PHUNZIRO 56

Pitirizani Kuchita Zinthu Mogwirizana Mumpingo

Pitirizani Kuchita Zinthu Mogwirizana Mumpingo

Tikakhala ndi Akhristu anzathu timamva ngati Mfumu Davide yemwe anati: “Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana.” (Salimo 133:1) Komatu mgwirizanowu sumangobwera wokha. Tonsefe tiyenera kumachita khama kuti tipitirize kugwirizana ndi abale athu.

1. Kodi anthu a Yehova amachita zinthu ziti zomwe zimakuchititsani chidwi?

Mukapita kudziko lina n’kupezeka pamisonkhano abale ndi alongo amakulandirani ndi manja awiri, amakusonyezani chikondi komanso mumakhala omasuka ngakhale kuti simumva chinenero chawo. Zili choncho chifukwa chakuti zinthu zomwe timagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo n’zofanana kulikonse. Kuwonjezera pamenepa, timayesetsa kusonyezana chikondi. Kaya timakhala kuti, tonsefe ‘timaitanira pa dzina la Yehova ndi kumutumikira mogwirizana.’​​—Zefaniya 3:9.

2. Kodi mungathandize bwanji kuti mumpingo mupitirize kukhala mgwirizano?

Baibulo limati: “Kondanani kwambiri kuchokera mumtima.” (1 Petulo 1:22) Kodi inuyo mungagwiritse ntchito bwanji malangizo amenewa? M’malo momangoona zimene anthu ena amalakwitsa, muziganizira kwambiri makhalidwe awo abwino. Musamangocheza ndi anthu okhawo amene amakonda zimene inuyo mumakonda. M’malomwake muziyesetsa kudziwana ndi abale ndi alongo osiyanasiyana. Ngati tili ndi kamtima ka tsankho tiyenera kuyesetsa kukathetsa. ​​​—Werengani 1 Petulo 2:17. a

3. Kodi muyenera kuchita chiyani mukasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzanu?

Ngakhale kuti ndife anthu ogwirizana, timasemphana maganizo kapena kukhumudwitsana chifukwa chakuti ndife anthu ochimwa. Choncho, Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Pitirizani . . . kukhululukirana ndi mtima wonse . . . monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.” (Werengani Akolose 3:13.) Anthufe timakhumudwitsa Yehova kambirimbiri komabe iye amatikhululukira. Choncho iye amafuna kuti nafenso tizikhululukira abale ndi alongo athu. Mukazindikira kuti mwakhumudwitsa winawake, inuyo muziyesetsa kukambirana ndi mnzanuyo n’cholinga choti muthetse kusamvana.​—Werengani Mateyu 5:23, 24 b

FUFUZANI MOZAMA

Ganizirani zimene mungachite pothandiza kuti mumpingo mupitirize kukhala mgwirizano ndi mtendere.

Kodi mungachite zotani kuti mukhazikitse mtendere?

4. Yesetsani kuthetsa mtima watsankho

Tonsefe timafuna kumakonda abale ndi alongo athu onse. Komabe tingavutike kugwirizana ndi munthu yemwe amaoneka wosiyana ndi ife. Ndiye n’chiyani chimene chingatithandize? Werengani Machitidwe 10:​34, 35, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Yehova amalandira anthu amitundu yonse kuti akhale Mboni zake. Ndiye kodi mungatengere bwanji chitsanzo cha Yehova pa nkhani ya mmene mumaonera anthu omwe ndi osiyana ndi inu?

  • Kodi inuyo mukufuna kupewa zinthu ziti zomwe anthu ambiri m’dera lanu amachita posonyeza tsankho?

Werengani 2 Akorinto 6:​11-13, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mukuganiza kuti muyenera kuchita chiyani kuti muzikonda kwambiri abale ndi alongo omwe mumasiyana nawo zinthu zina?

5. Muzikhululuka ndi mtima wonse komanso muziyesetsa kukhazikitsa mtendere

Yehova amatikhululukira ndi mtima wonse ngakhale kuti iyeyo satilakwira. Werengani Salimo 86:​5, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi vesili likutiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova pa nkhani yokhululuka?

  • Kodi mumathokoza Yehova chifukwa chakuti amatikhululukira? N’chifukwa chiyani mukutero?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kukhala mwamtendere ndi anzathu?

Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yokhululuka n’kumachitabe zinthu mogwirizana ndi abale ndi alongo athu? Werengani Miyambo 19:​11, kenako mukambirane funso ili:

  • Munthu wina akakukhumudwitsani kapena kukuputani, kodi muyenera kuchita chiyani kuti mukhalebe naye pamtendere?

Nthawi zina nafenso timakhumudwitsa ena. Ndiye tizitani zimenezi zikachitika? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

  • Kodi mlongo wamuvidiyoyi anachita zotani kuti akhazikitse mtendere?

6. Muziona zabwino mwa abale ndi alongo anu

Tikayamba kudziwana bwino ndi abale ndi alongo athu m’pamene timayamba kuona makhalidwe awo abwino komanso zimene amalakwitsa. Ndiye tingatani kuti tiziganizira kwambiri makhalidwe awo abwino? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

  • Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muziona zabwino mwa abale ndi alongo anu?

Yehova amaona kwambiri makhalidwe athu abwino. Werengani 2 Mbiri 16:9a, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mukumva bwanji podziwa kuti Yehova amaona kwambiri makhalidwe abwino omwe muli nawo?

Ngakhale mphete yodula itakandika, imakhalabe yamtengo wapatali. N’chimodzimodzinso ndi abale ndi alongo athu, ngakhale kuti si angwiro, Yehova amawaonabe kuti ndi amtengo wapatali

ZIMENE ENA AMANENA: “Ndimukhululukira pokhapokha andipepese kaye.”

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kumakhululukira ena ndi mtima wonse?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Mungathandize kuti mpingo upitirizebe kuchita zinthu mogwirizana mukamakhululuka komanso mukamayesetsa kukonda abale ndi alongo anu onse.

Kubwereza

  • Kodi mungathetse bwanji mtima watsankho?

  • Mukasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzanu, kodi muyenera kuchita chiyani?

  • Kodi inuyo mukufuna kutsanzira Yehova pa nkhani yokhululukira ena? N’chifukwa chiyani mukutero?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani mmene fanizo lina limene Yesu ananena lingatithandizire kuti tizipewa kuweruza anthu ena.

Chotsa Mtanda wa Denga M’diso Lako (6:56)

Onani chimene chinathandiza anthu awiri kuti ayambe kukondana kwambiri ngakhale kuti anakulira m’dziko limene anthu ambiri ankadana chifukwa chosankhana mitundu.

Johny ndi Gideon: Poyamba Anali Khoswe ndi Mphaka Koma Pano Ndi Ogwirizana (6:42)

a Mawu Akumapeto 6 akufotokoza mmene chikondi chimathandizira Akhristu kupewa kufalitsa matenda opatsirana.

b Mawu Akumapeto 7 akufotokoza zimene mungachite kuti muthetse kusamvana pa nkhani zokhudza bizinesi ndiponso malamulo.