PHUNZIRO 27

Kodi Imfa ya Yesu Ingatipulumutse Bwanji?

Kodi Imfa ya Yesu Ingatipulumutse Bwanji?

Anthufe timachimwa, kuvutika komanso kufa chifukwa chakuti Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu. a Komabe Yehova anakonza njira yotipulumutsira ku uchimo ndi imfa. Iye anachita zimenezi potumiza Mwana wake Yesu Khristu. Baibulo limaphunzitsa kuti imfa ya Yesu inali ngati dipo lotiwombola. Dipo ndi malipiro amene amaperekedwa kuti munthu amasulidwe. Choncho, mtengo umene Yesu anapereka unali moyo wake wangwiro. (Werengani Mateyu 20:28.) Popeza kuti Yesu anali wangwiro anali ndi ufulu wokhala ndi moyo wosatha padzikoli. Komabe, iye analolera kupereka moyo wake, zomwe zinathandiza kuti anthufe tidzapezenso zonse zimene Adamu ndi Hava anataya. Yesu anasonyezanso mmene Yehova komanso iyeyo amatikondera. Phunziroli likuthandizani kuti muziyamikira kwambiri zimene Yesu anachita potifera.

1. Kodi imfa ya Yesu ingatithandize bwanji masiku ano?

Popeza kuti ndife ochimwa, timachita zinthu zambiri zimene zimakhumudwitsa Yehova. Komabe ngati tikumva chisoni ndi machimo amene tachita, n’kumupempha Yehova kudzera mwa Yesu Khristu kuti atikhululukire komanso tikamayesetsa kuti tisabwereze machimowo, tikhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (1 Yohane 2:1) Baibulo limati: “Khristu anafera machimo kamodzi kokha basi. Munthu wolungamayo anafera anthu osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu.”​—1 Petulo 3:18.

2. Kodi imfa ya Yesu idzatithandiza bwanji m’tsogolo?

Yehova anatumiza Yesu kuti adzapereke moyo wake wangwiro “kuti aliyense wokhulupirira [Yesu] asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Chifukwa cha zimene Yesu anachitazi, posachedwapa Yehova adzachotsa zoipa zonse zimene zinayamba chifukwa cha kusamvera kwa Adamu. Izi zikutanthauza kuti tikamakhulupirira nsembe ya Yesu, tidzasangalala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.​—Yesaya 65:21-23.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza chifukwa chimene Yesu anaperekera moyo wake komanso mmene imfa yakeyi ingakuthandizireni.

3. Imfa ya Yesu inatimasula ku uchimo ndi imfa

  • Kodi Adamu anataya mwayi wotani chifukwa chosamvera Mulungu?

Werengani Aroma 5:12, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi inuyo mukukumana ndi zotani chifukwa choti Adamu anachimwa?

Werengani Yohane 3:​16, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani Yehova anatumiza Mwana wake padzikoli?

  1. Adamu anali munthu wangwiro yemwe sanamvere Mulungu. Chifukwa chakuti anachimwa, anthu onse amachimwa komanso kumwalira

  2. Yesu anali munthu wangwiro yemwe anamvera Mulungu. Chifukwa cha zimene anachita anthu onse adzakhala angwiro ndiponso sazidzafa

4. Imfa ya Yesu ingathandize anthu onse

Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi imfa ya munthu mmodzi ingathandize bwanji anthu onse?

Werengani 1 Timoteyo 2:5, 6, kenako mukambirane funso ili:

  • Adamu anali munthu wangwiro koma chifukwa chakuti anachimwa, anthu onse amachimwa komanso kumwalira. Yesu nayenso anali munthu wangwiro. Ndiye kodi zinatheka bwanji kuti apereke “dipo lokwanira ndendende”?

5. Dipo ndi mphatso imene Yehova anakupatsani

Aliyense amene ali pa ubwenzi ndi Yehova amaona kuti dipo ndi mphatso imene Mulungu anakonzera iyeyo. Mwachitsanzo, werengani Agalatiya 2:20 kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti dipo inali mphatso imene Mulungu anakonzera iyeyo?

Adamu atachimwa, iyeyo ndi ana ake onse anali oyenerera kufa. Koma Yehova anatumiza Mwana wake kuti adzatifere n’cholinga choti inuyo mudzakhale ndi moyo mpaka kalekale.

Mukamawerenga mavesi otsatirawa, ganizirani mmene Yehova anamvera pamene ankaona Mwana wake akuvutika. Werengani Yohane 19:1-7, 16-18, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mukumva bwanji mukaganizira zimene Yehova ndi Yesu anakuchitirani?

MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi zingatheke bwanji kuti munthu mmodzi afere anthu onse?”

  • Kodi mungayankhe bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Chifukwa chakuti Yesu anatifera, Yehova amatikhululukira machimo athu komanso tili ndi mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani Yesu anafa?

  • Kodi moyo wa Yesu wangwiro unakhala bwanji dipo lokwanira ndendende?

  • Kodi imfa ya Yesu imakuthandizani bwanji?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani chifukwa chake timanena kuti moyo wangwiro wa Yesu ndi dipo lotiwombola.

“Kodi Nsembe ya Yesu Imawombola Bwanji ‘Anthu Ambiri’?” (Nkhani yapawebusaiti)

Dziwani zimene mungachite kuti mupulumutsidwe ku uchimo ndi imfa.

“Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani mmene kuphunzira zokhudza nsembe ya Khristu kunathandizira munthu wina yemwe anakhudzidwa kwambiri ndi zinthu zoipa zimene anaona.

“Chikondi Changa cha Poyamba Chandithandiza Kupirira” (Nsanja ya Olonda, May 15, 2015)

a Tchimo silimangotanthauza kuchita chinthu chinachake cholakwika. Koma limatanthauzanso kuti tinatalikirana ndi Mulungu chifukwa chakuti ndife ana a Adamu.