ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kutchova Juga

Kutchova Juga

Anthu ena amaona kuti kutchova juga kulibe vuto lililonse, pomwe ena amaona kuti ndi khalidwe loipa.

Kodi kutchova juga kuli ndi vuto lililonse?

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ambiri amaona kuti kutchova juga n’kosangalatsa komanso kulibe vuto lililonse ngati malamulo a dzikolo saletsa. Amati kutchova juga kwina, monga malotale, kumathandiza kuti anthu apeze ndalama.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

M’Baibulo mulibe mawu akuti kutchova juga. Komabe mfundo zina za m’Baibulo zingatithandize kudziwa mmene Mulungu amaonera nkhaniyi.

Anthu akamatchova juga, amapeza ndalama chifukwa choti anzawo aluza. Zimenezi n’zosemphana ndi chenjezo la m’Baibulo lakuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse.” (Luka 12:15) Munthu wotchova juga amafunitsitsa kuti ena aluze, iyeyo apeze phindu. Makampani a malotale akamalengeza za mpikisano, amangotchula ndalama zambiri zimene munthu angawine chifukwa amadziwa kuti anthu amafuna kulemera mwamsanga. Zimenezi zimapangitsa kuti anthu azibetcha ndalama zambiri m’malo otchovera juga. Komatu makampaniwa satsindika mfundo yoti ngakhale munthu yemwe walowetsa ndalama zambiri akhoza kuluza. Choncho, m’malo molimbikitsa anthu kupewa mtima wadyera, kutchova juga kumapangitsa anthu kuti azilakalaka atapeza ndalama zambiri m’kanthawi kochepa.

Anthu otchova juga amangoganizira phindu limene angapeze. Komatu Baibulo limanena kuti munthu “asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:24) Komanso pa Malamulo Khumi aja, lina limanena kuti: “Usalakelake . . . chilichonse cha mnzako.” (Ekisodo 20:17) Munthu wotchova juga amaganiza kuti iyeyo ndi amene awine n’kutenga ndalama za enawo.

Baibulo limatichenjezanso kuti tisamaganize kuti pali mphamvu inayake imene imapangitsa munthu kuchita mwayi. Mwachitsanzo, ku Isiraeli wakale, kunali anthu ena omwe anasiya kukhulupirira Yehova ndipo anayamba ‘kuyalira tebulo mulungu wa Mwayi.’ Koma Mulungu sanasangalale ndi zimenezi ndipo anawauza kuti: “Munapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga ndipo munasankha zinthu zimene sindisangalala nazo.”—Yesaya 65:11, 12.

N’zoona kuti m’mayiko ena, ndalama zomwe makampani amapeza akapangitsa mipikisano ya malotale amazigwiritsa ntchito kulipirira anthu sukulu, kukweza chuma cha dziko komanso pa ntchito zina zothandiza anthu. Koma zimenezi sizipangitsa kuti kutchova juga kukhale khalidwe labwino chifukwa monga taonera, khalidweli limalimbikitsa mtima wadyera komanso wodzikonda. Ndipo wotchova juga amafunitsitsa kuti anzake aluze n’cholinga choti iyeyo awine.

“Usalakelake . . . chilichonse cha mnzako.”Ekisodo 20:17.

Kodi munthu wotchova juga amakumana ndi mavuto otani?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limachenjeza kuti “anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambiri zowapweteketsa ndiponso amachita zinthu mopanda nzeru. Zinthu zimenezi zimawawononga ndi kuwabweretsera mavuto.” (1 Timoteyo 6:9) Dyera kapena umbombo ndi zimene zimapangitsa kuti anthu azitchova juga. Komatu makhalidwe amenewa ndi oipa kwambiri moti Baibulo limati tiyenera kuwapewa.—Aefeso 5:3.

Popeza anthu otchova juga amapeza ndalama zambiri osakhetsa thukuta, khalidweli limalimbikitsa kukonda ndalama. Komatu Baibulo limati “kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.” Kungapangitse munthu kuti azikhala ndi nkhawa komanso kuti asamakhulupirire Mulungu. Baibulo limati anthu okonda ndalama ‘amadzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.’—1 Timoteyo 6:10.

Mtima wadyera umapangitsa kuti munthu asamakhutire ndi zomwe ali nazo ndipo zimenezi zimachititsa kuti azikhala wosasangalala. Baibulo limati: “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.”—Mlaliki 5:10.

Anthu ambiri akayamba kutchova juga, amazolowera kwambiri khalidweli ndipo amalephera kulisiya. Kutchova juga ndi vuto lalikulu padziko lonse, ndipo kafukufuku amasonyeza kuti ku United States kokha kuli anthu mamiliyoni ambiri omwe amatchova juga.

Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Cholowa chopezedwa mwadyera poyamba, tsogolo lake silidzadalitsidwa.” (Miyambo 20:21) Anthu amene anazolowera kwambiri kutchova juga moti amalephera kusiya, amakhala ndi ngongole ndiponso mavuto azachuma. Khalidweli lingachititsenso kuti banja la munthu lithe, achotsedwe ntchito komanso kuti adane ndi anzake. Munthu akamatsatira mfundo za m’Baibulo amakhala wosangalala komanso amapewa mavuto amene amabwera chifukwa cha kutchova juga.

“Anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambiri zowapweteketsa ndiponso amachita zinthu mopanda nzeru. Zinthu zimenezi zimawawononga ndi kuwabweretsera mavuto.”1 Timoteyo 6:9.