PHUNZIRO 36

Muzichita Zinthu Zonse Moona Mtima

Muzichita Zinthu Zonse Moona Mtima

Aliyense amafuna kukhala ndi anzake amene amachita zinthu moona mtima. Nayenso Yehova amafuna kuti anzake azichita zinthu moona mtima. Koma kuchita zimenezi si kophweka chifukwa tikukhala m’dziko limene anthu ambiri sachita zinthu moona mtima. Ndiye kodi timapindula bwanji chifukwa chochita zinthu zonse moona mtima?

1. N’chifukwa chiyani kuchita zinthu moona mtima n’kofunika kwambiri?

Tikamachita zinthu moona mtima timasonyeza kuti timakonda ndi kulemekeza Yehova. Taganizirani izi: Yehova amadziwa chilichonse chomwe tikuganiza komanso zimene tikuchita. (Aheberi 4:13) Iye amaona tikamachita zinthu moona mtima ndipo amayamikira kwambiri. Mawu ake amanena kuti: “Munthu wochita zachiphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.”​—Miyambo 3:32.

2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timachita zinthu moona mtima?

Yehova amafuna kuti ‘tizilankhula zoona zokhazokha.’ (Zekariya 8:16, 17) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Timayesetsa kupewa kunena bodza tikamalankhulana ndi anthu am’banja lathu, ogwira nawo ntchito, abale ndi alongo mumpingo kapenanso akuluakulu a boma. Anthu oona mtima sabera anthu ena kapena kuwapusitsa. (Werengani Miyambo 24:28 ndi Aefeso 4:28.) Komanso anthu oona mtima sazemba misonkho. (Aroma 13:5-7) Choncho, tiyenera kuyesetsa “kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

3. Kodi timapindula bwanji tikamachita zinthu moona mtima?

Tikamachita zinthu moona mtima nthawi zonse, anthu amayamba kutikhulupirira. Zimenezi zimathandizanso kuti anthu onse azisangalala mumpingo ngati mmene zimakhalira m’banja. Komanso timakhala ndi chikumbumtima choyera. Tikamachita zinthu moona mtima ‘timakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu.’ Anthu amene satumikira Mulungu akamationa tikuchita zinthu moona mtima angakopeke n’kuyamba kuphunzira zokhudza Yehova.​—Tito 2:10.

FUFUZANI MOZAMA

Onani mmene kuchita zinthu moona mtima kumasangalatsira Yehova komanso mmene kungathandizire kuti zinthu zizikuyenderani bwino. Onaninso zimene mungachite kuti muzichita zinthu moona mtima nthawi zonse.

4. Timasangalatsa Yehova tikamachita zinthu moona mtima

Werengani Salimo 44:21 ndi Malaki 3:​16, kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti si nzeru kukhulupirira kuti tingamubisire zinazake Yehova?

  • Kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji tikasankha kunena zoona ngakhale pa nthawi imene kunena zoona kungakhale kovuta?

Ana akamanena zoona amasangalatsa makolo awo. Ifenso tikamanena zoona Yehova amasangalala

5. Muzichita zinthu moona mtima nthawi zonse

Anthu ambiri amaganiza kuti n’zosatheka kumachita zinthu moona mtima nthawi zonse. Koma onani chifukwa chake tiyenera kumachita zinthu moona mtima nthawi zonse. Onerani VIDIYO.

Werengani Aheberi 13:​18, kenako mukambirane mmene tingachitire zinthu moona mtima . . .

  • ndi anthu am’banja lathu.

  • kuntchito kapena kusukulu.

  • pa zochitika zina.

6. Zinthu zimatiyendera bwino tikamachita zinthu moona mtima

Nthawi zina tikamachita zinthu moona mtima tikhoza kukumana ndi mavuto. Komabe, pamapeto pake timapeza madalitso. Werengani Salimo 34:12-16, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi kuchita zinthu moona mtima kungakuthandizeni bwanji?

  1. Amuna ndi akazi okwatirana akamachita zinthu moona mtima amakhala ndi banja losangalala

  2. Mabwana amakhulupirira kwambiri antchito amene amachita zinthu moona mtima

  3. Nzika zimene zimachita zinthu moona mtima zimakhala ndi mbiri yabwino kwa akuluakulu a boma

ZIMENE ENA AMANENA: “Mabodza ena ndi ang’onoang’ono ndiye sakhala odetsa nkhawa kwenikweni.”

  • N’chifukwa chiyani mumakhulupirira kuti Yehova amadana ndi mabodza alionse?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yehova amafuna kuti anzake azichita zinthu zonse moona mtima.

Kubwereza

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife oona mtima?

  • N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti si nzeru kukhulupirira kuti tingamubisire zinazake Yehova?

  • N’chifukwa chiyani mukufuna kumachita zinthu moona mtima nthawi zonse?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kuti azichita zinthu moona mtima?

Uzinena Zoona (1:44)

Kodi kuchita zomwe talonjeza kuli ndi ubwino wotani?

Anthu Omwe Amachita Zimene Alonjeza Amadalitsidwa (9:09)

N’chiyani chinathandiza munthu yemwe ankachita zachinyengo kuti ayambe kuchita zinthu moona mtima?

“Ndinaphunzira Kuti Yehova Ndi Wachifundo Komanso Amakhululuka” (Nsanja ya Olonda, May 1, 2015)