Kodi Mungatani Kuti Mupirire Mavuto a M’Dzikoli?

Kodi Mungatani Kuti Mupirire Mavuto a M’Dzikoli?

Kodi mumaona kuti panopa mukuvutika kwambiri ndi mavuto a m’dzikoli kusiyana ndi kale? Kodi mavuto otsatirawa amachitikanso kumene mukukhala?

  • nkhondo

  • miliri

  • ngozi zam’chilengedwe

  • umphawi

  • tsankho

  • uchigawenga

Zinthu zoopsa zikachitika, anthu ambiri amakhala ndi mantha komanso amakhala opanda chiyembekezo. Anthu ena akakumana ndi mavuto aakulu, amasokonezeka kwambiri. Komatu kusokonezeka kwambiri chonchi, komanso kukhala ndi mantha kwa nthawi yaitali kumangowonjezera mavutowo.

Mukakumana ndi mavuto, muyenera kuchita zinthu mwanzeru kuti muteteze okondedwa anu, thanzi lanu, ndalama zanu komanso zimene zimakuthandizani kuti mukhale osangalala.

Kodi mungatani panopa kuti mavuto obwera chifukwa cha zomwe zikuchitika m’dzikoli asamakukhudzeni kwambiri?