Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? YAMBANI Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? Pepani, zalephereka. Koperani Vidiyoyi Onetsani Kaonekedwe ka Mawu Bisani Kaonekedwe ka Mawu Kodi mungayankhe kuti ndi . . . chinachake chimene chimakhala mu mtima mwa munthu aliyense? mawu ongophiphiritsira? boma limene lili kumwamba? ZIMENE BAIBULO LIMANENA “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.”—Danieli 2:44, Baibulo la Dziko Latsopano. “Ife tapatsidwa mwana wamwamuna, ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.”—Yesaya 9:6. KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI? Kudzakhala boma lolungama limene mudzasangalale nalo.—Yesaya 48:17, 18. M’dziko latsopano anthu adzakhala angwiro, ndiponso osangalala.—Chivumbulutso 21:3, 4. KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI? Inde tingazikhulupirire pa zifukwa ziwiri izi: Yesu anasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere komanso kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Yesu anasonyeza mmene Mulungu adzayankhire pemphero limeneli. Pamene Yesu anali padziko lapansi anadyetsa anthu anjala, kuchiritsa odwala ndiponso kuukitsa akufa. (Mateyu 15:29-38; Yohane 11:38-44) Zimene anachitazi zinasonyeza zimene Ufumuwo udzachitire anthu Yesu akadzayamba kulamulira dziko lapansili monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 11:15. Zimene zikuchitika m’dzikoli zikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Yesu ananeneratu kuti Ufumu wa Mulungu usanabweretse mtendere padziko lapansi, m’dzikoli mudzakhala nkhondo, njala komanso zivomezi.—Mateyu 24:3, 7. Zimenezi ndi zomwe zikuchitika masiku ano. Choncho sitikukayikira kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uthetsa mavuto onsewa. GANIZIRANI MFUNDO IYI Kodi moyo udzakhala wotani mu Ufumu wa Mulungu? Baibulo limayankha funso limeneli pa SALIMO 37:29 ndi pa YESAYA 65:21-23. Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? Ali padziko lapansi, Yesu anafotokoza kwambiri za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse. Kwa zaka zambiri otsatira ake akhala akupempherera Ufumu umenewu kuti ubwere. ZOKHUDZA IFEYO N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo—Vidiyo Yathunthu Baibulo likuthandiza anthu ambirimbiri padziko lonse lapansi kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri. Kodi inunso mungakonde? Sindikizani Patsani ena Patsani ena Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? MABUKU Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? Chinenero Chamanja cha ku Malawi Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1102014810/univ/art/1102014810_univ_sqr_xl.jpg T-36 p. 2