Kabuku kano kakuthandizani kuti muzisangalala mukamaphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo. Kumapeto kwa ndime iliyonse kuli malemba a m’Baibulo omwe angakuthandizeni kudziwa yankho la funso limene lalembedwa ndi mawu akuda kwambiri lomwe lili pamwamba pa ndimeyo.
Pamene mukuwerenga malemba a m’Baibulo, ganizirani mmene malembawo akuyankhira mafunsowo. Aliyense wa Mboni za Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani kumvetsa bwino Malembawo.—Werengani Luka 24:32,45.
Dziwani izi: Mabuku omwe atchulidwa m’kabuku kano ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.