GAWO 15

Mneneri Amene Anali ku Ukapolo Anaona Masomphenya a Zimene Zidzachitike M’tsogolo

Mneneri Amene Anali ku Ukapolo Anaona Masomphenya a Zimene Zidzachitike M’tsogolo

Danieli analosera za Ufumu wa Mulungu ndiponso kubwera kwa Mesiya. Babulo anawonongedwa

DANIELI anali mnyamata amene ankatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika ndipo anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo Yerusalemu asanawonongedwe. Iye pamodzi ndi Ayuda ena anatengedwa kuchokera ku ufumu wa Yuda umene anali utagonjetsedwa ndipo iwo anapatsidwa ufulu wochita zinthu zina. Pa nthawi yonse imene Danieli anakhala ku Babulo, Mulungu anamudalitsa kwambiri ndiponso anamupulumutsa ataponyedwa m’dzenje la mikango. Komanso Mulungu anamuonetsa masomphenya a zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo. Ulosi wofunika kwambiri umene Danieli ananena unali wokhudza Mesiya ndiponso Ufumu wa Mesiyayo.

Danieli anauzidwa nthawi imene Mesiya adzafike. Danieli anauzidwa nthawi imene anthu a Mulungu anafunika kuyembekezera kubwera kwa “Mesiya Mtsogoleri.” Iye anauzidwa kuti Mesiya adzabwera pakatha milungu 69 ya zaka kuchokera nthawi imene lamulo linaperekedwa lonena kuti mpanda wa Yerusalemu umangidwenso. Mlungu umodzi umakhala ndi masiku 7, ndipo mlungu wa zaka umakhala ndi zaka 7. Lamulo lakuti Yerusalemu amangidwenso linaperekedwa mu 455 B.C.E., patadutsa nthawi yaitali kwambiri Danieli atamwalira kale. Tikawerengera “milungu” 69 ya zaka, imatipatsa zaka 483, ndipo tikawerengera zaka zimenezi kuyambira m’chaka cha 455 B.C.E., timafika m’chaka cha 29 C.E. M’mitu yakutsogoloku, tiona zimene zinachitika m’chaka chimenechi. Danieli anaonanso kuti Mesiya “adzaphedwa” n’cholinga choti aphimbe machimo a anthu.—Danieli 9:24-26.

Mesiya adzakhala Mfumu kumwamba. M’masomphenya ochititsa chidwi kwambiri a kumwamba, Danieli anaona Mesiya “wooneka ngati mwana wa munthu,” atafika kumpando wachifumu wa Yehova. Ndipo Yehova anamupatsa “ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu” umene sudzatha. Danieli anadziwanso mfundo ina yosangalatsa kwambiri yonena za Ufumu wa Mesiya. Iye anadziwa kuti pali anthu ena amene adzalamulira pamodzi ndi Mfumuyi, ndipo gulu la anthu amenewa limatchedwa “oyera a Wamkulukulu.”—Danieli 7:13, 14, 27.

Ufumu wa Mesiya udzawononga maboma a m’dzikoli. Mulungu anathandiza Danieli kumasulira maloto amene anaimitsa mutu Nebukadinezara, mfumu ya ku Babulo. Mfumuyo inaona chifaniziro chachikulu kwambiri ndipo chinali ndi mutu wagolide, chifuwa chake ndi manja ake zinali zasiliva, mimba yake ndi ntchafu zake zinali zamkuwa, miyendo yake inali yachitsulo, ndipo mapazi ake anali achitsulo chosakanizika ndi dongo. Kenako mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu ndipo unamenya chifanizirocho kumapazi ake achitsulo chosakanizika ndi dongo ndipo chinanyenyeka n’kukhala ngati phulusa. Danieli anafotokoza kuti mbali zosiyanasiyana za chifanizirocho zikuimira maulamuliro osiyanasiyana amphamvu kwambiri padziko lonse, kuyambira ndi ufumu wa Babulo umene unaimiridwa ndi mutu wagolide. Danieli anaonanso kuti m’nthawi ya ulamuliro womaliza wamphamvu kwambiri m’dziko loipali, Ufumu wa Mulungu udzalowererapo mwa kuphwanya maboma onse padziko lapansili ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.—Danieli, chaputala 2.

Danieli anali wokalamba kwambiri pamene anaona mzinda wa Babulo ukuwonongedwa. Mfumu Koresi anagonjetsa mzindawo monga mmene aneneri analoserera. Kenako, mogwirizana ndi zimene aneneri ananena, Ayuda anamasulidwa ku ukapolo ndipo anabwerera kudziko la kwawo, lomwe linakhala la bwinja kwa zaka 70. Motsogoleredwa ndi akazembe, ansembe ndiponso aneneri amene anali okhulupirika, Ayuda anamanganso Yerusalemu ndi kachisi wa Yehova. Koma kodi chinachitika n’chiyani zaka 483 zitatha?

—Nkhaniyi yachokera m’buku la Danieli.