PHUNZIRO 31
Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Uthenga wofunika kwambiri m’Baibulo ndi wokhudza Ufumu wa Mulungu. Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu umenewu pokwaniritsa cholinga chimene anali nacho chokhudza dziko lapansili. Ndiye kodi Ufumu wa Mulungu ndi chiyani? Timadziwa bwanji kuti Ufumuwu ukulamulira panopa? Ndi zinthu ziti zimene Ufumuwu wachita kale? Nanga udzachita zotani kutsogoloku? Mafunsowa ayankhidwa m’phunziroli komanso maphunziro awiri otsatira.
1. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, nanga Mfumu yake ndi ndani?
Ufumu wa Mulungu ndi boma limene linakhazikitsidwa ndi Yehova Mulungu. Mfumu yake ndi Yesu Khristu ndipo akulamulira kuchokera kumwamba. (Mateyu 4:17; Yohane 18:36) Ponena za Yesu, Baibulo limati: “Iye adzalamulira monga Mfumu . . . kwamuyaya.” (Luka 1:32, 33) Monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzalamulira anthu onse padzikoli.
2. Kodi ndi ndani akulamulira ndi Yesu?
Yesu sakulamulira yekha. Anthu ochokera “mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse . . . adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.” (Chivumbulutso 5:9, 10) Ndi anthu angati amene adzalamulire ndi Khristu? Kungoyambira pamene Yesu anabwera padziko lapansi, anthu ambiri akhala otsatira ake ndipo panopa alipo mamiliyoni ambiri. Koma ndi anthu okwana 144,000 okha amene adzapite kumwamba kukalamulira ndi Yesu. (Werengani Chivumbulutso 14:1-4.) Koma Akhristu ena onse adzakhala padziko lapansi ndipo azidzalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu.—Salimo 37:29.
3. Kodi Ufumu wa Mulungu umaposa bwanji maboma a anthu?
Ngakhale olamulira a dzikoli atayesetsa bwanji kuchita zinthu zabwino, iwo sangakwanitse kuchita zonse zimene akufuna. Pakapita nthawi amalowedwa m’malo ndi olamulira ena odzikonda kwambiri omwe safuna kuthandiza anthu. Mosiyana ndi olamulira amenewa, Yesu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu sadzalowedwa m’malo ndi wina aliyense. Mulungu wakhazikitsa “ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.” (Danieli 2:44) Yesu adzalamulira dziko lonse lapansi ndipo sazidzakondera mtundu winawake wa anthu. Yesu ndi wachikondi, wachifundo komanso wachilungamo ndipo adzaphunzitsa anthu kuti azidzasonyezana makhalidwe amenewa.—Werengani Yesaya 11:9.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake Ufumu wa Mulungu uli wabwino kwambiri kuposa maboma a anthu.
4. Ufumu wa Mulungu udzalamulira dziko lonse lapansi
Yesu Khristu ali ndi mphamvu zolamulira dzikoli kuposa anthu onse amene akulamulira dzikoli. Werengani Mateyu 28:18, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi ulamuliro wa Yesu umaposa bwanji ulamuliro wa anthu?
Maboma a anthu amasinthasintha ndipo dziko lililonse limakhala ndi wolamulira wake. Nanga bwanji Ufumu wa Mulungu? Werengani Danieli 7:14, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Popeza Ufumu wa Mulungu “sudzawonongedwa,” kodi zimenezi zili ndi ubwino wotani?
-
Kodi mukuganiza kuti tidzapindula bwanji Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira dziko lonse?
5. Maboma a anthu ayenera kuchotsedwa
N’chifukwa chiyani Ufumu wa Mulungu uyenera kulowa m’malo mwa maboma a anthu? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi zotsatira za ulamuliro wa anthu ndi zotani?
Werengani Mlaliki 8:9, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi mukuona kuti n’zoyenera kuti Ufumu wa Mulungu udzalowe m’malo mwa maboma a anthu? N’chifukwa chiyani mukutero?
6. Ufumu wa Mulungu uli ndi olamulira amene amatimvetsa
Popeza Yesu, yemwe ndi Mfumu yathu anakhalapo munthu, iye ‘amatimvera chisoni pa zofooka zathu.’ (Aheberi 4:15) Yehova anasankha amuna ndi akazi okwana 144,000 omwe adzalamulire ndi Yesu kuchokera “mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse.”—Chivumbulutso 5:9.
-
Popeza kuti Yesu komanso onse amene adzalamulire naye anakhalapo anthu, kodi mukuona kuti zimenezi n’zolimbikitsa? N’chifukwa chiyani mukutero?
7. Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo abwino kwambiri
Maboma a anthu amapanga malamulo omwe amayenera kuthandiza ndi kuteteza nzika zawo. Nawonso Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo amene nzika zake zimayenera kuwatsatira. Werengani 1 Akorinto 6:9-11, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzakhala bwanji padzikoli aliyense akamadzatsatira malamulo a Mulungu? a
-
Yehova amayembekezera kuti nzika za Ufumu wake zizitsatira malamulo ake, kodi mukuganiza kuti zimene Yehova amafunazi n’zoyenera? N’chifukwa chiyani mukutero?
-
Ndi mfundo iti imene ikusonyeza kuti anthu amene satsatira malamulo amenewa atha kusintha?—Onani vesi 11.
MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?”
-
Kodi mungamuyankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Ufumu wa Mulungu ndi boma lomwe lili kumwamba ndipo udzalamulira dziko lonse lapansi.
Kubwereza
-
Kodi ndi ndani amene adzalamulire mu Ufumu wa Mulungu?
-
Kodi Ufumu wa Mulungu umaposa bwanji maboma a anthu?
-
Kodi Yehova amayembekezera kuti nzika za Ufumu wake zizichita chiyani?
ONANI ZINANSO
Onani zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza komwe Ufumu wa Mulungu uli.
“Kodi Ufumu wa Mulungu Uli Mumtima Mwanu?” (Nkhani yapawebusaiti)
N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amaona kuti kukhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kukhala okhulupirika ku maulamuliro a anthu?
Onani zomwe Baibulo limafotokoza zokhudza anthu 144,000 omwe Yehova amawasankha kuti adzalamulire ndi Yesu.
“Kodi Ndi Ndani Amene Amapita Kumwamba?” (Nkhani yapawebusaiti)
MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE—KUPHUNZIRA BAIBULO MOKAMBIRANA