GAWO 19

Yesu Analosera Zinthu za M’tsogolo Zimene Zidzakhudze Dziko Lonse

Yesu Analosera Zinthu za M’tsogolo Zimene Zidzakhudze Dziko Lonse

Yesu anatchula zinthu zimene zidzasonyeze kuti wayamba kulamulira ndiponso kuti tili m’nthawi ya mapeto

YESU ali paphiri la Maolivi, pamene ankatha kuona mzinda wa Yerusalemu komanso kachisi, ophunzira ake anayi anamufunsa paokha kuti afotokoze bwino tanthauzo la zimene ananena. Yesu anali atanena kuti kachisi amene anali ku Yerusalemu adzawonongedwa. Ndipo asanawauze zimenezi, anali atawauza za “mapeto a nthawi ino.” (Mateyu 13:40, 49) Tsopano atumwiwo anafunsa kuti: “Kodi . . . chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?”—Mateyu 24:3.

Poyankha, Yesu ananena zimene zidzachitike Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa. Koma zimene ananenazo zinalinso ndi tanthauzo lina. Iye ananena ulosi umene kukwaniritsidwa kwake kwakukulu kudzakhudza dziko lonse. Yesu analosera zinthu zosiyanasiyana zimene zidzachitike padziko lapansi, zomwe zidzakhale chizindikiro chakuti iye wayamba kulamulira kumwamba. M’mawu ena tinganene kuti chizindikiro chimenechi chidzasonyeza kuti Yehova Mulungu waika Yesu kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya umene unalonjezedwa kalekale. Chizindikirocho chidzatanthauza kuti Ufumuwo watsala pang’ono kuthetsa zoipa zonse ndi kubweretsa mtendere weniweni kwa anthu onse. Choncho zinthu zimene Yesu analoserazo zinasonyeza zimene zidzachitike m’masiku otsiriza a nthawi ino, monga kutha kwa zipembedzo zonyenga, maboma andale ndiponso zochita zosiyanasiyana za anthu. Komanso zimene Yesu analoserazo zinasonyeza kuyambika kwa dziko latsopano.

Pofotokoza zimene zidzachitike padziko lapansi iye akadzapatsidwa Ufumu kumwamba, Yesu ananena kuti padzakhala nkhondo, njala, zivomerezi zamphamvu ndiponso miliri. Ananenanso kuti anthu ambiri azidzachita zinthu zosonyeza kusamvera malamulo. Ophunzira enieni a Yesu azidzalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi. Mapeto a zonsezi adzakhala “chisautso chachikulu” chimene sichinachitikepo n’kale lonse.—Mateyu 24:21.

Kodi otsatira a Yesu akanadziwa bwanji kuti chisautso chimenecho chayandikira? Yesu ananena kuti: “Phunzirani mfundo imeneyi pa fanizo ili la mkuyu.” (Mateyu 24:32) Mtengo wa mkuyu ukayamba kuphukira masamba, anthu amatha kudziwa kuti nyengo yadzinja yayandikira. Mofanana ndi zimenezi, zinthu zonse zimene Yesu ananena zikadzachitika pa nthawi imodzi, chidzakhala chizindikiro chakuti mapeto ayandikira. Atate okha ndi amene angadziwe tsiku kapena ola limene chisautso chachikulu chidzayambe. Choncho Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti: “Khalani tcheru, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika.”—Maliko 13:33.

—Nkhaniyi yachokera pa Mateyu chaputala 24 ndi 25, Maliko chaputala 13 ndi pa Luka chaputala 21.

^ ndime 14 Kuti mumve zambiri zokhudza ulosi wa Yesu, onani buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa mutu 9. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.