PHUNZIRO 39
Mmene Mulungu Amaonera Magazi
Magazi ndi ofunika kwambiri. Palibe munthu amene angakhale ndi moyo popanda magazi. Mulungu ndi amene anatilenga, choncho iye ndi amene ayenera kutiuza mmene tingagwiritsire ntchito magazi. Kodi Mulungu amanena zotani zokhudza magazi? Kodi anthu ayenera kudya kapena kuikidwa magazi? Kodi mungatani kuti musankhe zinthu mwanzeru pa nkhani imeneyi?
1. Kodi Yehova amawaona bwanji magazi?
Yehova anauza atumiki ake akale kuti: “Moyo wa nyama ina iliyonse [chamoyo chilichonse] ndi magazi ake.” (Levitiko 17:14) Yehova amaona kuti magazi amaimira moyo. Choncho popeza kuti moyo ndi mphatso yopatulika yochokera kwa Mulungu, nawonso magazi ndi opatulika.
2. Mulungu amaletsa kugwiritsa ntchito magazi molakwika
Yehova analamula atumiki ake kuti asamadye magazi. (Werengani Genesis 9:4 ndi Levitiko 17:10.) Iye anabwerezanso lamuloli pogwiritsa ntchito bungwe lolamulira lomwe linalangiza Akhristu kuti ‘apitirize kupewa . . . magazi.’—Werengani Machitidwe 15:28, 29.
Kodi kupewa magazi kumatanthauza chiyani? Ngati dokotala wakuuzani kuti mupewe mowa, ndiye kuti akutanthauza kuti musiye kumwa. Ndiye kodi mungadye chakudya chomwe chili ndi mowa kapena mungaike mowawo mujakisoni n’kudzibaya? Simungachite zimenezo. N’chimodzimodzinso ndi lamulo limene Mulungu anapereka lokhudza magazi. Lamuloli limatanthauza kuti sitiyenera kudya magazi kapena nyama yosazinga. Sitiyeneranso kuphika magazi n’kudya kapena kudya chakudya chimene chasakanizidwa ndi magazi.
Nanga bwanji kugwiritsa ntchito magazi pa nkhani zachipatala? Pali njira zina zothandizira odwala zimene zimaphwanya lamulo la Mulungu lokhudza magazi. Zimenezi zikuphatikizapo kuika wodwala magazi kapena zigawo zikuluzikulu za magazi zomwe ndi: Maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana ndi madzi am’magazi. Koma pali njira zina zothandizira odwala zomwe ndi zovuta kudziwa ngati zikuphwanya lamulo la Mulungu kapena ayi. Mwachitsanzo, achipatala amatha kugwiritsa ntchito tizigawo ting’onoting’ono tomwe timatengedwa kuchokera ku zigawo zikuluzikulu za magazi. Nthawi zina pamafunikira kugwiritsa ntchito magazi a munthu yemwe akudwala omwe anatengedwa m’thupi lake n’kusungidwa. Pa nkhani ngati zimenezi, aliyense ayenera kusankha yekha zoyenera kuchita. a—Agalatiya 6:5.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti muone mmene mungasankhire zochita pa nkhani ya thandizo lachipatala lokhudza magazi.
3. Muzisankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova
Mukamasankha thandizo lachipatala, kodi mungasankhe bwanji zinthu mogwirizana ndi mmene Mulungu amaonera magazi? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane kufunika kotsatira mfundo zomwe zili m’munsizi:
-
Muzipemphera kuti Yehova akuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru.—Yakobo 1:5.
-
Muzifufuza mfundo za m’Baibulo n’kuona mmene mungazigwiritsire ntchito.—Miyambo 13:16.
-
Fufuzani njira zimene kwanuko achipatala amagwiritsa ntchito pothandiza odwala omwe akufunikira magazi.
-
Pa njira zimene mwapezazo, onani njira zimene simungalole kulandira.
-
Sankhani zinthu zimene zingakuthandizeni kuti mukhale ndi chikumbumtima choyera.—Machitidwe 24:16. b
-
Dziwani kuti palibe munthu amene ayenera kukusankhirani zochita pa nkhani zokhudza chikumbumtima kaya ndi mkazi kapena mwamuna wanu, mkulu mumpingo kapenanso munthu amene amakuphunzitsani Baibulo.—Aroma 14:12.
-
Lembani zimene mwasankha.
4. A Mboni za Yehova amafuna kulandira thandizo labwino lachipatala
N’zotheka kumvera lamulo la Mulungu lokhudza magazi ndipo tingathe kulandira thandizo labwino lachipatala popanda kuikidwa magazi. Onerani VIDIYO.
Werengani Tito 3:2, kenako mukambirane funso ili:
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu mwaulemu ndiponso mofatsa tikamalankhula ndi madokotala?
Zosaloledwa |
Mkhristu angasankhe yekha |
---|---|
A. Madzi am’magazi |
Tizigawo tochokera m’madzi am’magazi |
B. Maselo oyera |
Tizigawo tochokera m’maselo oyera |
C. Maselo othandiza magazi kuundana |
Tizigawo tochokera m’maselo othandiza magazi kuundana |
D. Maselo ofiira |
Tizigawo tochokera m’maselo ofiira |
5. Zimene muyenera kudziwa zokhudza tizigawo ta magazi
Magazi ali ndi zigawo zikuluzikulu 4 zomwe ndi: Maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana ndi madzi am’magazi. Zigawo zimenezi zili ndi tizigawo c ting’onoting’ono tambirimbiri. Tina mwa tizigawoti amatigwiritsa ntchito popanga mankhwala olimbana ndi matenda kapenanso othandiza kuti magazi aundane n’kusiya kutuluka.
Pa nkhani yosankha tizigawo ting’onoting’ono ta magazi, Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha zochita mogwirizana ndi chikumbumtima chake. Akhristu ena angasankhe kukana thandizo lachipatala lomwe likufunika kuti madokotala agwiritse ntchito tizigawo ting’onoting’ono ta magazi. Pomwe chikumbumtima cha Akhristu ena chingawalole kulandira tizigawo ting’onoting’ono ta magazi.
Mukamasankha zochita pa nkhaniyi, dzifunseni kuti:
-
Kodi ndingamufotokozere bwanji dokotala chifukwa chimene ndikukanira kapena kulola kuti agwiritse ntchito tizigawo ting’onoting’ono ta magazi pondithandiza?
MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi n’kulakwa kuikidwa magazi?”
-
Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yehova amafuna kuti tiziona kuti magazi ndi opatulika.
Kubwereza
-
N’chifukwa chiyani Yehova amaona kuti magazi ndi opatulika?
-
Kodi timadziwa bwanji kuti lamulo la Mulungu lakuti tizipewa magazi limagwiranso ntchito pa nkhani ya kupewa kuikidwa magazi?
-
Kodi mungasankhe bwanji zochita mwanzeru pa nkhani yogwiritsa ntchito magazi monga chithandizo cha chipatala?
ONANI ZINANSO
Kodi muyenera kuganizira zinthu ziti musanasankhe thandizo lachipatala lofunika kugwiritsa ntchito magazi anu omwe?
“Mafunso Ochokera kwa Owerenga” (Nsanja ya Olonda, October 15, 2000)
Kodi muyenera kuganizira chiyani mukamasankha kulandira kapena kukana tizigawo ting’onoting’ono ta magazi?
“Mafunso Ochokera kwa Owerenga” (Nsanja ya Olonda, June 15, 2004)
Onani mmene akulu omwe amatumikira m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala amathandizira abale ndi alongo awo.
a Onani Phunziro 35, “N’chiyani Chingatithandize Kuti Tizisankha Zinthu Mwanzeru?”
b Onani mfundo 5, “Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Tizigawo ta Magazi,” komanso Mawu Akumapeto 3, “Njira Zothandizira Odwala Zokhudza Magazi.”
c Madokotala ena amaona kuti zigawo zikuluzikulu 4 za magazi zili ngati tizigawo ting’onoting’ono. Choncho mungafunike kufotokozera dokotala wanu momveka bwino kuti munasankha kuti simungalole kuikidwa magazi athunthu kapena maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana ndi madzi am’magazi.
MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE—KUPHUNZIRA BAIBULO MOKAMBIRANA