PHUNZIRO 45

Kodi Kusakhala Mbali ya Dziko Kumatanthauza Chiyani?

Kodi Kusakhala Mbali ya Dziko Kumatanthauza Chiyani?

Yesu anaphunzitsa kuti otsatira ake sayenera ‘kukhala mbali ya dziko.’ (Yohane 15:19) Zimenezi zikutanthauza kusalowerera ndale kapena nkhondo zimene zimachitika m’dzikoli. Koma kuchita zimenezi si kophweka ndipo anthu angamatinyoze kapena kutiseka chifukwa chosachita nawo zinthu zam’dziko. Kodi tingatani kuti tisakhale mbali ya dziko ndi cholinga choti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova Mulungu?

1. Kodi Akhristu oona amasonyeza bwanji kuti amalemekeza maboma a anthu?

Akhristu amalemekeza maboma a anthu pomvera zimene Yesu ananena kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara.” Choncho, timamvera malamulo am’dziko lomwe tikukhala omwe amaphatikizapo kupereka misonkho. (Maliko 12:17) Baibulo limanena kuti maboma a anthu alipo chifukwa chakuti Yehova wawalola kuti alamulire. (Aroma 13:1) Choncho timazindikira kuti maboma a anthu ali ndi malire, kapena kuti mphamvu zochepa, powayerekezera ndi Mulungu. Timadziwa kuti Mulungu wathu yekha ndi amene adzathetse mavuto onse a anthu pogwiritsa ntchito Ufumu wake.

2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitili mbali ya dziko?

Mofanana ndi Yesu, nafenso sitichita nawo zandale. Pa nthawi ina anthu ataona zozizwitsa zimene Yesu anachita ankafuna kumuveka ufumu koma iye anakana. (Yohane 6:15) N’chifukwa chiyani Yesu anakana? Iye ananena kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Popeza kuti ndife ophunzira a Yesu, nafenso timakana kukhala mbali ya dziko ndipo timachita zimenezi m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, sitimenya nawo nkhondo. (Werengani Mika 4:3.) Ngakhale kuti zizindikiro ngati mbendera timaziona kuti ndi zofunika, koma sitimazichitira sawatcha kapena kuzilambira chifukwa kuchita zimenezi kuli ngati kulambira mafano. (1 Yohane 5:21) Komanso sitiikira kumbuyo kapena kutsutsa chipani china chilichonse cha ndale ngakhalenso mtsogoleri wake. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti ndife okhulupirika ndi mtima wonse ku boma la Mulungu kapena kuti Ufumu wake.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zinthu zimene zingachititse kuti zikhale zovuta kusakhala mbali ya dziko, kenako ganizirani mmene mungasankhire zinthu zomwe zingasangalatse Yehova.

3. Akhristu oona sakhala mbali ya dziko

Yesu ndi otsatira ake anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Werengani Aroma 13:1, 5-7 ndi 1 Petulo 2:13, 14. Kenako onerani VIDIYO, ndi kukambirana mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani timafunika kulemekeza maboma a anthu?

  • Ndi zinthu ziti zomwe tingachite posonyeza kuti timawamvera?

Pa nthawi ya nkhondo, mayiko ena amanena kuti sali mbali ya gulu lina lililonse la nkhondo, koma amapezeka kuti akuthandiza magulu awiri omwe akumenyanawo. Ndiye kodi kusakhala mbali ya dziko kumatanthauza chiyani? Werengani Yohane 17:16. Kenako, muonere VIDIYO ndi kukambirana funso ili:

  • Kodi kusakhala mbali ya dziko kumatanthauza chiyani?

Mungatani ngati akuluakulu a boma akufuna kuti muchite zinthu zotsutsana ndi malamulo a Mulungu? Werengani Machitidwe 5:28, 29. Kenako, muonere VIDIYO ndi kukambirana mafunso awa:

  • Ngati zimene malamulo a anthu amanena n’zotsutsana ndi zimene lamulo la Mulungu likunena, kodi tiyenera kumvera lamulo la ndani?

  • Kodi mukuganiza kuti Mkhristu sakuyenera kumvera olamulira a dziko pa zinthu ngati ziti?

4. Muzipewa kuganiza ndi kuchita zinthu zosonyeza kuti muli mbali ya dziko

Werengani 1 Yohane 5:21. Kenako, muonere VIDIYO ndi kukambirana mafunso awa:

  • Muvidiyoyi, n’chifukwa chiyani Ayenge anakana kulowa chipani cha ndale kapena kuchita miyambo yosonyeza kukonda dziko lawo monga kuchitira sawatcha mbendera?

  • Kodi mukuganiza kuti iye anasankha zinthu mwanzeru?

Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene zingachititse kuti zikhale zovuta kusakhala mbali ya dziko? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitili mbali ya dziko pa nthawi imene pakuchitika mipikisano ya masewera a mayiko osiyanasiyana?

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitili mbali ya dziko ngati andale asankha zinthu zabwino kapena zoipa zomwe zingathe kukhudza moyo wathu?

  • Kodi zimene timawerenga ndi kumvetsera kapenanso zimene timamva kwa anthu amene timacheza nawo zingatikhudze bwanji pa nkhani ya kusakhala mbali ya dziko?

Kodi Mkhristu ayenera kupewa kuganizira ndiponso kuchita zinthu ziti zosonyeza kuti ali mbali ya dziko?

MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “N’chifukwa chiyani simuchitira sawatcha mbendera kapena kuimba nyimbo ya fuko?”

  • Kodi mungamuyankhe bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Akhristu amayesetsa kupewa kuganiza, kulankhula ndi kuchita zinthu zomwe zingawachititse kukhala mbali ya dziko.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza maboma a anthu?

  • N’chifukwa chiyani sitichita nawo zandale?

  • Ndi zinthu ziti zomwe zingachititse kuti tikhale mbali ya dziko?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Kodi tingalolere kusiya zinthu ziti n’cholinga choti tisakhale mbali ya dziko?

Yehova Sanatisiye (3:14)

Kodi mabanja angakonzekere bwanji kupewa mayesero omwe angawachititse kuti akhale mbali ya dziko?

Tisamachite Zinthu Zosonyeza Kuti Tili Mbali ya Dziko Tikakhala Pagulu (4:25)

N’chifukwa chiyani kuteteza dziko lanu si kofunika kwambiri poyerekezera ndi kudzipereka kwa Mulungu?

“Zinthu Zonse N’zotheka ndi Mulungu” (5:19)