Zimene mungachite kuti muzipindula pophunzira Baibulo

Zimene mungachite kuti muzipindula pophunzira Baibulo

Choyamba kambiranani zimene zili patsamba 2 ndi 3, kenako onerani VIDIYO.

MBALI YOYAMBA

Kuti mukonzekere phunziro lililonse, muziwerenga mbali yoyamba. Cholinga cha mafunso (A) komanso malemba (B)  ndi kutsindika mfundo zikuluzikulu. Malemba amene alembedwa kuti “werengani” muziwawerenga mokweza mukamaphunzira ndi mphunzitsi wanu.

MBALI YAPAKATI

Mawu oyamba (C) omwe ali pansi pa kamutu kakuti Fufuzani Mozama akufotokoza mfundo zomwe mutakambirane. Mitu ing’onoing’ono  (D) ikufotokozera mfundo zazikulu zomwe zili m’phunziro lililonse. Werengani malemba, yankhani mafunso ndi kuonera mavidiyo limodzi ndi mphunzitsi wanu.

MAVIDIYO ndi ZINTHU ZONGOMVETSERA zikuthandizani kumvetsa bwino mfundo zimene mukuphunzira. Mavidiyo ena akusonyeza zochitika zenizeni. Pomwe mavidiyo ena ndi masewero osonyeza zinthu zimene zimachitikadi pa moyo wathu.

Onetsetsani zithunzi ndi mawu ake (E), ndipo ganizirani mmene mungayankhire Zimene Ena Amanena (F).

MBALI YOMALIZA

Malizani phunziro lililonse pokambirana mbali ya Zomwe Taphunzira komanso Kubwereza (G). Lembani tsiku limene mwamaliza phunziro. Mbali yakuti Zolinga (H) ili ndi zoti muchite kuti mupitirizebe kuphunzira kapenanso mugwiritse ntchito zomwe mwaphunzira. Pansi pa mutu wakuti Onani Zinanso (I) pali zinthu zina zomwe mungakonde kuwerenga kapenanso kuonera.

Mmene mungapezere malemba m’Baibulo

M’Baibulo muli mabuku ang’onoang’ono okwana 66. Linagawidwa mbali ziwiri: Malemba Achiheberi ndi Chiaramu (“Chipangano Chakale”) ndiponso Malemba Achigiriki (“Chipangano Chatsopano”).

Malemba omwe ali m’bukuli akuyamba ndi dzina la buku la m’Baibulo (A), chaputala (B), kenako vesi kapena mavesi (C).

Mwachitsanzo, Yohane 17:3 akutanthauza buku la Yohane, chaputala 17 vesi 3.