Kodi Ndakonzeka?

Kodi Ndakonzeka?

Kodi Ndakonzeka Kulalikira Limodzi Ndi Mpingo?

Mukhoza kukhala wofalitsa wosabatizidwa ngati . . .

  • Nthawi zonse mumawerenga Baibulo, mumapemphera komanso mumachita nawo misonkhano yampingo.

  • Mumakonda ndi kukhulupirira zomwe mukuphunzira ndipo mukufuna kuyamba kuuzako anthu ena.

  • Mumakonda Yehova komanso mumacheza ndi anthu omwe amamukonda.

  • Munafufutitsa dzina lanu ndiponso kusiyiratu kuchita zinthu zokhudza ndale komanso chipembedzo chonyenga.

  • Mumatsatira mfundo za Yehova pa moyo wanu ndiponso mukufuna kukhala wa Mboni za Yehova.

Ngati mukuona kuti mwakonzeka kuyamba kulalikira limodzi ndi mpingo, amene amakuphunzitsani Baibulo angakonze zoti mukumane ndi akulu n’cholinga choti akuuzeni zoyenera kuchita.

Kodi Ndakonzeka Kubatizidwa?

Mukhoza kubatizidwa ngati . . .

  • Ndinu wofalitsa wosabatizidwa.

  • Mumayesetsa kulalikira nthawi zonse.

  • Mumamvera komanso kutsatira malangizo ochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”​—Mateyu 24:45-47.

  • Munadzipereka kwa Yehova m’pemphero ndipo mukufuna kumutumikira mpaka kalekale.

Ngati mukuona kuti mwakonzeka kubatizidwa, amene amakuphunzitsani Baibulo angakonze zoti mukumane ndi akulu n’cholinga choti akuuzeni zoyenera kuchita.