PHUNZIRO 57

Kodi Mukachita Tchimo Lalikulu Muyenera Kutani?

Kodi Mukachita Tchimo Lalikulu Muyenera Kutani?

Ngakhale kuti mumakonda kwambiri Yehova ndiponso mumayesetsa kupewa kuchita zinthu zomwe zingamukhumudwitse, nthawi zina mukhoza kulakwitsa zinazake. Komabe machimo ena amakhala aakulu kuposa ena. (1 Akorinto 6:​9, 10) Ngati mwachita tchimo lalikulu musataye mtima ndipo musaiwale kuti Yehova sanasiye kukukondani. Iye ndi wofunitsitsa kukukhululukirani komanso kukuthandizani kuti musinthe.

1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atikhululukire?

Anthu amene amakonda Yehova amadzimvera chisoni kwambiri akazindikira kuti achita tchimo lalikulu. Komabe Yehova amawatonthoza ndi lonjezo lakuti: “Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.” (Yesaya 1:18) Tikalapa mochokera pansi pa mtima, Yehova sakumbukiranso machimo athu ndipo amatikhululukira ndi mtima wonse. Ndiye timasonyeza bwanji kuti talapa? Timadzimvera chisoni kwambiri chifukwa cha zimene tachitazo, sitimazibwerezanso, kenako timapempha Yehova kuti atikhululukire. Komanso timachita khama kuti tisiye kuchita kapena kuganizira zinthu zoipa zimene zinachititsa kuti tichite tchimo. Kuonjezera pamenepa, timayesetsa kutsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino pa moyo wathu.​—Werengani Yesaya 55:6, 7.

2. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji akulu kuti atithandize tikachimwa?

Tikachita tchimo lalikulu Yehova amatiuza kuti ‘tiitane akulu a mpingo.’ (Werengani Yakobo 5:14, 15.) Akuluwa amakonda Yehova ndi nkhosa zake. Iwo anaphunzitsidwa bwino mmene angatithandizire n’cholinga choti tikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.​—Agalatiya 6:1.

Kodi akulu amatithandiza bwanji tikachita tchimo lalikulu? Akulu awiri kapena atatu amagwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba potithandiza kuzindikira kuti zomwe tachitazo ndi zolakwika. Iwo amatipatsa malangizo ndi kutilimbikitsa n’cholinga chotithandiza kuti tipewe kudzachitanso tchimolo. Iwo angatiuze kuti tisamachitenso zinthu zina mumpingo kwa kanthawi mpaka pamene ubwenzi wathu ndi Yehova wayambiranso kukhala wolimba. Pofuna kuteteza mpingo kuti ukhalebe woyera, akulu amachotsa mumpingo munthu yemwe wachita tchimo lalikulu koma sanasonyeze mtima wolapa.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zimene mungachite kuti muziyamikira zimene Yehova amachita potithandiza tikachita tchimo lalikulu.

3. Kuulula machimo athu kumatithandiza kuti tikhalenso pa ubwenzi ndi Yehova

Tikachita tchimo lililonse Yehova amakhumudwa. Choncho tingachite bwino kuulula kwa iyeyo. Werengani Salimo 32:1-5, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kuulula machimo athu kwa Yehova m’malo momubisira?

Tikaulula machimo athu kwa Yehova tiyeneranso kuuza akulu ndipo kuchita zimenezi kumathandiza kuti zinthu ziyambirenso kutiyendera bwino. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

  • Muvidiyoyi, kodi akulu anathandiza bwanji Canon kuti abwerere kwa Yehova?

Tizimasuka pofotokozera akulu za tchimo lathu ndipo tiziwauza zoona zokhazokha. Iwo amafuna kutithandiza. Werengani Yakobo 5:16, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani akulu savutika kutithandiza tikawauza zoona zokhazokha zokhudza tchimo lathu?

Muziulula machimo anu kwa Yehova, muziuza akulu zoona zokhazokha komanso muzivomereza chilango chochokera kwa Yehova chomwe amachipereka mwachikondi

4. Kodi kuchotsa munthu wosalapa mumpingo kuli ndi ubwino wotani?

Ngati munthu amene wachita tchimo lalikulu sakufuna kulapa komanso kutsatira mfundo za m’Malemba sayeneranso kukhala mumpingo. Zikatere amachotsedwa mumpingo ndipo sitiyenera kumacheza naye kapena kulankhula naye. Werengani 1 Akorinto 5:6, 11 ndi 2 Yohane 9-11, kenako mukambirane funso ili:

  • Monga mmene chofufumitsa chimafufumitsira mtanda wonse, kodi kucheza ndi munthu wochimwa yemwe sanalape kungakhudze bwanji mpingo wonse?

Anthu ambiri omwe anachotsedwa mumpingo anabwerera chifukwa cha chilango chomwe anapatsidwa. Ngakhale kuti chilangocho chinali chopweteka, chinawathandiza kuzindikira kuti zomwe anachita zinali zolakwika. (Salimo 141:5) Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

  • Muvidiyoyi, kodi kuchotsedwa mumpingo kunathandiza bwanji Sonia?

Kodi kuchotsa munthu wosalapa mumpingo . . .

  • kumalemekeza bwanji dzina la Yehova?

  • kumasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wachilungamo ndiponso wachikondi?

5. Yehova amakhululukira munthu amene walapa

Yesu anagwiritsa ntchito fanizo lomwe limatithandiza kumvetsa mmene Yehova amamvera munthu wochimwa akalapa. Werengani Luka 15:1-7, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi fanizoli likukuphunzitsani chiyani zokhudza Yehova?

Werengani Ezekieli 33:​11, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi munthu ayenera kuchita chiyani posonyeza kuti walapadi?

Mofanana ndi m’busa, Yehova amasamalira mwachikondi nkhosa zake

ZIMENE ENA AMANENA: “Ndikuopa kuti ndikaulula tchimo langa kwa akulu andichotsa mumpingo.”

  • Kodi munthu amene ali ndi maganizo amenewa mungamuuze zotani?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Ngati munthu wachita tchimo lalikulu n’kulapa mochokera pansi pa mtima komanso watsimikiza mtima kuti sadzachitanso tchimolo, Yehova amamukhululukira.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kuulula machimo athu kwa Yehova?

  • Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atikhululukire machimo athu?

  • Ngati tachita tchimo lalikulu, n’chifukwa chiyani tiyenera kupempha akulu kuti atithandize?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani mmene Yehova anasonyezera munthu wina chifundo chotchulidwa pa Yesaya 1:18.

Musamakayikire Kuti Yehova ndi Wachifundo (5:02)

Onani mmene mungafotokozere munthu yemwe si Mboni chifukwa chake nthawi zina munthu amachotsedwa mumpingo.

“Kodi Mumapewa Anthu Amene Kale Anali M’chipembedzo Chanu?” (Nkhani yapawebusaiti)