Zozizwitsa zimene Yesu ankachita zinasonyeza mmene adzagwiritsire ntchito mphamvu zake monga Mfumu
MULUNGU anapatsa Yesu mphamvu kuti azichita zinthu zimene anthu ena sangachite. Yesu anachita zozizwitsa zambirimbiri, ndipo kawirikawiri ankazichita anthu ambiri akuonerera. Zozizwitsa zimenezo zinasonyeza kuti Yesu ali ndi mphamvu zogonjetsera adani ndiponso kuthetsa mavuto onse amene anthu opanda ungwiro amalephera kuwathetsa. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.
Yesu anadyetsa anthu. Pa chozizwitsa chake choyamba, Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo wabwino. Pa nthawi zinanso ziwiri iye anadyetsa anthu ambirimbiri ndi mitanda yochepa ya mkate komanso nsomba zochepa. Pa nthawi zonsezi aliyense anadya ndipo anakhuta.
Yesu anachiritsa anthu odwala. Yesu anachiritsa anthu amene anali ndi “matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.” (Mateyu 4:23) Iye anachiritsa anthu akhungu, ogontha, akhate, akhunyu komanso olumala. Panalibe matenda aliwonse amene analephera kuwachiritsa.
Yesu analetsa mphepo yamkuntho. Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankawoloka nyanja ya Galileya pangalawa, panyanjapo panayamba mphepo yamkuntho ndipo ophunzirawo anachita mantha kwambiri. Koma Yesu anangoyang’ana mphepo yamkunthoyo n’kunena kuti: “Leka! Khala bata!” Atatero mphepoyo inaleka ndipo panachita bata lalikulu. (Maliko 4:37-39) Pa nthawi inanso, Yesu anayenda pamadzi amene ankachita mafunde akuluakulu chifukwa cha mphepo yamphamvu.—Mateyu 14:24-33.
Yesu anatulutsa mizimu yoipa. Mizimu yoipa ndi yamphamvu kwambiri kuposa anthu. Anthu ambiri alephera kumasuka ku mizimu yoipayi yomwe ndi adani a Mulungu. Koma nthawi zingapo, Yesu anailamula kuti ituluke mwa anthu, ndipo inatulukadi. Iye sankaopa mizimu imeneyo. Koma mizimuyo inkadziwa mphamvu zimene iye ali nazo ndipo inkamuopa.
Yesu anaukitsa akufa. Moyenerera, imfa imatchedwa “mdani womalizira” ndipo palibe munthu amene angaigonjetse. (1 Akorinto 15:26) Koma Yesu anaukitsa anthu akufa. Mwachitsanzo, anaukitsa mnyamata wina ndi kumupereka kwa mayi ake amene anali amasiye, komanso anaukitsa mtsikana wamng’ono ndi kumupereka kwa makolo ake amene anali ndi chisoni kwambiri. Pa nthawi ina, Yesu anachita zinthu zosaiwalika. Iye anaukitsa mnzake wapamtima Lazaro pamaso pa khamu la anthu amene ankalira maliro a Lazaroyo. Iye anachita zimenezi ngakhale kuti panapita masiku anayi kuchokera pamene anamwalira. Ngakhale adani enieni a Yesu, anavomereza kuti iye anachitadi chozizwitsa chimenechi.—Yohane 11:38-48; 12:9-11.
N’chifukwa chiyani Yesu anachita zozizwitsa zonsezi? N’zoona kuti anthu onse amene anawathandizawo anafabe patapita nthawi, koma zozizwitsa zimene Yesu ankachita n’zothandiza kwambiri. Zinasonyeza kuti maulosi onse osangalatsa okhudza Ufumu wa Mesiya adzakwaniritsidwadi. Sitingakayikire n’komwe kuti Mfumu yoikidwa ndi Mulungu imeneyi idzathetsa njala, matenda, masoka achilengedwe komanso kugonjetsa mizimu yoipa ngakhalenso imfa. Yesu anasonyeza kale kuti Mulungu anam’patsa mphamvu zochitira zinthu zimenezi.