PHUNZIRO 10
Kodi Chipembedzo Choona Mungachidziwe Bwanji?
1. Kodi chipembedzo choona chilipo chimodzi chokha?
Yesu anayambitsa chipembedzo choona chimodzi chokha, ndipo otsatira ake anali m’chipembedzo chimenecho. Chipembedzocho chili ngati msewu womwe ukulowera ku moyo wosatha. Ponena za msewu umenewu, Yesu ananena kuti: “Amene akuupeza ndi anthu owerengeka.” (Mateyu 7:14) Mulungu amavomereza anthu okhawo amene akumulambira mogwirizana ndi mfundo zochokera m’Mawu ake Baibulo, omwe ndi choonadi. Anthu onse omwe ndi olambira oona amakhulupirira zinthu zofanana.—Werengani Yohane 4:23, 24; 14:6; Aefeso 4:4, 5.
Onerani vidiyo yakuti Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?
2. Kodi Yesu ananena chiyani chokhudza Akhristu onyenga?
Yesu anachenjeza kuti aneneri onyenga adzayamba kuphunzitsa zinthu zabodza pakati pa Akhristu. Pamaso chabe, aneneri onyenga amenewa amaoneka ngati amalambira Mulungu m’njira yoyenera. Komanso amanena kuti zipembedzo zawo ndi zachikhristu. Komabe, munthu angathe kuwazindikira kuti si Akhristu oona. Kodi angawazindikire bwanji? Angawazindikire chifukwa chakuti ndi chipembedzo choona chokha chimene anthu ake ndi Akhristu enieni ndipo makhalidwe awo komanso zochita zawo zimakhala zabwino.—Werengani Mateyu 7:13-23.
3. N’chiyani chingakuthandizeni kuti mudziwe olambira oona?
Taonani zinthu zisanu zomwe ndi zizindikiro za olambira oona a Mulungu:
Olambira oona amalemekeza Baibulo monga Mawu a Mulungu. Iwo amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo. Choncho chipembedzo choona chimasiyana ndi chipembedzo chimene chimayendera maganizo a anthu. (Mateyu 15:7-9) Komanso olambira oona samangophunzitsa chabe koma amayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene amaphunzitsazo.—Werengani Yohane 17:17; 2 Timoteyo 3:16, 17.
Otsatira a Yesu enieni amalemekeza dzina la Mulungu lakuti Yehova. Yesu analemekeza dzina la Mulungu polidziwikitsa kwa anthu ena. Iye anathandiza anthu ena kudziwa Mulungu komanso anawaphunzitsa kupemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. (Mateyu 6:9) M’dera limene mukukhala, kodi ndi chipembedzo chiti chomwe chimauza anthu ena za dzina la Mulungu?—Werengani Yohane 17:26; Aroma 10:13, 14.
Akhristu enieni amalalikira za Ufumu wa Mulungu. Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzalalikire uthenga wabwino wa Ufumu. Tsogolo la anthu likudalira pa Ufumu wa Mulungu wokha womwe udzabweretse madalitso ambiri. Yesu ankauza anthu za Ufumu umenewu mpaka pa tsiku la imfa yake. (Luka 4:43; 8:1; 23:42, 43) Iye ananenanso kuti otsatira ake azilalikira za Ufumuwo. Ndiyeno kodi munthu wina atakupezani n’kumakuuzani za Ufumu wa Mulungu, mungaganize kuti munthu ameneyu ndi wachipembedzo chiti?—Werengani Mateyu 24:14.
Otsatira a Yesu sali mbali ya dziko loipali. Otsatira a Yesu mungawadziwe chifukwa chakuti iwo salowerera nkhani zandale kapena mikangano imene imachitika m’madera amene iwo akukhala. (Yohane 17:16; 18:36) Komanso samatengera makhalidwe ndi maganizo oipa a m’dzikoli.—Werengani Yakobo 4:4.
Akhristu enieni amakondana kuchokera pansi pa mtima. Iwo amaphunzira m’Mawu a Mulungu kuti ayenera kulemekeza anthu a mitundu yonse. Ngakhale kuti zipembedzo zonyenga zakhala zikulowerera nkhondo mayiko osiyanasiyana akamamenyana, olambira oona amakana kuchita zimenezi. (Mika 4:1-3) M’malomwake, Akhristu oona amagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso chuma chawo kuti athandize ena komanso kuwalimbikitsa.—Werengani Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 4:20.
4. Kodi tsopano mwachidziwa chipembedzo choona?
Kodi ndi chipembedzo chiti chomwe mfundo zake zonse zimachokera m’Mawu a Mulungu, chimalemekeza dzina la Mulungu komanso chimalalikira zoti ndi Ufumu wa Mulungu wokha womwe ungabweretse madalitso kwa a anthu padziko lapansi? Kodi ndi gulu liti la anthu lomwe limakondana kuchokera pansi pa mtima komanso lomwe limakana kumenya nkhondo? Tikukhulupirira kuti mwalidziwa tsopano.—Werengani 1 Yohane 3:10-12.
UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU