PHUNZIRO 8
N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Zinthu Zoipa Komanso Kuti Anthu Azivutika?
1. Kodi zinthu zoipa zinayamba bwanji?
Zinthu zoipa zinayamba padziko lapansi pamene Satana ananena bodza loyamba. Poyamba Satana anali mngelo wangwiro, koma “sanakhazikike m’choonadi.” (Yohane 8:44) Choncho anayamba kulakalaka kulambiridwa. Zimenezi sizinali zoyenera chifukwa Mulungu yekha ndiye woyenera kulambiridwa. Pofuna kukwaniritsa cholinga chake, Satana ananamiza mkazi woyamba, Hava, n’kumunyengerera kuti amumvere m’malo momvera Mulungu. Kenako Adamu nayenso sanamvere Mulungu, ndipo anachita zimene Hava anachita. Zimenezi zinachititsa kuti anthu azivutika komanso kufa.—Werengani Genesis 3:1-6, 19.
Satana anayamba kugalukira ulamuliro wa Mulungu kapena kuti udindo wake monga Wam’mwambamwamba, pamene anauza Hava kuti asamvere Mulungu. Anthu ambiri m’dzikoli ali kumbali ya Satana ndipo akukana kuti Mulungu akhale Wolamulira wawo. Choncho, Satana wakhala “wolamulira wa dziko.”—Werengani Yohane 14:30; 1 Yohane 5:19.
2. Kodi zinthu zimene Mulungu analenga n’zimene zinali ndi vuto?
Zonse zimene Mulungu amapanga zimakhala zangwiro zokhazokha. Mwachitsanzo, Mulungu analenga anthu komanso angelo angwiro amene akanatha kumumvera popanda chovuta chilichonse. (Deuteronomo 32:4, 5) Potilenga, Mulungu anatipatsa ufulu wosankha kuchita chabwino kapena choipa. Ufulu umenewu umatipatsa mwayi wosonyeza chikondi chathu kwa Mulungu.—Werengani Yakobo 1:13-15; 1 Yohane 5:3.
3. N’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti anthu azivutika mpaka pano?
Kwa nthawi yochepa, Yehova walola kuti anthu komanso angelo ena apandukire ufumu wake. Chifukwa chiyani wachita zimenezi? Iye wachita zimenezi kuti anthu aone okha kuti ndi ulamuliro wa Mulungu wokha umene ungathetse mavuto a anthu. (Mlaliki 7:29; 8:9) Tsopano padutsa zaka 6,000 anthu akudzilamulira okha, ndipo zikuonekeratu kuti ulamuliro wa anthu walephera kuthetsa nkhondo, uchigawenga, kupanda chilungamo, komanso matenda.—Werengani Yeremiya 10:23; Aroma 9:17.
Mosiyana ndi ulamuliro wa anthu, ulamuliro wa Mulungu umathandiza anthu amene ali kumbali yake. (Yesaya 48:17, 18) Posachedwapa Yehova athetsa maboma onse a anthu, ndipo anthu okhawo amene asankha kuti Mulungu aziwalamulira, adzakhala padziko lapansi.—Yesaya 11:9; Werengani Danieli 2:44.
Onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?
4. Kodi kuleza mtima kwa Mulungu kwatipatsa mpata wochita chiyani?
Satana ananena kuti anthu amatumikira Yehova chifukwa cha dyera basi. Kodi mungakonde kutsutsa bodza limeneli? Mungathe kulitsutsa. Kuleza mtima kwa Mulungu kwatipatsa mpata woti tisonyeze ngati timakonda ulamuliro wa Mulungu kapena wa anthu. Zimene timachita pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku n’zomwe zimasonyeza ulamuliro umene tasankha.—Werengani Yobu 1:8-12; Miyambo 27:11.
5. Kodi tingasankhe bwanji Mulungu kuti akhale Wolamulira wathu?
Tingasankhe Mulungu kuti akhale Wolamulira wathu pofufuza chipembedzo choona n’kumachita zimene chipembedzo choonacho chimafuna mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, Baibulo. (Yohane 4:23) Tingakane Satana kuti akhale wolamulira wathu potengera chitsanzo cha Yesu amene anapewa kulowerera mu ndale komanso kumenya nkhondo.—Werengani Yohane 17:14.
Satana akugwiritsa ntchito mphamvu zake polimbikitsa anthu kuti azichita chiwerewere ndi makhalidwe ena oipa. Tikamapewa makhalidwe amenewa, anzathu kapena achibale ena angayambe kutinyoza kapena kutitsutsa. (1 Petulo 4:3, 4) Zikatero tingafunike kusankha zimene tikuona kuti n’zabwino. Kodi tidzapitiriza kugwirizana ndi anthu amene amakonda Mulungu? Kodi tidzamvera malamulo ake anzeru, amenenso amasonyeza mmene amatikondera? Ngati titachita zimenezi, tidzasonyeza kuti Satana ananama ponena kuti munthu aliyense sangamvere Mulungu pamene akukumana ndi mavuto.—Werengani 1 Akorinto 6:9, 10; 15:33.
Mulungu amakonda kwambiri anthu, ndipo umenewu ndi umboni wakuti adzathetsa mavuto komanso zinthu zonse zoipa. Choncho aliyense amene amakhulupirira zimenezi, adzasangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi kwamuyaya.—Werengani Yohane 3:16.
UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU