Yehova anasonyeza Adamu ndi Hava mtengo umodzi wa zipatso m’mundamo ndipo anawauza kuti akadzadya zipatso za mtengo umenewo, adzafa.
Mngelo mmodzi anagalukira Mulungu. Mngelo woipa ameneyu ndi Satana Mdyerekezi.
Satana sanafune kuti Adamu ndi Hava amvere Yehova. Choncho, kudzera mwa njoka anauza Hava kuti iwo akadya chipatso cha mtengo umene Mulungu anawauza kuti asadye, sadzafa, koma adzafanana ndi Mulungu. Limenelitu linali bodza lenileni.—Genesis 3:1-5.