PHUNZIRO 50

Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?​—Mbali Yachiwiri

Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?​—Mbali Yachiwiri

Ana ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo iye amafuna kuti makolo azisamalira bwino mphatso imeneyi. Yehova amapereka malangizo anzeru amene angathandize makolo kuti akwanitse kuchita zimenezi. Malangizo ake amathandizanso ana kudziwa zimene angachite kuti banja lizikhala losangalala.

1. Kodi Yehova amapereka malangizo otani kwa makolo?

Yehova amafuna kuti makolo azikonda ana awo ndiponso aziyesetsa kupeza nthawi yocheza nawo. Iye amafunanso kuti makolo aziteteza ana awo ku zinthu zoipa ndiponso azigwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo powaphunzitsa. (Miyambo 1:8) Iye amalangiza abambo kuti: “Muwalere [ana anu] ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake [ka Yehova].” (Werengani Aefeso 6:4.) Yehova amasangalala makolo akamagwiritsa ntchito malangizo ake polera ana awo komanso ngati sakupatsa anthu ena udindo wowalerera ana awo.

2. Kodi Yehova amapereka malangizo otani kwa ana?

Yehova amalangiza ana kuti: “Muzimvera makolo anu.” (Werengani Akolose 3:20.) Ana akamalemekeza komanso kumvera makolo awo, amasangalatsa Yehova ndiponso makolowo. (Miyambo 23:22-25) Ali mwana, Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. Ngakhale kuti anali wangwiro, iye ankamvera ndi kulemekeza makolo ake.​—Luka 2:51, 52.

3. Mungatani kuti nonse m’banja lanu mukhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu?

Ngati ndinu kholo, n’zosakayikitsa kuti mumafuna kuti ana anu azikonda Yehova ngati mmene inuyo mumachitira. Ndiye mungatani kuti zimenezi zitheke? Muzichita zimene Baibulo limanena. Paja limati: ‘Uzikhomereza [Mawu a Yehova] mwa ana ako. Uzilankhula nawo za mawuwo ukakhala pansi m’nyumba mwako ndi poyenda pamsewu.’ (Deuteronomo 6:7) Mawu akuti ‘kukhomereza’ amatanthauza kuphunzitsa munthu mfundo inayake mobwerezabwereza. Mwina mukafuna kuthandiza ana anu kuti asaiwale mfundo inayake, mumawauza mfundoyo mobwerezabwereza. Choncho mfundo yapalembali ndi yakuti, nthawi zonse muyenera kumapeza mpata wophunzitsa ana anu zokhudza Yehova. Mungachite bwino kwambiri mutamapeza mpata mlungu uliwonse n’kumaphunzira zokhudza Yehova monga banja. Ngati mulibe ana, kuphunzira Mawu a Mulungu mlungu uliwonse kungakuthandizeni kuti mukhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.

FUFUZANI MOZAMA

Onani mfundo zimene zingathandize kuti banja likhale lotetezeka komanso losangalala.

4. Muziphunzitsa ana anu mwachikondi

Kuphunzitsa mwana si ntchito yamasewera. Koma kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji? Werengani Yakobo 1:19, 20, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi makolo angasonyeze bwanji chikondi akamalankhula ndi ana awo?

  • N’chifukwa chiyani makolo akakwiya sayenera kulangiza ana awo pa nthawi imeneyo? a

5. Muziteteza ana anu

Kuti muteteze ana anu, mufunika kumafotokozera mwana wanu aliyense nkhani zokhudza kugonana. Mwina mungachite manyazi kukambirana ndi ana anu nkhani zimenezi. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • N’chifukwa chiyani makolo ena amavutika kukambirana ndi ana awo nkhani zokhudza kugonana?

  • Kodi makolo ena agwiritsa ntchito njira ziti pofotokozera ana awo nkhani zokhudza kugonana?

Baibulo linaneneratu kuti dziko la Satanali liziipiraipirabe. Werengani 2 Timoteyo 3:1, 13, kenako mukambirane funso ili:

  • Ena mwa anthu oipa amene atchulidwa muvesi 13 amachitira ana nkhanza zokhudza kugonana. Ndiye kodi n’chifukwa chiyani makolo afunika kuphunzitsa ana awo nkhani zokhudza kugonana komanso mmene angadzitetezere kwa anthu amene amachita nkhanza zimenezi?

Kodi mukudziwa?

A Mboni za Yehova amafalitsa mabuku ndi zinthu zina zothandiza makolo kuti aziphunzitsa ana awo nkhani zokhudza kugonana komanso kuti awateteze kwa anthu amene angafune kuwachitira nkhanza. Mwachitsanzo, onani:

6. Muzilemekeza makolo anu

Ana ndi achinyamata, angalemekeze makolo awo polankhula nawo mwaulemu. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

  • N’chifukwa chiyani mwana kapena wachinyamata ayenera kumalankhula mwaulemu ndi makolo ake?

  • Kodi wachinyamata angasonyeze bwanji kuti amalemekeza makolo ake akamalankhula nawo?

Werengani Miyambo 1:8, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi wachinyamata ayenera kuchita chiyani makolo ake akamamulangiza?

7. Muzipeza nthawi yophunzira Baibulo monga banja

Mabanja a Mboni za Yehova amayesetsa kupeza nthawi mlungu uliwonse kuti aphunzire limodzi Baibulo. Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite pa kulambira kwa pabanja? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi banja lingatani kuti lizichita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse?

  • Kodi kholo lingatani kuti kulambira kwa pabanja kuzikhala kosangalatsa komanso kothandiza?​—Onani chithunzi chomwe chili kumayambiriro kwa phunziroli.

  • N’chiyani chingachititse banja lanu kuti lizilephera kuphunzirira limodzi Mawu a Mulungu?

Kale ku Isiraeli, Yehova ankayembekezera kuti banja lililonse lizipeza nthawi yokambirana Malemba nthawi zonse. Werengani Deuteronomo 6:6, 7, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo yamulembali?

Zomwe mungachite pa kulambira kwa pabanja:

  • Kukonzekera misonkhano yampingo.

  • Kuwerenga komanso kukambirana nkhani ya m’Baibulo yomwe ingasangalatse banja lanu.

  • Ngati muli ndi ana aang’ono, pangani dawunilodi kapena kusindikiza zoti ana achite pa jw.org.

  • Ngati ana anu ndi achinyamata, kambiranani nawo nkhani yokhudza achinyamata ya pa jw.org.

  • Kuchita sewero la nkhani ya m’Baibulo ndi ana anu.

  • Kuonera ndi kukambirana vidiyo ya pa jw.org.

ZIMENE ENA AMANENA: “Baibulo ndi lovuta kwambiri moti ana sangalimvetse.”

  • Kodi mungayankhe bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yehova amafuna kuti makolo azikonda ana awo, kuwaphunzitsa komanso kuwateteza. Iye amafuna kuti ana azilemekeza ndi kumvera makolo awo ndiponso kuti banja lonse lizimulambira mogwirizana.

Kubwereza

  • Kodi makolo angatani kuti aphunzitse komanso kuteteza ana awo?

  • Kodi ana angasonyeze bwanji kuti amalemekeza makolo awo?

  • Kodi banja lingapindule bwanji likamapeza nthawi yolambira limodzi mlungu uliwonse?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani malangizo omwe Baibulo limapereka kwa anthu omwe amasamalira achikulire.

“Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yosamalira Makolo Achikulire?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani chimene chinathandiza bambo yemwe sankadziwa mmene angalerere ana kuti akhale bambo wabwino.

Yehova Anandiphunzitsa Kulera Bwino Ana (5:58)

a M’Baibulo, mawu akuti “malangizo” amatanthauza kuphunzitsa, kutsogolera komanso kuthandiza munthu kuti asinthe. Koma satanthauza kuzunza kapena kuchitira munthu nkhanza.​—Miyambo 4:1.