PHUNZIRO 02

Baibulo Limatithandiza Kukhala Ndi Chiyembekezo

Baibulo Limatithandiza Kukhala Ndi Chiyembekezo

Anthu padziko lonse amakumana ndi mavuto amene amawachititsa kukhumudwa, kuda nkhawa komanso kumva kupweteka. Kodi inunso munakumanapo ndi vuto limene linakuchititsani kumva chonchi? Mwina panopa mukudwala kapena munthu amene mumamukonda anamwalira. Mwina mukudzifunsa kuti, ‘Koma zinthu zidzakhalanso bwino?’ Baibulo limayankha mogwira mtima funso limeneli.

1. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kukhala ndi chiyembekezo?

Baibulo silimangofotokoza chifukwa chake padzikoli pali mavuto ochuluka chonchi, koma limatiuzanso uthenga wabwino wakuti posachedwapa mavuto onsewa adzatha. Zimene Baibulo limalonjeza zingatithandize kukhala ndi “chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino.” (Werengani Yeremiya 29:11, 12.) Zimenezi zimatithandiza kuti tizitha kupirira mavuto, tiziona zinthu moyenera ndiponso kuti tidzakhale osangalala mpaka kalekale.

2. Kodi Baibulo limafotokoza kuti m’tsogolomu mudzachitika zotani?

Baibulo limanena kuti m’tsogolomu “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Werengani Chivumbulutso 21:4.) Mavuto amene tikukumana nawo masiku ano monga umphawi, kupanda chilungamo, matenda komanso imfa sadzakhalaponso. Baibulo limalonjeza kuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.

3. Kodi inuyo mungatani kuti muzikhulupirira kwambiri zimene Baibulo limalonjeza?

Anthu ambiri amafuna zinthu zabwino zitachitika, koma sakhulupirira ndi mtima wonse kuti zidzachitikadi. Koma zimene Baibulo limalonjeza n’zosiyana ndi zimenezi. Tingakhulupirire kwambiri zimene Baibulo limanena ngati tikuyesetsa “kufufuza Malemba mosamala.” (Machitidwe 17:11) Mukamaphunzira Baibulo, mudziwa zimene limanena zokhudza m’tsogolo. Ndiye zili ndi inu kuzikhulupirira kapena ayi.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani zinthu zina zimene Baibulo limalonjeza zokhudza m’tsogolo ndipo onani mmene chiyembekezo chotchulidwa m’Baibulo chikuthandizira anthu masiku ano.

4. Baibulo limatilonjeza moyo wosatha komanso wangwiro

Taonani malonjezo otsatirawa amene amapezeka m’Baibulo. Kodi ndi malonjezo ati amene akusangalatsani kwambiri? Nanga n’chifukwa chiyani mukutero?

Werengani malemba amene ali pa lonjezo lililonse, kenako yankhani mafunso awa:

  • Kodi malemba amenewa akukupatsani chiyembekezo? Nanga angathandizenso anthu a m’banja lanu ndi anzanu kukhala ndi chiyembekezo?

Yerekezerani kuti muli m’dziko lomwe

PALIBE ALIYENSE AMENE . . .

ALIYENSE ADZAKHALA NDI MWAYI . . .

  • akumva kupweteka, kuvutika ndi ukalamba kapena kumwalira.​—Yesaya 25:8.

  • woona anthu amene anamwalira akuukitsidwa padziko lapansi.​—Yohane 5:28, 29.

  • wokhala ndi thanzi labwino komanso mphamvu.​—Yobu 33:25.

  • akuvutika maganizo kapena kukumbukira mavuto.​—Yesaya 65:17.

  • wokhala ndi moyo wosatha m’dziko labwino kwambiri.​—Salimo 37:29.

5. Malonjezo a m’Baibulo angakuthandizeni panopa

Anthu ambiri amakhumudwa kapenanso kukwiya akaona mavuto amene ali m’dzikoli. Anthu ena amayesetsa kumenyera ufulu kuti zinthu zisinthe. Onani mmene malonjezo a m’Baibulo akuti zinthu zidzasintha akuthandizira anthu masiku ano. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

  • Muvidiyoyi, kodi ndi zinthu ziti zopanda chilungamo zimene zinkamupweteka kwambiri Rafika?

  • Ngakhale kuti zinthu zopanda chilungamozo sizinathe, kodi Baibulo linamuthandiza bwanji?

Zimene Baibulo limatilonjeza zimatithandiza kukhala ndi chiyembekezo chabwino ndipo timasiya kukhumudwa n’kumapirira mavuto athu bwinobwino. Werengani Miyambo 17:22 ndi Aroma 12:12, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi mukuganiza kuti uthenga wa chiyembekezo wopezeka m’Baibulo ungakuthandizeni pamoyo wanu masiku ano? N’chifukwa chiyani mukutero?

ZIMENE ENA AMANENA: “Zimene Baibulo limalonjeza ndi zabwino kwambiri, koma sizingatheke.”

  • N’chifukwa chiyani muyenera kufufuza umboni wakuti zimene Baibulo limalonjeza zidzachitikadi?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Baibulo limatithandiza kukhala ndi chiyembekezo ndipo limatilonjeza kuti tidzasangalala m’tsogolo. Zimenezi zimatithandiza kuti tipirire mavuto athu panopa.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani anthu akufunika kukhala ndi chiyembekezo?

  • Kodi Baibulo limati m’tsogolo mudzachitika zotani?

  • Kodi kukhala ndi chiyembekezo kungatithandize bwanji masiku ano?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani mmene kuyembekezera zinthu zabwino za m’tsogolo kungathandizire anthu amene akudwala.

“Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onani mmene munthu wina yemwe ankamenyera ufulu wa anthu ndi zinyama anasinthira moyo wake atangophunzira zimene Baibulo limalonjeza zokhudza m’tsogolo.

“Panopa Ndilibenso Maganizo Ofuna Kusintha Zinthu M’dzikoli” (Nsanja ya Olonda, July 1, 2013)