PHUNZIRO 53

Muzisankha Zosangalatsa Zomwe Sizingakhumudwitse Yehova

Muzisankha Zosangalatsa Zomwe Sizingakhumudwitse Yehova

Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Iye amafuna kuti tizikhala moyo wosangalala ndipo amasangalala tikamapeza nthawi yopuma pambuyo pogwira ntchito. M’phunziroli tiona zomwe tingachite kuti tizigwiritsa ntchito nthawi yathu yopuma m’njira yoti tizisangalala n’kumasangalatsanso Yehova.

1. Kodi tiziganizira zinthu ziti tikamasankha zosangalatsa?

Kodi inuyo mumakonda kuchita chiyani pa nthawi yopuma? Anthu ena amakonda kungokhala panyumba n’kumawerenga mabuku, kumvetsera nyimbo, kuonera mafilimu kapena kufufuza zinthu pa intaneti. Pomwe ena amakonda kupita kukawongola miyendo ndi anzawo, kukasambira, kukasewera mpira kapena kuchita masewera ena. Kaya tasankha kuchita zotani, nthawi zonse tizitsimikizira kuti zosangalatsa zomwe tasankhazo ndi ‘zovomerezeka kwa Ambuye.’ (Aefeso 5:10) Choncho, ndi bwino kuganizira mfundo imeneyi chifukwa masiku ano anthu ambiri amakonda zosangalatsa zimene Yehova amadana nazo monga zachiwawa, zachiwerewere kapenanso zamizimu. (Werengani Salimo 11:5.) Ndiye kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tizisankha zosangalatsa mwanzeru?

Tikamakonda kucheza ndi anthu amene amakonda Yehova, nafenso tingatengere makhalidwe awo abwino ndiponso tingamasankhe zosangalatsa zabwino. Monga mmene tinaonera m’phunziro 48, “munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.” Komabe ngati timakonda kucheza ndi anthu amene sagwiritsa ntchito mfundo za Mulungu pa moyo wawo ‘tidzapeza mavuto.’​​​—Miyambo 13:20.

2. N’chifukwa chiyani tifunika kusamala kuti tisamangokhalira kuchita zosangalatsa?

Ngakhale titasankha zosangalatsa zimene sizingakhumudwitse Yehova, tifunika kusamala kuti tisamangokhalira kuchita zosangalatsazo. Zili choncho chifukwa chakuti kupanda kusamala tingalephere kupeza nthawi yochitira zinthu zofunika kwambiri. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu.’​—Werengani Aefeso 5:15, 16.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zimene zingakuthandizeni kuti muzisankha zosangalatsa mwanzeru.

3. Muzipewa zosangalatsa zoipa

N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha zosangalatsa? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi masewera amene ankachitika kale ku Roma amafanana bwanji ndi zosangalatsa zina zimene anthu amachita masiku ano?

  • Muvidiyoyi, kodi Danny anaphunzira zotani zokhudza zosangalatsa?

Werengani Aroma 12:9, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi vesili lingakuthandizeni bwanji posankha zosangalatsa?

Kodi ndi zinthu zina ziti zimene Yehova amadana nazo? Werengani Miyambo 6:16, 17 ndi Agalatiya 5:19-21. Pambuyo powerenga lemba lililonse mukambirane funso ili:

  • Kodi m’mavesiwa mwatchulidwa zinthu ziti zomwe zimapezeka kwambiri m’zosangalatsa zimene anthu amakonda masiku ano?

 Zimene mungachite kuti muzisankha zosangalatsa mwanzeru

Muzidzifunsa kuti:

  • Kodi zosangalatsazi zikuphatikizapo zinthu zimene Yehova amadana nazo?

  • Kodi zindilepheretsa kuchita zinthu zofunika kwambiri?

  • Kodi zichititsa kuti ndizigwirizana kwambiri ndi anthu amene sakonda Yehova?

Tiyenera kuyesetsa kupewa chilichonse chimene chingatigwetsere m’mavuto. Choncho ngati pali zosangalatsa zina zimene tikuzikayikira, ndi bwino kungozipeweratu

4. Muzigwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru

Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:

  • Ngakhale kuti m’bale wamuvidiyoyi sankaonera zinthu zoipa, kodi vuto lake linali lotani?

Werengani Afilipi 1:10, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi vesili lingatithandize bwanji kupewa kuthera nthawi yaitali pa zinthu zosangalatsa?

5. Muzisankha zosangalatsa zabwino

Ngakhale kuti pali zosangalatsa zina zimene Yehova sasangalala nazo, pali zambiri zomwe sizingamukhumudwitse. Werengani Mlaliki 8:15 ndi Afilipi 4:8, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi ndi zosangalatsa zabwino ziti zimene inuyo mumakonda?

Pali zosangalatsa zabwino zambiri zimene mungamachite

ZIMENE ENA AMANENA: “Sindikuona vuto lililonse ndi zosangalatsa monga zachiwawa, zachiwerewere kapenanso zamizimu. Ubwino wake siine amene ndimazichita.”

  • Kodi inuyo mukuona bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yehova amafuna kuti tizisankha zosangalatsa zabwino.

Kubwereza

  • Kodi Akhristu ayenera kupewa zosangalatsa zotani?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuthera nthawi yambiri pa zosangalatsa?

  • N’chifukwa chiyani mukufuna kusankha zosangalatsa zimene sizingakhumudwitse Yehova?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Kodi ndani ali ndi udindo wotisankhira zosangalatsa? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe yankho lake.

“Kodi Muli ndi Lamulo Loletsa Mavidiyo Ena, Mabuku Ena Ndiponso Nyimbo Zina?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani zimene zinathandiza mayi wina kuti asankhe zinthu mwanzeru pa nkhani ya zosangalatsa zokhudzana ndi zamizimu.

Muzipewa Zosangalatsa Zokhudzana Ndi Zamizimu 2:02