Kodi N’zotheka Kukhala Ndi Moyo Mpaka Kalekale?

Kodi N’zotheka Kukhala Ndi Moyo Mpaka Kalekale?

Kodi mungayankhe kuti . . .

  • inde?

  • ayi?

  • mwina?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—SALIMO 37:29.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

M’tsogolomu mudzakhala ndi moyo wosangalala komanso wamtendere limodzi ndi banja lanu ndiponso anzanu.YEREMIYA 29:11.

Mudzasangalala ndi moyo osati kwa nthawi yochepa koma kwamuyaya.​SALIMO 22:26.

KODI TIYENERA KUKHULUPIRIRA BAIBULO?

Inde. Kuti mudziwe chifukwa chake onani maumboni omwe akupezeka m’maphunziro atatu amene ali m’kabukuka. Mitu yake ndi iyi: