GAWO 2

Anataya Mwayi Wokhala M’Paradaiso

Anataya Mwayi Wokhala M’Paradaiso

Mngelo wopanduka anakopa Adamu ndi Hava, mwamuna ndi mkazi oyamba, kuti akane ulamuliro wa Mulungu. Chifukwa cha zimenezi anthu onse anachimwa ndipo anayamba kufa

KALE kwambiri Mulungu asanalenge anthu, analenga angelo ambirimbiri omwe sitingathe kuwaona. M’munda wa Edeni, mngelo wopanduka, amene anadzakhala Satana Mdyerekezi, mochenjera anayesetsa kunyengerera Hava kuti adye chipatso cha mtengo umene Mulungu anawaletsa.

Polankhula kudzera mwa njoka, Satana ananena kuti Mulungu anabisira mwamuna ndi mkazi wakeyo zinthu zabwino kwambiri. Mngeloyo anauza Hava kuti iye ndi mwamuna wake sangafe atadya chipatso chimene Mulungu anawaletsacho. Choncho pamenepa Satana anaimba Mulungu mlandu woti ananamiza Adamu ndi Hava, omwe anali ana ake. Satana ananama kuti ngati anthu atapanda kumvera Mulungu, zinthu zidzawayendera bwino kwambiri ndiponso adzadziwa zinthu zochuluka komanso adzakhala ndi ufulu. Koma limeneli linali bodza lamkunkhuniza, ndipotu linali bodza loyamba kunenedwa padziko lapansi. Nkhani yaikulu pamenepa inali yokhudza ulamuliro umene Mulungu ali nawo pa chilengedwe chonse. Satana anakayikira zoti Mulungu ndi woyenera kulamulira, zoti amalamulira mwachilungamo komanso mokomera anthu.

Hava anakhulupirira bodza la Satanalo. Iye anayamba kusirira chipatsocho, ndipo anadya. Kenako anapatsa mwamuna wake ndipo nayenso anadya. Atachita zimenezi anachimwa. Zimene anachitazi, ngakhale kuti zingaoneke ngati nkhani yaing’ono, zinasonyeza kusamvera Mulungu. Posankha mwadala kusamvera lamulo la Mulungu, Adamu ndi Hava anakana ulamuliro wa Mlengi amene anawapatsa chilichonse, ngakhalenso moyo wangwiro.

Mbewu “idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.”—Genesis 3:15

Mulungu anaweruza opandukawo chifukwa cha zimene anachitazo. Iye ananeneratu kuti kudzabwera Mbewu yolonjezedwa, kapena kuti Mpulumutsi, amene adzawononge Satana yemwe akuimiridwa ndi njoka. Mulungu anapereka chilango cha imfa kwa Adamu ndi Hava, koma sanawaphe nthawi yomweyo. Pamenepa Mulungu anachitira chifundo ana awo amene anali asanabadwe. Ana amenewo anali ndi chifukwa choyembekezera zabwino m’tsogolo popeza Mulungu analonjeza kuti adzatumiza winawake amene adzachotse mavuto amene anayambika m’munda wa Edeni chifukwa cha kupandukako. Pamene ntchito yolemba Baibulo inkapitirira, zinadziwika mmene Mulungu adzakwaniritsire cholinga chake chokhudza Mpulumutsi wam’tsogoloyu komanso kuti Mpulumutsi ameneyo adzakhala ndani.

Mulungu anapitikitsa Adamu ndi Hava m’Paradaiso, ndipo iwo anafunika kugwira mwakhama ntchito yolima, kunja kwa munda wa Edeni, kuti apeze chakudya. Kenako Hava anakhala ndi pakati ndipo anabereka Kaini, mwana wawo woyamba. Adamu ndi Hava anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi, ndipo ena mwa iwo anali Abele ndiponso Seti, agogo ake a Nowa.

—Nkhaniyi yachokera m’buku la Genesis chaputala 3 mpaka 5 ndi pa Chivumbulutso 12:9.