GAWO 12

Nzeru Zochokera kwa Mulungu N’zothandiza pa Moyo

Nzeru Zochokera kwa Mulungu N’zothandiza pa Moyo

M’buku la Miyambo muli malangizo ouziridwa amene amathandiza pa moyo wa tsiku ndi tsiku, ndipo amene analemba mbali yaikulu ya bukuli ndi Solomo

KODI Yehova ndi Wolamulira wanzeru? Njira imodzi imene ingatithandize kwambiri kuyankha funso limeneli ndi kuona malangizo amene iye amapereka. Kodi malangizo amene iye amapereka ndi othandizadi? Kodi anthu akamatsatira malangizo akewo amakhala ndi moyo wabwino ndiponso wosangalatsa? Mfumu yanzeru Solomo inalemba malangizo ambirimbiri amene ali m’buku la Miyambo ndipo ndi othandiza pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Taonani ena mwa malangizo amenewo.

Tiyenera kukhulupirira Mulungu. Kukhulupirira Yehova n’kofunika kwambiri kuti tikhale naye pa ubwenzi wabwino. Solomo analemba kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.” (Miyambo 3:5, 6) Kukhulupirira Mulungu mwa kumvera ndi kutsatira malangizo ake kumathandiza kuti munthu akhale ndi moyo wabwino. Munthu akamachita zimenezi amasangalatsa mtima wa Mulungu ndiponso amathandiza Yehova kuti ayankhe mabodza a mdani wake Satana.—Miyambo 27:11.

Tiyenera kuchita zinthu mwanzeru ndi anthu ena. Masiku ano, m’pofunika kwambiri kutsatira malangizo amene Mulungu amapereka kwa amuna, akazi ndiponso ana. Mulungu akulangiza mwamuna wokwatira kuti: “Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako,” ndipo zimenezi zikutanthauza kuti mwamuna ayenera kukhala wokhulupirika kwa mkazi wake. (Miyambo 5:18-20) Akazi okwatiwa angapeze malangizo othandiza m’buku la Miyambo chifukwa muli mfundo zomveka bwino zokhudza mkazi wabwino amene mwamuna ndi ana ake amamulemekeza. (Miyambo, chaputala 31) Nawonso ana angapeze malangizo owathandiza kumvera makolo awo. (Miyambo 6:20) Bukuli likusonyezanso kuti ndi bwino kuti munthu akhale ndi anzake ocheza nawo chifukwa munthu akamadzipatula amayamba kudzikonda. (Miyambo 18:1) Komabe tiyenera kusankha mwanzeru anthu ocheza nawo chifukwa timatengera zochita za anzathu, kaya ndi zabwino kapena zoipa.—Miyambo 13:20; 17:17.

Muzichita zinthu mwanzeru. M’buku la Miyambo muli malangizo abwino kwambiri otithandiza kupewa kumwa mowa mwauchidakwa, otithandiza kukhala ndi maganizo abwino komanso kupewa maganizo oipa. Mulinso malangizo otilimbikitsa kuti tizigwira ntchito mwakhama. (Miyambo 6:6; 14:30; 20:1) Bukuli limatichenjezanso kuti kudalira nzeru za munthu, zimene ndi zosiyana ndi malangizo amene Mulungu amapereka, n’koopsa. (Miyambo 14:12) Komanso, bukuli limatilimbikitsa kuti tiziteteza mtima wathu ku zinthu zimene zingatiwononge, “pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.”—Miyambo 4:23.

Anthu ambirimbiri padziko lonse aona kuti kutsatira malangizo a m’buku limeneli kwawathandiza kwambiri pa moyo wawo. Ndipotu zimenezi zawathandiza kuvomereza mosavuta kuti Yehova ndi Wolamulira wawo.

—Nkhaniyi yachokera m’buku la Miyambo.