Davide ndi anthu ena anapeka nyimbo zomwe ankaziimba polambira Mulungu, ndipo ena mwa mawu a nyimbo zimenezo ali m’buku la Masalimo. M’buku limeneli muli mawu a nyimbo zokwana 150
BUKU la Masalimo, lomwe ndi lalikulu kwambiri m’Baibulo, ndi buku la nyimbo zopatulika. Buku lonseli linalembedwa pa nthawi ya zaka pafupifupi 1,000. Pa mfundo zonse zokhudza chikhulupiriro zimene zinalembedwapo, buku la Masalimo lili ndi mfundo zambiri zosangalatsa komanso zogwira mtima kwambiri. Buku limeneli likusonyeza m’njira zosiyanasiyana mmene anthu ankamvera mumtima mwawo. Mwachitsanzo, muli mawu osonyeza kusangalala, kutamanda ndi kuyamikira Mulungu, kulira, kumva chisoni komanso osonyeza kulapa. N’zoonekeratu kuti anthu amene analemba Masalimo ankakonda kwambiri Mulungu ndiponso ankamukhulupirira. Tiyeni tione zina mwa mfundo zikuluzikulu zimene zili m’nyimbo zimenezi.
Yehova ndiye woyenera kulamulira komanso woyenera kumulambira ndi kumutamanda. Pa lemba la Salimo 83:18 pali mawu akuti: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” Masalimo ambiri amatamanda Yehova chifukwa cha zinthu zimene analenga, monga nyenyezi zakumwamba, zinthu zamoyo zapadziko zomwe ndi zochititsa chidwi komanso thupi la munthu lomwe ndi lodabwitsa. (Masalimo 8, 19, 139, 148) Masalimo ena amalemekeza Yehova chifukwa ndi Mulungu amene amateteza ndi kupulumutsa anthu ake okhulupirika. (Masalimo 18, 97, 138) Ndipo masalimo ena amatamanda Yehova chifukwa ndi Mulungu wachilungamo, amene amathandiza anthu oponderezedwa ndi kupereka chilango kwa anthu oipa.—Masalimo 11, 68, 146.