N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Baibulo?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Baibulo?

Kodi Baibulo mumalidziwa bwino? Palibe buku limene lafalitsidwa kwambiri kuposa Baibulo. Anthu a mafuko onse amaona kuti uthenga wake ndi wolimbikitsa ndiponso wopatsa chiyembekezo. Amaonanso kuti m’Baibulo muli malangizo othandiza pamoyo watsiku ndi tsiku. Komabe, anthu ambiri masiku ano sakulidziwa bwino Baibulo. Mwina inuyo mumachita chidwi ndi Baibulo, kaya ndinu wopemphera kapena ayi. Kabuku kano kakonzedwa kuti kakuthandizeni kudziwa mwachidule zimene zili m’Baibulo.

MUSANAYAMBE kuwerenga Baibulo, ndi bwino kuti mudziwe zinthu zina zokhudza bukuli. Baibulo limatchedwanso Malemba Opatulika, ndipo lili ndi mabuku kapena kuti zigawo zokwana 66, kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso.

Kodi uthenga umene uli m’Baibulo ndi wochokera kwa ndani? Limeneli ndi funso labwino kwambiri. Baibulo linalembedwa ndi amuna okwana 40 pa nthawi ya zaka zoposa 1,600. N’zochititsa chidwi kuti amuna amenewa sananene kuti uthenga wa m’Baibulo unachokera kwa iwowo. Mwachitsanzo, mwamuna wina amene analemba nawo Baibulo ananena kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Winanso amene analemba nawo Baibulo anati: “Mzimu wa Yehova unandilankhulitsa, ndipo mawu ake anali palilime langa.” (2 Samueli 23:2) Chotero anthu amene analemba Baibulo amanena kuti uthenga wa m’Baibulo unachokera kwa Yehova Mulungu, Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Olemba Baibulo anasonyeza kuti Mulungu akufuna kuti anthu amudziwe bwino.

Palinso chinthu china chofunika kwambiri chimene chingatithandize kuti timvetse bwino Baibulo. Malemba onse ali ndi mfundo imodzi yaikulu yakuti: Mulungu ndiye woyenera kulamulira anthu kudzera mu Ufumu wake wakumwamba. M’masamba akutsogoloku muona kuti mfundo yaikulu imeneyi ikuoneka m’mabuku onse kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso.

Tsopano tiyeni tione uthenga wopezeka m’Baibulo, buku lotchuka kwambiri padziko lonse.