PHUNZIRO 51

Mungatani Kuti Zimene Mumalankhula Zizisangalatsa Yehova?

Mungatani Kuti Zimene Mumalankhula Zizisangalatsa Yehova?

Yehova anatilenga m’njira yakuti tizitha kulankhula ndipo imeneyi ndi mphatso yapadera. Kodi zimamukhudza akamaona mmene timagwiritsira ntchito mphatsoyi? Inde. (Werengani Yakobo 1:​26.) Ndiye kodi tingatani kuti zolankhula zathu zizisangalatsa Yehova?

1. Kodi tizigwiritsa ntchito bwanji mphatso ya kulankhula?

Baibulo limatiuza kuti ‘tipitirize kutonthozana ndi kulimbikitsana.’ (1 Atesalonika 5:11) Kodi mukuona kuti pali anthu ena amene mukufunika kuwalimbikitsa? Ndiye mungatani kuti muwalimbikitse? Muziwatsimikizira kuti ndi ofunika kwambiri. Mwinanso mungawauze makhalidwe abwino omwe ali nawo amene amakusangalatsani. Kodi mungaganizire lemba linalake lomwe mungalimbikitse nalo munthu wina? Pali malemba ambiri ndipo mungathe kusankha limodzi n’kuligwiritsa ntchito. Musaiwalenso kuti mungathe kulimbikitsa munthu chifukwa cha mawu amene mwasankha kuwagwiritsa ntchito komanso mmene mwawalankhulira. Choncho nthawi zonse muzilankhula mokoma mtima komanso modekha.​—Miyambo 15:1.

2. Kodi tiyenera kupewa kulankhula zinthu zotani?

Baibulo limati: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu.” (Werengani Aefeso 4:29.) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kupewa kulankhula mawu otukwana kapena achipongwe, ndiponso tisamanene zinthu n’cholinga chofuna kupsetsa mtima munthu wina. Tizipewanso miseche komanso kunena zinthu zoipa zokhudza anthu ena.​—Werengani Miyambo 16:28.

3. N’chiyani chimene chingatithandize kuti tizilankhula zinthu zolimbikitsa?

Nthawi zambiri zinthu zimene timalankhula zimasonyeza zimene zili mumtima mwathu kapenanso zimene tikuganiza. (Luka 6:​45) Choncho tiziyesetsa kudziphunzitsa kuti tiziganizira zinthu zabwino zomwe ndi zolungama, zoyera, zachikondi ndi zoyamikirika. (Afilipi 4:8) Kuti zimenezi zitheke, tizisamala posankha zosangalatsa komanso anthu ocheza nawo. (Miyambo 13:20) Tingachitenso bwino kumaganizira kaye zomwe tikufuna kulankhula tisanazilankhule. Tiziganiziranso mmene zonena zathuzo zingakhudzire anthu ena. Baibulo limati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.”​—Miyambo 12:18.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zimene mungachite kuti muzilankhula zinthu zomwe zingasangalatse Yehova ndi kulimbikitsa anthu ena.

4. Muzisamala ndi zimene mumalankhula

Tonsefe nthawi zina timalankhula zinthu zimene timadzanong’oneza nazo bondo pambuyo pake. (Yakobo 3:2) Werengani Agalatiya 5:22, 23, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi makhalidwe ati n’cholinga choti muzisamala ndi zimene mumalankhula? Kodi makhalidwe amenewa angakuthandizeni bwanji?

Werengani 1 Akorinto 15:33, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi anzanu ndiponso zosangalatsa zomwe mumasankha zingakhudze bwanji mmene mumalankhulira?

Werengani Mlaliki 3:1, 7, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi ndi pa nthawi iti imene muyenera kukhala chete kapena kudikira kaye nthawi yabwino yoti mulankhule?

5. Muzilankhula zinthu zabwino zokhudza ena

Kodi tingapewe bwanji kulankhula mawu omwe angakhumudwitse anthu ena? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

  • N’chifukwa chiyani m’bale wamuvidiyoyi ankafunika kusintha mmene amalankhulira zokhudza anthu ena?

  • Nanga anachita chiyani kuti asinthe?

Werengani Mlaliki 7:16, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi tizikumbukira mfundo iti kuti tipewe kulankhula zinthu zoipa zokhudza munthu winawake?

Werengani Mlaliki 7:21, 22, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mavesiwa angakuthandizeni bwanji kuti musamafulumire kupsa mtima munthu wina akalankhula zoipa zokhudza inuyo?

6. Muzilankhula bwino ndi anthu am’banja lanu

Yehova amafuna kuti tizilankhula mwachikondi komanso mokoma mtima ndi anthu am’banja lathu. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

  • N’chiyani chingakuthandizeni kuti muzilankhulana mokoma mtima m’banja lanu?

Werengani Aefeso 4:31, 32, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi tizilankhula mawu otani kwa anthu am’banja lathu kuti azimva kuti timawakonda?

Yehova anafotokoza mmene amakondera Mwana wake Yesu. Werengani Mateyu 17:5, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mungatsanzire bwanji Yehova polankhula ndi anthu am’banja lanu?

Muzichita chidwi ndi zimene ena amachita n’kumawayamikira

ZIMENE ENA AMANENA: “Ine ndimalankhula zimene zabwera m’mutu mwanga. Ndiye kaya anthu akhumudwa, izo n’zawo.”

  • Kodi inunso mumaona choncho? N’chifukwa chiyani mukutero?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Zimene timalankhula zingakhumudwitse kapena kulimbikitsa anthu ena. Choncho tiyenera kusamala ndi zimene timalankhula, mmene timazilankhulira komanso nthawi imene tingalankhule.

Kubwereza

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite kuti muzilimbikitsa ena ndi zimene mumalankhula?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene mukufuna kupewa kumazilankhula?

  • Kodi n’chiyani chingatithandize kuti nthawi zonse tizilankhula zinthu zabwino komanso zolimbikitsa?

Zolinga

ONANI ZINANSO

N’chiyani chingatithandize kuti tizilankhula zinthu zanzeru?

Khalani Ndi Lilime la Anthu Anzeru 8:04

Onani zimene mungachite kuti mupewe miseche.

Kodi Ndingatani Kuti Ndithetse Miseche? 2:36