PHUNZIRO 41
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kugonana?
Anthu ambiri amaona kuti nkhani zokhudza kugonana ndi zoumitsa pakamwa. Komabe, Baibulo likamanena zokhudza kugonana, limanena zinthu mosapita m’mbali, koma mwaulemu. Ndipo zimene limanena n’zothandiza kwambiri. Zimenezi ndi zomveka chifukwa Yehova ndi amene anatilenga. Choncho amadziwa bwino zimene zingatithandize kuti tizikhala ndi moyo wabwino. Iye amatiuza zimene tiyenera kuchita kuti tizimusangalatsa ndiponso zimene zingatithandize kuti tizisangalala ndi moyo kuyambira panopa mpaka kalekale.
1. Kodi maganizo a Yehova ndi otani pa nkhani ya kugonana?
Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Yehova yomwe anapereka kwa anthu okwatirana kuti azisangalala nayo. Mphatsoyi simangothandiza anthu kuti azibereka ana basi, koma imawathandizanso kuti azisonyezana chikondi n’kumasangalala. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amati: “Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.” (Miyambo 5:18, 19) Yehova amayembekezera kuti Akhristu okwatirana azikhala okhulupirika m’banja, choncho sangachite chigololo.—Werengani Aheberi 13:4.
2. Kodi chiwerewere n’chiyani?
Baibulo limatiuza kuti “adama [achiwerewere] . . . sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Olemba Baibulo ena amene analilemba m’Chigiriki anagwiritsa ntchito mawu akuti por·neiʹa ponena za chiwerewere. Mawuwa amanena za (1) kugonana a kwa anthu amene sali pabanja, (2) kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, komanso (3) kugonana ndi nyama. Timasangalatsa Yehova komanso timakhala ndi moyo wabwino tikamayesetsa “kupewa dama” kapena kuti chiwerewere.—1 Atesalonika 4:3.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene mungachite kuti mupewe chiwerewere komanso phindu limene mungapeze ngati mutayesetsa kukhalabe ndi makhalidwe oyera.
3. Muziyesetsa kupewa chiwerewere
Yosefe, yemwe anali munthu wokhulupirika, anakana kugonana ndi mzimayi yemwe ankamunyengerera kuti achite naye zachiwerewere. Werengani Genesis 39:1-12, kenako mukambirane mafunso awa:
-
N’chifukwa chiyani Yosefe anakana kuchita chiwerewere?—Onani vesi 9.
-
Kodi mukuganiza kuti Yosefe anachita zinthu mwanzeru? N’chifukwa chiyani mukutero?
Kodi masiku ano achinyamata angatsanzire bwanji Yosefe pa nkhani yokana kuchita chiwerewere? Onerani VIDIYO.
Yehova amafuna kuti tonsefe tiziyesetsa kupewa chiwerewere. Werengani 1 Akorinto 6:18, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingapangitse munthu kuchita chiwerewere?
-
Kodi mungatani kuti mupewe kuchita chiwerewere?
4. Yesetsani kuti musagonje pa mayesero
N’chiyani chingapangitse kuti munthu agonje mosavuta akamayesedwa kuti achite chiwerewere? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
-
Kodi m’bale wamuvidiyoyi anachita chiyani atazindikira kuti zinthu zina zimene amaganiza ndi kuchita zikanachititsa kuti asiye kukhala wokhulupirika kwa mkazi wake?
Ngakhale Akhristu okhulupirika amafunika kuchita khama kuti asamaganizire zinthu zoipa. Kodi mungatani kuti musamaganizire zinthu zachiwerewere? Werengani Afilipi 4:8, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kumaziganizira?
-
Kodi kuwerenga Baibulo komanso kukhala ndi zochita zambiri potumikira Yehova kungatithandize bwanji kuti tipewe mayesero?
5. Mfundo za Yehova zimatithandiza kukhala ndi moyo wabwino
Yehova amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino. Iye amatiuza zimene tingachite kuti tikhale ndi makhalidwe oyera komanso ubwino wochita zimenezi. Werengani Miyambo 7:7-27 kapena onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
-
Kodi mnyamatayu anachita chiyani chomwe chikanatha kumulowetsa m’mayesero?—Onani Miyambo 7:8, 9.
-
Lemba la Miyambo 7:23, 26, limasonyeza kuti kuchita chiwerewere kukhoza kutibweretsera mavuto aakulu. Ndiye kodi tingapewe mavuto ati tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe oyera?
-
Kodi kukhala ndi makhalidwe oyera kungatithandize bwanji kuti tizisangalala ndi moyo panopa mpaka kalekale?
Anthu ena amaona kuti zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana kwa amuna komanso akazi okhaokha, ndi kukhwimitsa zinthu. Koma zimenezi si zoona chifukwa Yehova amatikonda ndipo amafuna kuti tonse tizisangalala ndi moyo panopa mpaka kalekale. Kuti zimenezi zitheke, tiziyesetsa kutsatira mfundo zake. Werengani 1 Akorinto 6:9-11, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha ndi khalidwe lokhalo limene Mulungu amadana nalo?
Kuti tizisangalatsa Mulungu, tonsefe tiyenera kuyesetsa kusintha moyo wathu. Kodi kuchita zimenezi n’kothandizadi? Werengani Salimo 19:8, 11, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi Yehova anachita bwino kutipatsa mfundo zamakhalidwe abwino kapena anangokhwimitsa zinthu? N’chifukwa chiyani mukutero?
ZIMENE ENA AMANENA: “Palibe vuto kugonana ndi wina aliyense amene ukufuna, bola ngati mukukondana.”
-
Kodi inuyo mungamuuze zotani munthu wotereyu?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo imathandiza kuti mwamuna ndi mkazi wake azisangalala.
Kubwereza
-
Kodi kuchita chiwerewere kumaphatikizaponso kuchita zinthu ziti?
-
N’chiyani chingatithandize kuti tipewe kuchita chiwerewere?
-
Kodi timapindula bwanji tikamatsatira mfundo za Yehova zamakhalidwe abwino?
ONANI ZINANSO
Onani chifukwa chake Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi azimanga kaye banja lawo asanatengane.
Onani chifukwa chimene Baibulo likamaphunzitsa kuti kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha n’kolakwika, silitanthauza kuti tizidana ndi anthu amene amachita zimenezi.
“Kodi Kugonana Kwa Amuna Kapena Akazi Okhaokha N’kolakwika?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani mmene malamulo a Mulungu pa nkhani zokhudza kugonana amatitetezera.
“Kodi Kugonana M’kamwa Kumakhaladi Kugonana?” (Nkhani yapawebusaiti)
Munkhani yakuti, “Anandilandira Mwaulemu Kwambiri,” onani zimene zinathandiza munthu wina kusiya khalidwe logonana ndi amuna anzake n’cholinga choti azisangalatsa Mulungu.
“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2011)
a Zimenezi zikuphatikizapo kuchita zinthu monga chiwerewere, kugonana m’kamwa, kugonana kobibira komanso kuseweretsa maliseche a munthu wina ndi cholinga chofuna kudzutsa kapena kukhutiritsa chilakolako cha kugonana.
MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE—KUPHUNZIRA BAIBULO MOKAMBIRANA