PHUNZIRO 34

Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Yehova?

Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Yehova?

Kodi panopa mwayamba kukonda kwambiri Mulungu kuposa nthawi imene munkayamba kuphunzira Baibulo? Kodi mukufuna kupitiriza kukhala naye pa ubwenzi wolimba? Ngati ndi choncho, muzikumbukira kuti Yehova akamaona kuti mukupitiriza kumukonda m’pamenenso iye angakukondeni kwambiri. Ndiye kodi mungasonyeze bwanji kuti mumamukonda?

1. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova?

Timasonyeza kuti timakonda Yehova tikamamvera malamulo ake. (Werengani 1 Yohane 5:3.) Iye satikakamiza kuti tizimumvera. Koma amafuna kuti wina aliyense wa ife azisankha yekha kumumvera kapena ayi. Yehova amachita zimenezi chifukwa amafuna kuti ‘tizimumvera mochokera pansi pa mtima.’ (Aroma 6:17) Zimenezi zikutanthauza kuti iye amafuna kuti muzimumvera chifukwa chakuti mumamukonda, osati mongokakamizika. Gawo 3 ndi 4 la bukuli likuthandizani kusonyeza kuti mumakonda Yehova mwa kuchita zimene zimamusangalatsa ndi kupewa zimene amadana nazo.

2. N’chifukwa chiyani zingativute kusonyeza kuti timakonda Yehova?

Baibulo limati: “Masoka a munthu wolungama ndi ochuluka.” (Salimo 34:19) Tonsefe timavutika kusonyeza kuti timakonda Mulungu chifukwa chakuti ndife ochimwa. Tingakumanenso ndi mavuto azachuma, kupanda chilungamo ndi mavuto ena. Tikamakumana ndi mavuto zimakhala zovuta kuchita zimene Yehova amafuna. Koma mukayesetsa kukhala okhulupirika n’kuchita zimene Yehova akufuna, m’pamenenso mumasonyeza kuti mumamukonda kwambiri kuposa chinthu china chilichonse. Mukamachita zimenezi, mumasonyeza kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova ndipo iyenso adzakhala wokhulupirika kwa inu. Yehova sadzakusiyani.​—Werengani Salimo 4:3.

FUFUZANI MOZAMA

Onani chifukwa chake Yehova amasangalala mukamamumvera komanso zimene zingakuthandizeni kuti mupitirize kukhala okhulupirika kwa iye.

3. Nkhani imene imakukhudzani

Malinga ndi zimene timawerenga m’Baibulo m’buku la Yobu, Satana ananena kuti Yobu ankatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. Masiku anonso, Satana amanena kuti anthu amatumikira Yehova chifukwa cha dyera. Werengani Yobu 1:1, 6 mpaka 2:​1-10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi Satana ananena kuti Yobu ankamvera Yehova chifukwa chiyani?​—Onani Yobu 1:9-11.

  • Kodi Satana amanena kuti anthu onse, kuphatikizapo inuyo, amamvera Yehova chifukwa chiyani?​—Onani Yobu 2:4.

Werengani Yobu 27:5b, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi Yobu anasonyeza bwanji kuti ankakonda Yehova ndi mtima wake wonse?

Yobu anasonyeza kuti amakonda Yehova pokhalabe wokhulupirika kwa iye

Nafenso timasonyeza kuti timakonda Yehova pokhalabe okhulupirika kwa iye

4. Muzisangalatsa mtima wa Yehova

Werengani Miyambo 27:11, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi Yehova amamva bwanji mukamachita zinthu mwanzeru komanso mukamamumvera? N’chifukwa chiyani mukutero?

5. N’zotheka kukhala okhulupirika kwa Yehova

Timayesetsa kuuza ena zokhudza Yehova chifukwa timamukonda. Ndipo timachita zimenezi posonyeza kuti ndife okhulupirika kwa iye ngakhale kuti nthawi zina zingakhale zovuta. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi inuyo zimakuvutani kuuza ena zokhudza Yehova?

  • Malinga ndi zimene taona m’vidiyoyi, n’chiyani chinathandiza Grayson kuti athetse mantha?

Tikamakonda zimene Yehova amakonda ndi kudana ndi zimene iye amadana nazo, sitingavutike kukhala okhulupirika kwa iye. Werengani Salimo 97:10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Malinga ndi zimene mwaphunzira, kodi zina mwa zinthu zimene Yehova amakonda ndi ziti? Nanga ndi zinthu ziti zimene amadana nazo?

  • Kodi mungatani kuti muyambe kukonda zabwino ndi kudana ndi zoipa?

6. Zinthu zimatiyendera bwino tikamamvera Yehova

Anthu amene amamvera Yehova, zinthu zimawayendera bwino nthawi zonse. Werengani Yesaya 48:​17, 18, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Malinga ndi lembali, kodi n’zomveka kukhulupirira kuti nthawi zonse Yehova akamatipatsa malangizo amadziwa kuti atithandiza? N’chifukwa chiyani mukutero?

  • Pofika pano, kodi kuphunzira Baibulo komanso zokhudza Mulungu woona Yehova, kwakuthandizani bwanji?

MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi zochita zanga zingathe kusangalatsa Mulungu?”

  • Kodi mungawerenge lemba liti lomwe lingamuthandize kudziwa kuti Yehova amasangalala kapena kukhumudwa ndi zomwe timachita?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Mungasonyeze kuti mumakonda Yehova pomumvera ndi kupitirizabe kukhala wokhulupirika kwa iye ngakhale pamene mukukumana ndi mavuto.

Kubwereza

  • Kodi mwaphunzira zotani pa chitsanzo cha Yobu?

  • Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakonda Yehova?

  • N’chiyani chingakuthandizeni kuti mupitirize kukhala wokhulupirika kwa Yehova?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani zimene zingakuthandizeni kukhala okhulupirika kwa Yehova komanso mumpingo.

“Munthu Wokhulupirika, Mudzamuchitira Mokhulupirika” 16:49

Onani mmene ana angasonyezere kuti amakonda Yehova.

Uzisangalatsa Yehova (8:16)

Kodi wachinyamata amene anzake akumukakamiza kuchita zoipa angatani kuti akhalebe wokhulupirika kwa Mulungu?

Musamangotengera Zochita za Anzanu (3:59)