PHUNZIRO 33

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

Ufumu wa Mulungu unayamba kale kulamulira. Posachedwapa Ufumuwu ubweretsa madalitso ambiri padzikoli. Tiyeni tione ena mwa madalitso amene tidzasangalale nawo Ufumuwu ukadzayamba kulamulira dziko lonse lapansi.

1. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani kuti ubweretse mtendere ndi chilungamo padzikoli?

Yesu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzawononga anthu oipa ndi maboma onse a anthu pa nkhondo ya Aramagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Pa nthawi imeneyo, tidzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la m’Baibulo ili: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso.” (Salimo 37:10) Yesu adzagwiritsa ntchito Ufumuwu pobweretsa mtendere komanso chilungamo padziko lonse lapansi.​—Werengani Yesaya 11:4.

2. Kodi moyo udzakhala wotani chifuniro cha Mulungu chikadzachitika padziko lapansi?

Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira dzikoli, “olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kuona kuti aliyense padzikoli ndi wolungama ndipo akukonda Yehova ndi anthu ena. Palibe aliyense amene azidzadwala ndipo anthu onse adzakhala ndi moyo mpaka kalekale.

3. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani anthu oipa akadzawonongedwa?

Anthu oipa akadzawonongedwa, Yesu adzalamulira monga Mfumu kwa zaka 1,000. Pa nthawiyi, Yesu ndi olamulira anzake okwana 144,000, adzathandiza anthu onse padzikoli kuti akhale angwiro. Pofika kumapeto kwa zaka 1,000, dziko lonse lidzakhala paradaiso ndipo anthu azidzakhala mosangalala chifukwa chomvera malamulo a Yehova. Kenako Yesu adzabwezera Ufumu kwa Atate wake Yehova. Pa nthawi imeneyo, dzina la Yehova ‘lidzayeretsedwa’ kusiyana ndi kale lonse. (Mateyu 6:9, 10) Aliyense adzadziwa kuti Yehova ndi wolamulira wabwino kwambiri yemwe amaganizira atumiki ake. Kenako Yehova adzawononga Satana, ziwanda ndi anthu onse amene adzasonyeze kuti sakufuna kumvera ulamuliro wake. (Chivumbulutso 20:7-10) Zimenezi zikadzachitika, madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse padzikoli adzakhalapo mpaka kalekale.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake sitikayikira kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pokwaniritsa malonjezo onse amene ali m’Baibulo.

4. Mulungu adzathetsa maboma onse a anthu

Baibulo limati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pothetsa zinthu zonse zopanda chilungamo zimene anthu amachitira anzawo.

Werengani Danieli 2:44 ndi 2 Atesalonika 1:6-8, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi Yehova komanso mwana wake Yesu, adzachita chiyani ndi maboma a anthu komanso anthu amene amawatsatira?

  • Kodi zimene mwaphunzira zokhudza Yehova ndi Yesu zikukutsimikizirani bwanji kuti azidzachita zinthu mwachilungamo?

5. Yesu ndi Mfumu yabwino kwambiri

Monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzachitira anthu zinthu zabwino kwambiri padzikoli. Onerani VIDIYO kuti muone umboni wosonyeza kuti Yesu ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu komanso kuti Mulungu anamupatsa mphamvu zochitira zimenezo.

Zimene Yesu ankachita ali padzikoli, zinasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu padzikoli. Pa madalitso amene ali m’munsiwa, ndi dalitso liti limene inuyo mukuliyembekezera kwambiri? Werengani malemba amene ali kutsogolo kwa dalitso lililonse.

ALI PADZIKOLI, YESU . . .

ALI KUMWAMBA, YESU . . .

  • adzakonza zinthu zonse zimene zawonongedwa padzikoli.​—Yesaya 35:1, 2.

6. Madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse

Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti anthu azikhala moyo wabwino ngati mmene Yehova ankafunira poyamba. Anthu adzakhala ndi moyo m’paradaiso padzikoli mpaka kalekale. Onerani VIDIYO kuti muone mmene Yehova akukwaniritsira cholinga chake pogwiritsa ntchito Mwana wake Yesu.

Werengani Salimo 145:16, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mumamva bwanji mukaganizira kuti Yehova ‘adzakhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse’?

ZIMENE ENA AMANENA: “Ngati titamachita zinthu mogwirizana, tikhoza kuthetsa mavuto apadziko lonse.”

  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto ati amene maboma a anthu alephera kuwathetsa?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa cholinga chimene Mulungu anali nacho poyamba. Udzachititsa dzikoli kuti likhale paradaiso, momwe mudzakhale anthu abwino omwe azidzalambira Yehova mpaka kalekale.

Kubwereza

  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzachititsa bwanji kuti dzina la Yehova liyeretsedwe?

  • N’chifukwa chiyani timakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa zonse zimene Baibulo linalonjeza?

  • Pa madalitso onse amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse, ndi dalitso liti limene inuyo mukuliyembekezera kwambiri?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Fufuzani kuti mudziwe zimene Aramagedo amatanthauza.

“Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani zimene zingathandize mabanja kuyerekezera kuti ali m’Paradaiso.

Yerekeza Kuti Uli M’Paradaiso (1:50)