PHUNZIRO 38

Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali

Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali

Anthufe timatha kuchita komanso kusangalala ndi zinthu zosiyanasiyana chifukwa choti tili ndi moyo. Ngakhale kuti timakumana ndi mavuto koma nthawi zambiri timatha kusangalala ndi zinthu zina pa moyo wathu. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova chifukwa chotipatsa mphatso ya moyo? Nanga n’chifukwa chiyani tikufunikira kuchita zimenezi?

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira Yehova chifukwa chotipatsa moyo?

Moyo ndi mphatso yochokera kwa Atate wathu wachikondi, Yehova. Choncho tiyenera kumamuyamikira chifukwa cha mphatso imeneyi. Baibulo limati iye ndi “kasupe wa moyo” kutanthauza kuti ndi amene analenga zamoyo zonse. (Salimo 36:9) Limanenanso kuti: “Ndi iyeyo amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25, 28) Yehova amatipatsa zinthu zonse zofunikira kuti tikhale ndi moyo. Kuwonjezera pamenepa, Yehova amatipatsa zinthu zina zosiyanasiyana kuti tizisangalala ndi moyo.​—Werengani Machitidwe 14:17.

2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova chifukwa chotipatsa mphatso ya moyo?

Yehova anaona kuti ndinu wamtengo wapatali kungochokera pamene mayi anu anatenga pakati. M’pemphero limene Yehova analola kuti lilembedwe m’Mawu ake, mtumiki wake Davide anauza Yehova kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza.” (Salimo 139:16) Yehova amaona kuti moyo wanu ndi wamtengo wapatali kwambiri. (Werengani Mateyu 10:29-31.) Zimamupweteka kwambiri Yehova akaona munthu wina akuchotsa mwadala moyo wake kapenanso wa munthu wina. a (Ekisodo 20:13) Zimamupwetekanso kwambiri tikamachitira dala zinthu zimene zingaike moyo wathu pa ngozi kapenanso tikamalephera kutsatira malangizo omwe angateteze moyo wathu ndi wa anthu ena. Tikamayesetsa kusamala moyo wathu komanso tikamalemekeza moyo wa anthu ena timasonyeza kuti timayamikira mphatso ya moyo yomwe ndi yamtengo wapatali.

FUFUZANI MOZAMA

Onani njira zina zomwe mungasonyezere kuti mumayamikira mphatso ya moyo.

3. Muzisamalira thanzi lanu

Nthawi zonse timayesetsa kuchita zimene Yehova amafuna chifukwa tinamulonjeza kuti tizimutumikira ndi moyo wathu wonse. Tikamachita zimenezi timakhala ngati tikupereka matupi athu nsembe kwa Mulungu. Werengani Aroma 12:1, 2, kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani muyenera kusamalira thanzi lanu?

  • Nanga ndi zinthu ziti zomwe mungachite posonyeza kuti mumasamalira thanzi lanu?

4. Tiziyesetsa kupewa zinthu zimene zingaike moyo wathu ndi wa anthu ena pa ngozi

Baibulo limanena kuti tiyenera kupewa zinthu zimene zimaika moyo wathu ndi wa anthu ena pa ngozi. Onerani VIDIYO kuti muone zinthu zimene mungachite kuti mupewe ngozi.

Werengani Miyambo 22:3, kenako mukambirane mmene inuyo ndi anthu ena mungapewere ngozi . . .

  • mukakhala kunyumba.

  • mukakhala kuntchito.

  • mukamachita masewera osiyanasiyana.

  • mukamayendetsa kapena kukwera zinthu monga galimoto, njinga, boti, ngolo ndi zina.

5. Muziona kuti moyo wa mwana amene sanabadwe ndi wamtengo wapatali

Davide anafotokoza kuti Yehova amachita chidwi ndi chilichonse chimene chimachitika mwana akamakula m’mimba mwa amayi ake. Werengani Salimo 139:13-17, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi Yehova amaona kuti moyo umayamba pa nthawi iti, pamene mayi wangotenga mimba kapena mwana akangobadwa?

Malamulo amene Yehova anapereka kwa Aisiraeli ankateteza moyo wa mayi komanso wa mwana amene sanabadwe. Werengani Ekisodo 21:22, 23, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi Yehova ankaona bwanji munthu yemwe wapha mwana wosabadwa mwangozi?

  • Nanga kodi angaone bwanji munthu yemwe wapha mwana wosabadwa mwadala? b

  • Kodi inuyo mukuona kuti maganizo a Mulungu pa nkhani imeneyi ndi omveka?

Onerani VIDIYO.

Nthawi zina ngakhale mayi yemwe amaona kuti moyo wa mwana wosabadwa ndi wamtengo wapatali, akhoza kukumana ndi vuto lomwe lingamuchititse kuona kuti sangachitire mwina koma kuchotsa mimba basi. Werengani Yesaya 41:10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Ngati mayi akukakamizidwa kuti achotse mimba, kodi ayenera kudalira ndani kuti amuthandize? N’chifukwa chiyani mukutero?

ZIMENE ENA AMANENA: “Mzimayi ali ndi ufulu wosankha kuchotsa mimba kapena ayi.”

  • N’chiyani chikukutsimikizirani kuti Yehova amaona kuti moyo wa mayi ndi wa mwana wosabadwa ndi wofunika kwambiri?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Baibulo limatiphunzitsa kuti tiyenera kukonda, kulemekeza ndi kuteteza mphatso ya moyo imene Yehova anatipatsa. Zimenezi zikuphatikizapo moyo wathu komanso wa anthu ena.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani Yehova amaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali?

  • Kodi Yehova amamva bwanji munthu akadzipha kapena akapha munthu wina mwadala?

  • Kodi inuyo mumayamikira mphatso ya moyo?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Yehova chifukwa chotipatsa mphatso ya moyo?

Nyimbo 141​—Moyo Ndi Wodabwitsa (2:41)

Pezani yankho la funso lakuti: Kodi Mulungu angakhululukire mzimayi yemwe anachotsapo mimba?

“Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yochotsa Mimba?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani mmene Baibulo lingathandizire munthu yemwe ali ndi maganizo ofuna kudzipha.

“Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?” (Nkhani yapawebusaiti)

a Yehova amasamalira anthu amtima wosweka. (Salimo 34:18) Anthu oterewa amakhala ndi ululu waukulu mumtima mwawo moti amafuna kudzipha. Koma Yehova amawamvetsa ndipo amafunitsitsa kuwathandiza. Kuti muone mmene malangizo a m’Baibulo angathandizire munthu kuti asiye kuganiza zofuna kudzipha, werengani nkhani yakuti, “Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?” pagawo lakuti Onani Zinanso m’phunziroli.

b Anthu amene anachotsapo mimba sayenera kumadziimba mlandu kwambiri chifukwa Yehova akhoza kuwakhululukira. Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yochotsa Mimba?” pagawo lakuti Onani Zinanso m’phunziroli.