PHUNZIRO 42
Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Pabanja Ndi Kusakhala Pabanja?
Anthu azikhalidwe zina amakhulupirira kuti munthu sangakhale wosangalala pokhapokha akhale pabanja. Komabe, si anthu onse omwe ali pabanja amene amakhala mosangalala. Komanso si anthu onse amene sali pabanja amene amakhala osasangalala. Baibulo limanena kuti kukhala pabanja komanso kusakhala pabanja, zonse ndi mphatso zochokera kwa Yehova.
1. Kodi kusakhala pabanja kuli ndi ubwino wotani?
Baibulo limati: “Nayenso amene walekana ndi moyo wokhala yekha n’kulowa m’banja wachita bwino, koma amene sanalowe m’banja wachita bwino koposa.” (Werengani 1 Akorinto 7:32, 33, 38.) N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu amene wasankha kusakhala pabanja “wachita bwino koposa”? Popeza kuti Mkhristu amene sali pabanja sakhala ndi udindo wosamalira mwamuna kapena mkazi wake, iye amakhala ndi ufulu wambiri. Anthu amene sali pabanja akhoza kuwonjezera utumiki wawo m’njira zambiri. Mwachitsanzo, angapite kudziko lina kuti akalalikire uthenga wabwino. Komanso chofunika kwambiri, amakhala ndi nthawi yambiri yolimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova.
2. Kodi kupanga ukwati wovomerezeka ndi boma kuli ndi ubwino wotani?
Kukhala pabanja nakonso, kuli ndi ubwino wake ngati mmene zilili ndi kusakhala pabanja. Baibulo limanena kuti “awiri amaposa mmodzi.” (Mlaliki 4:9) Komabe, kuti banja liziyenda bwino, anthu okwatiranawo amafunikira kutsatira mfundo za m’Baibulo. Anthu amene amapanga ukwati wovomerezeka ndi boma, amalonjeza kuti azikonda ndi kulemekeza mnzawoyo komanso kumuona kuti ndi wofunika kwambiri. Anthu amene ali m’banja lotereli, amaona kuti ndi otetezeka kwambiri kusiyana ndi anthu amene amangotengana n’kumakhala limodzi. Ubwino winanso ndi wakuti ana amene abadwira m’banja limene makolo awo anapanga ukwati wovomerezeka ndi boma amakhala otetezeka.
3. Kodi maganizo a Yehova ndi otani pa nkhani ya banja?
Pamene Yehova ankayambitsa banja ananena kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake.” (Genesis 2:24) Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi akakwatirana azikondana n’kumakhala limodzi kwa moyo wawo wonse. Iye amalola munthu kuthetsa ukwati pokhapokha ngati mnzake wachita chigololo. Zikatere, Yehova amapereka mwayi kwa munthu wosalakwayo kuti asankhe kuthetsa banja kapena ayi. a (Mateyu 19:9) Yehova safuna kuti Akhristu azikhala pamitala.—1 Timoteyo 3:2.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene mungachite kuti muzisangalala komanso kusangalatsa Yehova kaya muli pabanja kapena ayi.
4. Muzigwiritsa ntchito bwino mphatso ya kusakhala pabanja
Yesu ankaona kuti kusakhala pabanja ndi mphatso. (Mateyu 19:11, 12) Werengani Mateyu 4:23, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji mphatso ya kusakhala pabanja potumikira Atate wake ndi kuthandiza anthu ena?
Akhristu akhoza kumasangalala pogwiritsa ntchito mphatso yawo ya kusakhala pabanja ngati mmene Yesu ankachitira. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi Akhristu angagwiritse ntchito bwanji mphatso yawo ya kusakhala pabanja?
Kodi mukudziwa?
Baibulo silinena zaka zimene munthu ayenera kukhala pabanja. Komabe, limalimbikitsa kuti munthu ayenera kudikira mpaka pa nthawi imene “wapitirira pachimake pa unyamata.” Pa nthawi imeneyi, wachinyamata amakhala ndi chilakolako champhamvu kwambiri cha kugonana zomwe zingachititse kuti alephere kusankha zinthu moyenera.—1 Akorinto 7:36.
5. Sankhani mwanzeru amene mukufuna kukwatirana naye
Kusankha munthu yemwe mukufuna kukwatirana naye ndi nkhani yaikulu. Werengani Mateyu 19:4-6, 9, kenako mukambirane funso ili:
-
N’chifukwa chiyani Mkhristu sayenera kuthamangira kulowa m’banja?
Baibulo lingakuthandizeni kuti musankhe bwino munthu yemwe mungakhale naye pabanja. Koma chofunika kwambiri ndi kusankha munthu yemwe amakonda Yehova. b Werengani 1 Akorinto 7:39 ndi 2 Akorinto 6:14. Kenako mukambirane mafunso awa:
-
N’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kukwatirana ndi Mkhristu mnzake?
-
Kodi mukuganiza kuti Yehova angamve bwanji ngati Mkhristu atakwatirana ndi munthu yemwe samutumikira?
6. Muziona ukwati mmene Yehova amauonera
Kale ku Isiraeli, amuna ena ankasiya akazi awo pa zifukwa zosamveka. Werengani Malaki 2:13, 14, 16, kenako mukambirane funso ili:
-
N’chifukwa chiyani Yehova amadana ndi kuthetsa banja pa zifukwa zosamveka?
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
-
Ngati munakwatirana ndi munthu yemwe satumikira Yehova, kodi mungatani kuti banja lanu liziyenda bwino?
7. Muzigwiritsa ntchito mfundo za Yehova zokhudza ukwati
Munthu angafunike kuchita khama kuti azigwiritsa ntchito mfundo za Yehova zokhudza ukwati. c Komabe Yehova amadalitsa anthu amene amayesetsa kuchita zimenezi. Onerani VIDIYO.
Werengani Aheberi 13:4, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi inuyo mukuona kuti mfundo zimene Yehova anatipatsa zokhudza banja ndi zomveka? N’chifukwa chiyani mukutero?
Yehova amafuna kuti Akhristu amene akufuna kukwatirana azikalembetsa ukwati wawo kuboma. Akhristu amene banja lawo latha nawonso amafunika kukatenga chikalata chothetsera ukwati kuboma, chifukwa n’zimene maboma amafuna kuti nzika zawo zizichita. Werengani Tito 3:1, kenako mukambirane funso ili:
-
Ngati muli pabanja, kodi munalembetsa ukwati wanu kuboma?
MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi pali chifukwa chokalembetsera ukwati wanga kuboma? Si bola ngati tikukondana basi?”
-
Kodi munthu wotereyu mungamuyankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Kukhala pabanja kapena kusakhala pabanja, zonse ndi mphatso zochokera kwa Yehova. Zonse zingathandize munthu amene akuchita zimene Yehova amafuna kukhala wosangalala.
Kubwereza
-
Kodi munthu angatani kuti azigwiritsa ntchito bwino mphatso yake ya kusakhala pabanja?
-
N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti Mkhristu azikwatirana ndi Mkhristu mnzake?
-
Kodi Baibulo limanena kuti munthu akhoza kuthetsa banja pa chifukwa chiti?
ONANI ZINANSO
Onerani vidiyo ya mbali zitatu yomwe ingakuthandizeni kusankha zochita mwanzeru pa nkhani zokhudza chibwenzi komanso kukhala pabanja.
Onani chifukwa chake m’bale wina amaona kuti zimene Yehova wamupatsa ndi zamtengo wapatali kwambiri kuposa zinthu zonse zimene anasiya.
Ndinkakhulupirira Kuti Nayenso Akhoza Kuphunzira Choonadi 1:56
Kodi munthu ayenera kuganizira mfundo ziti akamafuna kupatukana kapena kuthetsa ukwati?
“Tizilemekeza ‘Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi’” (Nsanja ya Olonda, December 2018)
a Onani Mawu Akumapeto 4, pa nkhani ya kupatukana ngati wina sanachite chigololo.
b M’zikhalidwe zina, makolo amatha kusankhira mwana wawo munthu woti adzakwatirane naye. Ngati zili choncho, makolo achikondi amayang’ana munthu amene amakonda Yehova osati chuma chimene munthuyo ali nacho.
c Ngati mukukhala ndi munthu amene simunakwatirane naye, zili ndi inu kusankha kumusiya kapena kukwatirana naye.
MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE—KUPHUNZIRA BAIBULO MOKAMBIRANA