PHUNZIRO 40
Tingatani Kuti Mulungu Azitiona Kuti Ndife Oyera?
Taganizirani zimene mayi wachikondi amachita pokonzekeretsa mwana wake kuti apite kusukulu. Mayiyo amaonetsetsa kuti mwana wake wasamba ndiponso wavala zovala zoyera. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti mwanayo akhale ndi thanzi labwino, ndipo anthu ena amaona kuti makolo ake amamusamalira. N’chimodzimodzinso Atate wathu wachikondi Yehova. Iye amafuna kuti tizikhala oyera mwakuthupi, komanso amafuna kuti zimene timaganiza, kulankhula ndi kuchita zizisonyeza kuti ndife oyera. Tikamayesetsa kukhala oyera zinthu zimatiyendera bwino ndiponso timalemekeza Yehova.
1. Tingatani kuti tikhale oyera mwakuthupi?
Yehova amatiuza kuti: “Mukhale oyera.” (1 Petulo 1:16) Kuti Yehova azitiona kuti ndife oyera, tiyenera kukhala ndi makhalidwe oyera komanso kukhala oyera mwakuthupi. Tingakhale oyera mwakuthupi ngati timasamba nthawi zonse, kuchapa zovala zathu, kukonza pakhomo komanso ngati timaonetsetsa kuti galimoto kapena njinga yathu ndi zoyera. Tikhozanso kugwira nawo ntchito yoyeretsa Nyumba ya Ufumu yathu. Tikamayesetsa kukhala oyera mwakuthupi, timalemekeza Yehova.—2 Akorinto 6:3, 4.
2. Kodi ndi makhalidwe ati amene tiyenera kupewa kuti tikhale oyera?
Baibulo limatilimbikitsa kuti “tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kupewa chilichonse chimene chingawononge thupi kapena maganizo athu. Zimene timaganiza ziyenera kusangalatsa Yehova. Choncho tiyenera kuyesetsa kupewa kuganiza zinthu zoipa. (Salimo 104:34) Tiyeneranso kuyesetsa kuti zolankhula zathu zizikhala zabwino.—Werengani Akolose 3:8.
Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene zingachititse kuti tisakhale oyera mwakuthupi komanso mwa makhalidwe? Pali zinthu zina zomwe zikhoza kuwononga thupi lathu. Choncho timapewa zinthu monga kusuta fodya, kusuta chamba, kutafuna mtedza wotchedwa betel, kutafuna masamba enaake otchedwa coca, kugwiritsa ntchito mankhwala oletsedwa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala molakwika. Tikamapewa zinthu zimenezi timakhala anthu athanzi komanso timasonyeza kuti timalemekeza mphatso ya moyo. Tiyeneranso kuyesetsa kukhala oyera mwa makhalidwe popewa makhalidwe amene angachititse kuti tisakhale oyera monga, kudziseweretsa maliseche ndi kuonera zolaula. (Salimo 119:37; Aefeso 5:5) Si zophweka kusiya makhalidwe ngati amenewa komabe Yehova angatithandize kuti tiwasiye.—Werengani Yesaya 41:13.
FUFUZANI MOZAMA
Onani chifukwa chake tikakhala oyera mwakuthupi timalemekeza Yehova komanso onani zimene tingachite kuti tisiye makhalidwe amene angachititse kuti tisakhale oyera.
3. Tikakhala oyera mwakuthupi timalemekeza Yehova
Tikamawerenga zokhudza malamulo amene Yehova anapereka ku mtundu wa Isiraeli, timaona kuti Yehova amafuna kuti anthu ake azikhala oyera. Werengani Ekisodo 19:10 ndi 30:17-19, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi mavesiwa akusonyeza bwanji kuti Yehova amafuna kuti anthu ake azikhala aukhondo?
-
Ndi zinthu zabwino ziti zimene muyenera kumachita kuti mukhalebe oyera mwakuthupi?
Pamafunika nthawi komanso khama kuti munthu akhale waukhondo. Koma n’zotheka kuchita zimenezi posatengera dera limene tikukhala komanso kuti ndife olemera kapena osauka. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
-
Kodi zinthu zathu zikamasungidwa mwadongosolo komanso zikamakhala zaukhondo, zingachititse bwanji kuti anthu amene timawalalikira azilemekeza Yehova?
4. Siyani makhalidwe oipa
Ngati mumasuta fodya kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo chifukwa chongofuna kusangalala, n’kutheka kuti mumadziwa mmene zimavutira kusiya makhalidwe amenewa. Kodi n’chiyani chimene chingakuthandizeni? Muziganizira mmene kuchita zimenezi kungakhudzire moyo wanu. Werengani Mateyu 22:37-39, kenako mukambirane mmene kusuta fodya kapena kugwiritsa ntchito mankhwala molakwika kungakhudzire . . .
-
ubwenzi umene munthu ali nawo ndi Yehova.
-
banja la munthu ndi anthu ena.
Ganizirani zimene mungachite kuti mukwanitse kusiya khalidwe loipa. a Onerani VIDIYO.
Werengani Afilipi 4:13, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi kupemphera, kuphunzira Baibulo ndiponso kuchita nawo misonkhano nthawi zonse kungathandize bwanji munthu kusiya khalidwe loipa?
5. Yesetsani kusiya kuganizira ndi kuchita zinthu zoipa
Werengani Akolose 3:5, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi timadziwa bwanji kuti kuonera zolaula, kutumizira ena mauthenga kapena zinthu zina zolaula komanso kudziseweretsa maliseche Yehova amaona kuti ndi kodetsa?
-
Kodi mukuganiza kuti n’zomveka kuti Yehova aziyembekezera kuti tizikhala ndi makhalidwe oyera? N’chifukwa chiyani mukutero?
Onani zimene mungachite kuti musamaganizire zoipa. Onerani VIDIYO.
Yesu anagwiritsa ntchito fanizo lomwe limasonyeza kuti tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tikhalebe oyera. Werengani Mateyu 5:29, 30, kenako mukambirane funso ili:
-
Palembali Yesu sankanena kuti tiyenera kudzivulaza koma ankatanthauza kuti tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tizichita zimene Mulungu amafuna. Kodi n’chiyani chimene munthu ayenera kuchita kuti asamaganizire zinthu zoipa? b
Yehova amayamikira kwambiri mukamayesetsa kuchita khama kuti musiye kuganizira zinthu zoipa. Werengani Salimo 103:13, 14, kenako mukambirane funso ili:
-
Ngati mukuyesetsa kulimbana ndi khalidwe linalake loipa, kodi lembali lingakuthandizeni bwanji kuti musafooke?
Musataye mtima
Zimakhala zosavuta kuganiza kuti, ‘Popeza ndachitanso khalidwe loipali, basi sindingakwanitse kulisiya.’ Koma taganizirani mfundo iyi: Munthu amene ali pampikisano wothamanga akapunthwa n’kugwa, sizitanthauza kuti sangapambane mpikisanowo. Sizitanthauzanso kuti akuyenera kubwerera n’kukayambiranso kuthamangako. N’zimene zingachitike ngati mwayambiranso kuchita khalidwe linalake loipa. Mukalephera ulendo umodzi wokha, sizitanthauza kuti mwalephera kulimbana ndi khalidwelo. Sizitanthauzanso kuti khama lonse limene munachita lija langopita pachabe. Zimachitika ndithu kuyambiranso khalidwe linalake loipa. Koma zikatere, musataye mtima chifukwa sizitanthauza kuti ndinu wolephera. Yehova akhoza kukuthandizani kusiya khalidwe loipalo.
ZIMENE ENA AMANENA: “Ine ndiye zinandilowerera kwambiri moti sindingasiye.”
-
Kodi mungagwiritse ntchito lemba liti pothandiza munthuyo kudziwa kuti Yehova angamuthandize kusiya khalidwe loipalo?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Timasangalatsa Yehova tikamayesetsa kukhala aukhondo ndiponso tikamapewa kuganizira ndi kuchita makhalidwe oipa.
Kubwereza
-
N’chifukwa chiyani kukhala oyera n’kofunika kwambiri?
-
Kodi mungatani kuti mukhale aukhondo?
-
Kodi mungatani kuti muzipewa kuganiza ndi kuchita zinthu zoipa?
ONANI ZINANSO
Ndi zinthu ziti zimene mungachite kuti mukhale aukhondo ngakhale zitakhala kuti ndinu osauka?
Onani kuopsa kuonera zolaula.
“Kodi Kuonera Zolaula Kuli Ndi Mavuto Otani?” (Nsanja ya Olonda, August 1, 2013)
Onani zimene munthu wina anachita kuti asiye kuonera zolaula.
“Ndinasintha Khalidwe Langa Movutikira Kwambiri” (Nsanja ya Olonda Na. 4 2016)
a Nkhani yamutu wakuti “N’zotheka Kusiya Fodya,” yomwe ikupeza pachigawo chakuti Onani Zinanso m’phunziroli, ikufotokoza mfundo zimene zingathandize munthu kuthana ndi vuto losuta fodya.
b Kuti mudziwe zimene mungachite kuti musamadziseweretse maliseche, onani nkhani yakuti, “Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Chizolowezi Choseweretsa Maliseche?” m’buku lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amadzifunsa, Buku Loyamba, mutu 25.
MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE—KUPHUNZIRA BAIBULO MOKAMBIRANA