Yakobo, Petulo, Yohane ndi Yuda analemba makalata polimbikitsa Akhristu anzawo
YAKOBO ndi Yuda anali abale ake a Yesu, ndipo Petulo ndi Yohane anali m’gulu la atumwi ake 12. Amuna anayi amenewa analemba makalata okwana 7 amene ali m’Malemba Achigiriki. Kalata iliyonse ili ndi dzina la amene anailemba ndipo malangizo ouziridwa amene ali m’makalata amenewa, anaperekedwa pothandiza Akhristu kuti azikhala okhulupirika kwa Yehova ndi Ufumu wake.
Akhristu ayenera kusonyeza chikhulupiriro. Kungonena kuti tili ndi chikhulupiriro si kokwanira. Munthu amene ali ndi chikhulupiriro chenicheni amaoneka ndi zochita zake. Yakobo analemba kuti: “Chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.” (Yakobo 2:26) Munthu akasonyeza chikhulupiriro pamene akukumana ndi mayesero, amakhala wopirira. Kuti alimbane ndi mayesero, Mkhristu ayenera kupempha nzeru kwa Mulungu, ndipo azikhulupirira kuti Mulungu adzam’patsa nzeruzo. Mulungu amasangalala ndi munthu amene akupirira. (Yakobo 1:2-6, 12) Munthu akamasonyeza chikhulupiriro potumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, Yehova Mulungu amamuthandiza. Yakobo anati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.