CHIGAWO 8 Kodi Imfa ya Yesu Imakukhudzani bwanji? YAMBANI Kodi Imfa ya Yesu Imakukhudzani bwanji? Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Yesu anafa kuti ife tikhale ndi moyo. Yohane 3:16 Patapita masiku atatu Yesu atamwalira, amayi ena anapita kumanda ake ndipo sanapezeko kanthu. Yehova anali ataukitsa Yesu. Kenako Yesu anaonekera kwa atumwi ake. Inde, Yehova anaukitsa Yesu kuti akhale mngelo wamphamvu ndipo anam’patsa moyo umene sungafe. Ophunzira a Yesu anamuona pamene iye ankapita kumwamba. Mulungu anaukitsa Yesu ndipo anamuika kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Danieli 7:13, 14 Yesu anapereka moyo wake dipo kuti awombole anthu. (Mateyu 20:28) Kudzera mu dipo limenelo, Mulungu wakonza zoti tidzakhale ndi moyo wosatha. Yehova anasankha Yesu kukhala Mfumu kuti alamulire dziko lapansi. Iye adzalamulira limodzi ndi anthu okhulupirika okwanira 144,000 amene amaukitsidwa kuchokera padziko lapansi kupita kumwamba. Yesu pamodzi ndi anthu 144,000 amenewo adzalamulira m’boma lakumwamba, kapena kuti, Ufumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 14:1-3. Ufumu wa Mulungu udzabweretsa paradaiso padziko lapansi. Ndipo sipadzakhalanso nkhondo, chiwawa, umphawi ndiponso njala. Anthu adzakhala osangalala kwambiri.—Salimo 145:16. Yam'mbuyo Yotsatira Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa? Baibulo limasonyeza kuti imfa ya Yesu ndi yofunika kwambiri. Kodi imfa ya Yesu ili ndi phindu lililonse? KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI? Yesu Khristu Anaphedwa Kodi Yesu anayambitsa mwambo watsopano uti, atatsala pang’ono kuti akhomedwe pa mtengo? CHIKUMBUTSO Tizikumbukira Imfa ya Yesu Tikukuitanani kuti mudzachite nafe mwambo wokumbukira imfa ya Yesu mogwirizana ndi zimene iye ananena. Mudzaphunzira mmene moyo komanso imfa ya Yesu zingakuthandizireni. MABUKU Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka? Kodi pali munthu wina yemwe munkamukonda ndipo anamwalira? Baibulo lili ndi lonjezo labwino limene lingakutonthozeni. Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kodi Imfa ya Yesu Imakukhudzani bwanji? MVERANI MULUNGU KUTI MUDZAPEZE MOYO WOSATHA Kodi Imfa ya Yesu Imakukhudzani Bwanji? Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kodi Imfa ya Yesu Imakukhudzani Bwanji? https://assetsnffrgf-a.akamaihd.net/assets/ct/e781f8601f/images/syn_placeholder_sqr.png