Anthu amene anali m’chingalawa aja anapulumuka. Ngakhale kuti patapita nthawi Nowa ndi anthu onse a m’banja lake anamwalira, Mulungu adzawaukitsa ndipo adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha.
Mulungu adzawononganso anthu oipa ndi kupulumutsa anthu abwino. Mateyu 24:37-39
Satana ndi ziwanda akupitiriza kusocheretsa anthu.