PHUNZIRO 28

Muziyamikira Zimene Yehova Ndi Yesu Anakuchitirani

Muziyamikira Zimene Yehova Ndi Yesu Anakuchitirani

Kodi mumamva bwanji mnzanu akakupatsani mphatso yokongola kwambiri? N’zosachita kufunsa kuti mumasangalala kwambiri komanso mumayamikira mnzanuyo chifukwa chokupatsani mphatso. Yehova ndi Yesu anatipatsa mphatso yamtengo wapatali kuposa ina iliyonse. Kodi mphatso imeneyi n’chiyani nanga tingasonyeze bwanji kuti timayamikira?

1. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene Mulungu ndi Khristu anatichitira?

Baibulo limalonjeza kuti “aliyense wokhulupirira [Yesu]” angakhale ndi moyo mpaka kalekale. (Yohane 3:16) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingasonyeze kuti timakhulupirira Yesu mwa zosankha ndi zochita zathu. (Yakobo 2:17) Kuchita zimenezi kumatithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yesu komanso Atate wake Yehova.​—Werengani Yohane 14:21.

2. Kodi ndi mwambo wapadera uti umene umatithandiza kuyamikira zimene Yehova ndi Yesu anatichitira?

Pa usiku wake womaliza, Yesu anauza otsatira ake zokhudza njira ina imene tingasonyezere kuti timayamikira nsembe imene anapereka. Iye anayambitsa mwambo wapadera umene m’Baibulo umatchedwa kuti “Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.” Mwambowu umatchedwanso kuti Chikumbutso cha imfa ya Khristu. (1 Akorinto 11:20) Poyambitsa mwambowu, Yesu ankafuna kuti atumwi ake ndi Akhristu oona onse azikumbukira kuti iye anatifera. Choncho anatilamula kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Luka 22:19) Tikamapezeka pa Chikumbutso timasonyeza kuti timayamikira chikondi chachikulu chimene Yehova ndi Yesu anatisonyeza.

FUFUZANI MOZAMA

Onani njira zina zimene mungasonyezere kuti mumayamikira chikondi chachikulu chimene Yehova ndi Yesu anatisonyeza. Onaninso chifukwa chake kupezeka pamwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Khristu, n’kofunika kwambiri.

3. Zimene tingachite posonyeza kuyamikira

Tiyerekeze kuti munthu wina anakupulumutsani pamene munkamira m’madzi. Kodi mungangozinyalanyaza n’kuiwala zimene munthuyo anakuchitirani? Kapena mungayesetse kuchita zinthu zosonyeza kumuyamikira?

Tidzapeza moyo wosatha chifukwa chakuti Yehova anatikomera mtima. Werengani 1 Yohane 4:8-10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani tikunena kuti nsembe ya Yesu ndi mphatso yapadera?

  • Kodi inuyo mukumva bwanji mukaganizira zimene Yehova ndi Yesu anakuchitirani?

Tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene Yehova ndi Yesu anatichitira? Werengani 2 Akorinto 5:15 ndi 1 Yohane 4:11; 5:3. Pambuyo powerenga lemba lililonse mukambirane funso ili:

  • Malinga ndi lembali, kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira?

4. Muzitsanzira Yesu

Tingasonyezenso kuyamikira tikamatsanzira Yesu. Werengani 1 Petulo 2:21, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumatsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri?

5. Muzichita nawo Chikumbutso cha imfa ya Khristu

Kuti mudziwe zimene zinachitika pamwambo woyamba wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, werengani Luka 22:14, 19 ndi 20. Kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chiyani chimene chinachitika pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye?

  • Kodi mkate ndi vinyo zimaimira chiyani?​—Onani vesi 19 ndi 20.

Cholinga cha Yesu poyambitsa mwambo wa Chikumbutso chinali chakuti ophunzira ake aziuchita kamodzi pachaka pa tsiku limene iye anafa. N’chifukwa chake chaka chilichonse a Mboni za Yehova amachita mwambo wokumbukira imfa ya Khristu mogwirizana ndi mmene iye analamulira. Kuti mudziwe zambiri zokhudza mwambo wofunika kwambiriwu, onerani VIDIYO. Kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi pamwambo wa Chikumbutso pamachitika zotani?

Mkate womwe umagwiritsidwa ntchito pa Chikumbutso umaimira thupi langwiro la Yesu limene anapereka m’malo mwa anthu. Ndipo vinyo amaimira magazi ake

ZIMENE ENA AMANENA: “Ndinalandira kale Yesu kukhala Mbuye ndi Mpulumutsi wanga ndiye sindikufunikiranso kuchita zinthu zina.”

  • Kodi mungagwiritsire ntchito bwanji lemba la Yohane 3:16 ndi Yakobo 2:17 pofuna kumuthandiza kuzindikira kuti pali zambiri zimene munthu angachite kuti adzapulumuke?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Tikamakhulupirira Yesu ndi kupezeka pamwambo wa Chikumbutso cha imfa yake, timasonyeza kuti timayamikira zimene iye anatichitira.

Kubwereza

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Yesu?

  • Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira zimene Yehova ndi Yesu anakuchitirani?

  • N’chifukwa chiyani mufunika kumachita nawo mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Khristu?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Kodi imfa ya Khristu imatilimbikitsa kuchita chiyani?

Anagwiritsa Ntchito Thupi Lake Polemekeza Yehova (9:28)

Dziwani zambiri zokhudza chikhulupiriro komanso mmene tingachisonyezere.

“Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Malonjezo a Yehova” (Nsanja ya Olonda, October 2016)

Onani chifukwa chake anthu ochepa okha ndi amene amadya mkate ndi kumwa vinyo pamwambo wa Chikumbutso.

“N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Mumachita Mwambo wa Mgonero wa Ambuye Mosiyana ndi Zipembedzo Zina?” (Nkhani yapawebusaiti)