PHUNZIRO 58

Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Yehova

Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Yehova

Akhristu oona salola kuti munthu kapena chinthu chilichonse chiwalepheretse kulambira Yehova. Sitikukayikira kuti nanunso mumaona choncho. Yehova amasangalala kwambiri akamaona kuti mukupitiriza kukhala okhulupirika kwa iye. (Werengani 1 Mbiri 28:9.) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingakulepheretseni kukhala wokhulupirika kwa Yehova? Nanga n’chiyani chingakuthandizeni kuti musasiye kukhala wokhulupirika kwa Yehova?

1. Kodi anthu ena angachititse bwanji kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova?

Anthu ena amafuna titasiya kutumikira Yehova. Kodi anthu amenewa angakhale ndani? Anthu ena amene anasiya kutumikira Yehova amanena mabodza okhudza gulu la Mulungu n’cholinga choti ifenso tisiye kutumikira Yehova. Anthu amenewa amatchedwa ampatuko. Komanso atsogoleri achipembedzo ena amafalitsa mabodza n’cholinga chofuna kusokoneza anthu omwe amangotengeka ndi zilizonse kuti asiye kutumikira Yehova. Tiyenera kupeweratu kutsutsana ndi anthu ampatuko, kuwerenga mabuku awo kapena zimene amalemba pa intaneti, kutsegula mawebusaiti awo kapenanso kuonera mavidiyo awo. Ponena za anthu amene amachititsa ena kuti asiye kutumikira Yehova mokhulupirika, Yesu anati: “Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu. Chotero ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera m’dzenje.”​—Mateyu 15:14.

Nanga mungatani ngati munthu wina yemwe mumamudziwa wanena kuti sakufunanso kukhala wa Mboni za Yehova? Zimakhala zopweteka kwambiri ngati munthu yemwe timamukonda wasankha kuchita zimenezi. N’kuthekanso kuti angatikakamize kuti tisankhe pakati pa iyeyo ndi Yehova. Zikatere, tiyenera kutsimikiza mtima kuti tikhalabe okhulupirika kwa Yehova kuposa wina aliyense. (Mateyu 10:37) Choncho tiyenera kumvera lamulo la Yehova lakuti tisamagwirizane ndi anthu oterowo.​—Werengani 1 Akorinto 5:11.

2. Kodi zimene timasankha pa moyo wathu zingachititse bwanji kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova?

Ngati timakonda Yehova tidzapewa kuchita chilichonse chokhudzana ndi chipembedzo chonyenga. Tidzapewa kukhala kapena kugwira ntchito m’gulu linalake lachipembedzo kapenanso kuchita chilichonse chokhudzana ndi chipembedzo chonyenga. Yehova amatichenjeza kuti: “Tulukani [mu Babulo Wamkulu] anthu anga.”​​—Chivumbulutso 18:2, 4.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zimene mungachite kuti aliyense asakulepheretseni kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Muonanso mmene mungasonyezere kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova potuluka mu Babulo Wamkulu.

3. Samalani ndi aphunzitsi abodza

Kodi tiyenera kutani tikamva ena akunena zinthu zoipa zokhudza gulu la Yehova? Werengani Miyambo 14:15, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kuti tisamangokhulupirira zilizonse zomwe tamva?

Werengani 2 Yohane 10, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Malinga ndi lembali, kodi tizitani ndi anthu ampatuko?

  • Ngakhale kuti sitingacheze mwachindunji ndi anthu ampatuko, kodi tingasokonezedwe bwanji ndi zimene amaphunzitsa?

  • Kodi mukuganiza kuti Yehova angamve bwanji tikamamvetsera zinthu zabodza zokhudza iyeyo kapenanso gulu lake?

4. Muzikhalabe okhulupirika kwa Mulungu munthu wina akachita tchimo

Kodi tiyenera kuchita chiyani tikadziwa kuti munthu wina mumpingo wachita tchimo lalikulu? Onani mfundo yomwe ikupezeka mulamulo lomwe Mulungu anapereka kwa Aisiraeli. Werengani Levitiko 5:1.

Mogwirizana ndi vesili, tikadziwa kuti munthu wina wachita tchimo lalikulu, tiyenera kuuza akulu zomwe tikudziwa pa nkhaniyo. Komabe tisanachite zimenezi, tiyenera kuuza munthu wochimwayo kuti akaulule yekha kwa akulu za tchimo lakelo. Ndiyeno akakanika kuchita zimenezi, ifeyo tiyenera kusonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova pokanena kwa akulu. Kodi tikachita zimenezi timasonyeza bwanji kuti tili ndi chikondi chokhulupirika kwa . . .

  • Yehova Mulungu?

  • munthu yemwe wachimwayo?

  • anthu ena onse mumpingo?

Ngati Mkhristu mnzanu wachita zoipa, muyenera kumuthandiza

5. Tulukani mu Babulo Wamkulu

Werengani Luka 4:8 ndi Chivumbulutso 18:4, 5, kenako muyankhe mafunso awa:

  • Kodi sindinafufutitse dzina langa kuchipembedzo chonyenga?

  • Kodi ndili m’bungwe lomwe limachita zinthu zogwirizana ndi chipembedzo chinachake?

  • Kodi ntchito yomwe ndimagwira imathandizira zochita za chipembedzo chonyenga?

  • Kodi pali zinthu zinanso zomwe ndingachite kuti ndisiyiretu kuchita zinthu zogwirizana ndi chipembedzo chonyenga?

  • Ngati funso linalake ndaliyankha kuti inde, kodi ndiyenera kusintha zinthu ziti?

Pa zinthu zonse zomwe takambiranazi muzionetsetsa kuti zomwe mungasankhe zizikuthandizani kukhala ndi chikumbumtima choyera komanso zizisonyeza kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova.

Kodi mungatani mutapemphedwa kuti mupereke ndalama zothandizira pa ntchito zachifundo za chipembedzo chinachake?

ZIMENE ENA AMANENA: “Ndikufunika kudziwa zimene ampatuko amanena zokhudza Mboni za Yehova kuti nditeteze choonadi.”

  • Kodi mukuona kuti ndi nzeru kuchita zimenezi? N’chifukwa chiyani mukutero?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Kuti tipitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova tiyenera kupewa kugwirizana ndi anthu amene ndi osakhulupirika kwa iye. Tiyeneranso kupewa kuchita chilichonse chogwirizana ndi chipembedzo chonyenga.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kuonera, kuwerenga kapenanso kumvetsera zimene ampatuko amaphunzitsa?

  • Kodi tiyenera kuchita bwanji zinthu ndi anthu amene asankha kuti asakhalenso a Mboni za Yehova?

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikumvera chenjezo lakuti tituluke m’chipembedzo chonyenga?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani zimene muyenera kuchita anthu ena akamanena zinthu zabodza zokhudza Mboni za Yehova.

“Kodi Mukudziwa Nkhani Yonse?” (Nsanja ya Olonda, August 2018)

Kodi mungadziwe bwanji kuti mabungwe kapena zinthu zinazake zikugwirizana ndi Babulo Wamkulu?

“Tizitumikira Yehova Mwakhama Kumapeto kwa ‘Masiku Otsirizawa’” (Nsanja ya Olonda, October 2019, ndime 16-18)

Kodi ndi zinthu ziti zimene anthu ena otsutsa achita pofuna kufooketsa chikhulupiriro chathu?

Samalani Ndi Anthu Achinyengo (9:32)