Zimene mungachite kuti muzipindula ndi phunziro lililonse
Pezani munthu woti azikuphunzitsani: Pemphani wa Mboni za Yehova kuti azikuphunzitsani Baibulo kapena lembani fomu pawebusaiti yathu ya jw.org.
MBALI YOYAMBA
Werengani ndime iliyonse kuphatikizapo mafunso (A) komanso malemba (B) omwe akutsindika mfundo zikuluzikulu. Malemba amene alembedwa kuti “werengani” muziwawerenga mokweza mukamaphunzira ndi mphunzitsi wanu.
MBALI YAPAKATI
Mawu oyamba (C) omwe ali pansi pa kamutu kakuti Fufuzani Mozama akufotokoza mfundo zomwe mutakambirane. Mitu ing’onoing’ono (D) ikufotokozera mfundo zazikulu zomwe zili m’phunziro lililonse. Werengani malemba, yankhani mafunso ndi kuonera mavidiyo (E).
Onetsetsani zithunzi ndi mawu ake (F) ndipo ganizirani mmene mungayankhire Zimene Ena Amanena (G).
MBALI YOMALIZA
Malizani phunziro lililonse pokambirana mbali ya Zomwe Taphunzira komanso Kubwereza (H). Lembani tsiku limene mwamaliza phunziro. Mbali yakuti Zolinga (I), ili ndi zoti muchite kuti mupitirizebe kuphunzira kapenanso mugwiritse ntchito zomwe mwaphunzira. Pansi pa mutu wakuti Onani Zinanso pali zinthu zina zomwe mungakonde kuwerenga kapenanso kuonera.
Mmene mungapezere malemba m’Baibulo
Malemba asonyezedwa ndi buku la m’Baibulo (A), chaputala (B) ndi vesi kapena mavesi (C). Mwachitsanzo, Yohane 17:3 akutanthauza buku la Yohane, chaputala 17 vesi 3.