PHUNZIRO 9
Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?
1. Kodi kukwatirana motsatira malamulo kumathandiza bwanji kuti banja likhale losangalala?
Yehova, Mulungu wachimwemwe, amafuna kuti mabanja azikhala osangalala, ndipo umenewu ndi uthenga wabwino. (1 Timoteyo 1:11) Iye ndi amene anayambitsa ukwati. Kukwatirana motsatira malamulo kumathandiza kuti banja likhale losangalala chifukwa chakuti limakhala malo abwino olereramo ana. Choncho Akhristu ayenera kulemekeza malamulo a boma okhudza kulembetsa ukwati.—Werengani Luka 2:1, 4, 5.
Kodi Mulungu amaona bwanji ukwati? Mulungu amafuna kuti mwamuna ndi mkazi okwatirana azikhala limodzi moyo wawo wonse. Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi amene ali pabanja, onse azikhala okhulupirika m’banjamo. (Aheberi 13:4) Iye amadana ndi kuthetsa ukwati. (Malaki 2:16) Komabe amalola kuti Mkhristu athetse ukwati wake n’kukwatirana ndi munthu wina ngati mnzake m’banjamo wachita chigololo.—Werengani Mateyu 19:3-6, 9.
2. Kodi mwamuna ndi mkazi wake ayenera kumakhala motani?
Yehova analenga mwamuna ndi mkazi kuti azithandizana m’banja. (Genesis 2:18) Mwamuna, yemwe ndi mutu wa banja, ali ndi udindo waukulu wopezera banja lake zinthu zofunika komanso kuliphunzitsa zokhudza Mulungu. Mwamuna ayenera kusonyeza chikondi chololera kuvutikira mkazi wake. Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kukondana kwambiri komanso kulemekezana. Popeza kuti onse, mwamuna ndi mkazi, ndi anthu opanda ungwiro, ayenera kuphunzira kukhululukirana ndipo zimenezi zidzawathandiza kuti azikhala osangalala m’banja.—Werengani Aefeso 4:31, 32; 5:22-25, 33; 1 Petulo 3:7.
3. Ngati banja silikuyenda bwino, kodi ndi bwino kungolithawa?
Ngati mukuona kuti m’banja mwanu muli mavuto, aliyense wa inu ayesetse kusonyeza mnzake chikondi. (1 Akorinto 13:4, 5) Mawu a Mulungu salimbikitsa anthu okwatirana kuti azipatukana n’cholinga chothana ndi mavuto a m’banja mwawo.—Werengani 1 Akorinto 7:10-13.
4. Ananu, kodi Mulungu amafuna kuti muzichita chiyani?
Yehova amafuna kuti ananu muzikhala osangalala. Iye wakupatsani malangizo abwino kwambiri okuthandizani kuti muzisangalala pamene muli achinyamata. Mulungu akufuna kuti mupindule ndi nzeru za makolo anu komanso zinthu zimene iwowo akumana nazo pa moyo. (Akolose 3:20) Yehova, yemwe ndi Mlengi wanu, akufunanso kuti muzisangalala pochita zinthu zimene iye komanso Mwana wake akufuna.—Werengani Mlaliki 11:9–12:1; Mateyu 19:13-15; 21:15, 16.
5. Inu makolo, kodi mungatani kuti ana anu azikhala osangalala?
Muyenera kuyesetsa kuwapezera chakudya, pokhala ndiponso zovala. (1 Timoteyo 5:8) Koma kuti ana anuwo azikhala osangalala, muyeneranso kuwaphunzitsa kukonda Mulungu ndiponso kutengera chitsanzo chake. (Aefeso 6:4) Ngati inuyo mumakonda Mulungu, chitsanzo chanu chidzathandiza kwambiri ana anu kuti nawonso azikonda kwambiri Mulungu. Mukamalangiza ana anu pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, mungawathandize kwambiri anawo kuti aziona zinthu moyenera.—Werengani Deuteronomo 6:4-7; Miyambo 22:6.
Zimakhala zothandiza kwambiri kwa ana mukamawalimbikitsa komanso kuwayamikira. Koma akalakwitsa amafunika kuwapatsa chilango kapena kuwadzudzula. Zimenezi zingathandize kuti anawo azipewa makhalidwe omwe angachititse kuti azikhala osasangalala. (Miyambo 22:15) Komabe, si bwino kupatsa mwana chilango chokhwima kwambiri kapena kumulanga mwankhanza.—Werengani Akolose 3:21.
A Mboni za Yehova ali ndi mabuku osiyanasiyana omwe cholinga chake n’kuthandiza makolo komanso ana. Mfundo za m’mabuku amenewa ndi zochokera m’Baibulo.—Werengani Salimo 19:7, 11.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
BANJA LANU LIKHOZA KUKHALA LOSANGALALA
Muzidalira Kwambiri Mulungu
Kudzifunsa mafunso awiri okha kungathandize kuti banja lanu liziyenda bwino.
BANJA LANU LIKHOZA KUKHALA LOSANGALALA
Zimene Mungachite Pothetsa Mavuto
Zimene mumachita pothetsa mavuto zingachititse kuti banja lanu likhale lolimba komanso losangalala kapena ayi.
UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU