwanda. Popeza kuti angelowa anali kumwamba, Yehova anawathamangitsira padziko lapansi ndipo akuyembekezera kuwonongedwa posachedwapa.​​​—Werengani Chivumbulutso 12:​9, 12.

3. Kodi Satana ndi ziwanda zake amapusitsa bwanji anthu?

Satana ndi ziwanda zake amapusitsa anthu ambiri kuti azichita zamizimu. Kuchita zimenezi n’koopsa kwambiri chifukwa amawachititsa kukhulupirira kuti angalankhulane ndi anthu amene anamwalira. Mwachitsanzo, anthu ena akakhala ndi vuto amapita kukakumana ndi okhulupirira nyenyezi, olosera zam’tsogolo kapenanso asing’anga. Anthu ena akadwala amakafunafuna mankhwala kwa anthu ochita zamizimu. Satana ndi ziwanda zake amapangitsanso anthu kukhulupirira kuti akhoza kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. Koma Yehova amatichenjeza kuti: “Musatembenukire kwa olankhula ndi mizimu ndipo musafunsire olosera zam’tsogolo.” (Levitiko 19:31) Iye amatiuza zimenezi chifukwa amafuna kutiteteza kwa Satana ndi ziwanda zake, omwe ndi adani a Mulungu ndipo amafuna kutipweteka.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti muone zinthu zabwino zimene angelo amachita, kuopsa kwa kukhulupirira mizimu komanso zimene tingachite kuti tidziteteze kwa Satana ndi ziwanda zake.

4. Angelo amathandiza anthu kuphunzira zokhudza Yehova

Angelo a Mulungu salalikira mwachindunji kwa anthu. M’malomwake amatsogolera atumiki a Mulungu kwa anthu amene akufuna kuphunzira. Werengani Chivumbulutso 14:6, 7, kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani timafunikira kuthandizidwa ndi angelo tikamalalikira?

  • Kodi mukumva bwanji mukaganizira kuti angelo angakutsogolereni kwa anthu amene akufuna kuphunzira Baibulo? N’chifukwa chiyani mukutero?

5. Muzipewa zamizimu

Satana ndi ziwanda ndi adani a Yehova komanso a anthufe. Werengani Luka 9:38-42, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi ziwanda zimawachitira zotani anthu?

Sitifuna kumachita zinthu zomwe zingapangitse kuti ziwanda zizitivutitsa. Werengani Deuteronomo 18:10-12, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi ziwanda zimafuna kumalankhula nafe komanso kutipusitsa pogwiritsa ntchito njira ziti? Kodi ndi zinthu ziti zomwe zimakonda kuchitika komwe mumakhala?

  • Kodi mukuona kuti ndi zomveka Yehova akamatiletsa kuchita zamizimu? N’chifukwa chiyani mukutero?

Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi mukuganiza kuti khoza limene Palesa anamveka mwana wake linali loopsa? N’chifukwa chiyani mukutero?

  • Kodi Palesa anafunika kuchita chiyani kuti asamavutitsidwe ndi ziwanda?

Akhristu enieni salola kuti ziwanda ziziwavutitsa. Werengani Machitidwe 19:19 ndi 1 Akorinto 10:21, kenako mukambirane funso ili:

  • Ngati muli ndi zinthu zokhudzana ndi zamizimu, n’chifukwa chiyani muyenera kuziwotcha kapena kuzitaya?

6. N’zotheka kugonjetsa Satana ndi ziwanda zake

Satana ndi amene amalamulira ziwanda. Koma angelo okhulupirika amatsogoleredwa ndi Mikayeli, mkulu wa angelo. Mikayeli ndi dzina lina la Yesu. Kodi Mikayeli ali ndi mphamvu zochuluka bwanji? Werengani Chivumbulutso 12:7-9, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi wamphamvu kwambiri ndi ndani, pakati pa Mikayeli ndi angelo ake komanso Satana ndi ziwanda zake?

  • Kodi mukuganiza kuti otsatira a Yesu ayenera kumaopa Satana ndi ziwanda zake?

Mungathe kugonjetsa Satana ndi ziwanda zake. Werengani Yakobo 4:7, kenako mukambirane funso ili:

  • Mungatani kuti musamavutitsidwe ndi Satana ndi ziwanda zake?

ZIMENE ENA AMANENA: “Palibe vuto lina lililonse kumasewera magemu ndi kuwonera mafilimu okhudzana ndi zamizimu. Ndi zosangalatsa basi.”

  • Kodi maganizo amenewa ndi oopsa chifukwa chiyani?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Angelo okhulupirika amatithandiza. Satana ndi ziwanda zake ndi adani a Yehova ndipo amagwiritsa ntchito zamizimu pofuna kusocheretsa anthu.

Kubwereza

  • Kodi angelo okhulupirika amathandiza bwanji anthu kuphunzira zokhudza Yehova?

  • Kodi Satana ndi ziwanda zake ndi ndani?

  • N’chifukwa chiyani inuyo simukufuna kuchita chilichonse chokhudzana ndi zamizimu?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani umboni wosonyeza kuti Yesu ndi Mikayeli mkulu wa angelo.

“Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani umboni wotsimikizira kuti Mdyerekezi ndi weniweni.

“Kodi Mdyerekezi Alipodi?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani zimene zinathandiza mayi wina kusiya kukhulupirira zamizimu.

“Anapeza Chifuno cha Moyo” (Nsanja ya Olonda, July 1, 1993)