Mlengi wathu si mphamvu chabe. Koma ali ndi makhalidwe ochititsa chidwi. Ndipo iye amafuna kuti tiphunzire za iyeyo komanso tikhale anzake. (Yohane 17:3; Yakobo 4:8) N’chifukwa chake amatiuza zambiri zokhudza iyeyo.
Baibulo limaphunzitsa kuti Yehova ndi Mulungu woona. Iye ndi amene analenga chilengedwe chonse komanso zamoyo zonse. Choncho iye yekha ndi amene tiyenera kumulambira.—Chivumbulutso 4:11.