KODI DZIKOLI LIDZAKHALANSO BWINO?

Nkhalango

Nkhalango

NKHALANGO zili ngati “mapapo a dziko, ndipo zimathandiza zinthu za m’dzikoli kukhala ndi moyo.” Zimenezi ndi zomveka chifukwa mitengo imatenga mpweya wa kaboni dayokisaidi, umene ukhoza kutivulaza. Mitengo imatulutsanso okosijeni, womwe ndi mpweya wofunika kwambiri umene timapuma. Pafupifupi 80 peresenti ya zomera komanso nyama zapamtunda zimakhala m’nkhalango. Popanda nkhalango sitingakhale ndi moyo.

Nkhalango Zili Pachiopsezo

Chaka chilichonse anthu amadula mitengo mabiliyoni ambiri kuti apeze malo olima. Kungoyambira chakumapeto kwa zaka za m’ma 1940, pafupifupi hafu ya nkhalango zonse zikuluzikulu padzikoli zinatha.

Nkhalango ikawonongedwa, zomera ndi nyama zonse zomwe zimakhalamo zimatha.

Dzikoli Linapangidwa M’njira Yoti Lizitha Kudzikonza Lokha

Nkhalango zina zimene zinawonongedwa zinabwereranso ndipo zina zinakula kwambiri kuposa mmene zinalili poyamba. Akatswiri azachilengedwe adabwa kwambiri kuzindikira kuti pasanapite nthawi yaitali, nkhalango zimene zinawonongedwa zimayambiranso kukula n’kukhala nkhalango zazikulu kwambiri. Taganizirani zitsanzo zotsatirazi:

  • Akatswiri anayamba kuchita kafukufuku pamalo amene anthu anagwetsa nkhalango kuti apeze malo olima koma kenako anthuwo anangosiya malowo osalimaponso. Kafukufukuyu yemwe anachitika ku America ndi ku West Africa pamalo osiyanasiyana oterewa okwana 2,200, anasonyeza kuti nthaka ikhoza kubwerera mwakale kuti ithandize nkhalango kuyambiranso kukula pomatha zaka 10.

  • Akatswiriwa ananena kuti pomatha zaka 100, nkhalangozi zikhoza kukhala zitabwerera mwakale ndipo mitengo ndi zamoyo zina zimene zinkakhalamo zikhoza kubwereranso.—Science magazine.

  • Chaposachedwapa, akatswiri asayansi ku Brazil anayerekezera nkhalango zimene anangozisiya kuti zibwerere zokha ndi nkhalango zimene anthu anapitako kuti akadzale mitengo kuti aone kuti ndi ziti zimene zingakule msanga.

  • A National Geographic anapereka lipoti pa zimene akatswiriwa ankafufuzazi. Iwo anati: “Anadabwa kwambiri kuzindikira kuti sankachita kufunika kudzala mitengo.” M’zaka 5 zokha anapeza kuti malo amene anayesedwa aja “anali ndi mitengo yambiri yachilengedwe” ngakhale kuti sanadzalepo mtengo uliwonse.

Zimene Anthu Akuchita Kuti Athetse Vutoli

Padziko lonse, anthu akuyesetsa kusamalira nkhalango zimene zilipo komanso akuyesetsa kuti abwezeretse nkhalango zimene zinawonongedwa. Lipoti lina la bungwe la United Nations linanena kuti chifukwa cha zimenezi, “padziko lonse anthu achepetsa kudula mitengo ya m’nkhalango ndi 50 peresenti,” poyerekezera ndi zaka 25 zapitazi.

Komatu zimenezi si zokwanira kuti titeteze nkhalango zathu. Lipoti la bungwe lina linanena kuti: “Chiwerengero cha nkhalango zimene zikuwonongedwa sichinasinthe kwambiri m’zaka zochepa zapitazi.”—Global Forest Watch.

Makampani ambiri amagwetsa mitengo popanda chilolezo cha boma ndipo amapanga ndalama mabiliyoni ambiri. Dyera lawoli likuchititsa kuti nkhalango zambiri ziwonongedwe.

Anthu amene amagwira ntchito yosamalira nkhalango amadula mitengo imene yakhwima n’kudzala ina

Kodi Baibulo Limatipatsa Chiyembekezo Chotani?

“Yehova a Mulungu anameretsa munthaka mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino komanso wazipatso zabwino kudya.” —Genesis 2:9.

Mlengi wa nkhalango zonse anazikonza m’njira yoti zizitha kudzibwezeretsa zokha ngakhale anthu ataziwononga. Iye amafuna kuti nkhalangozi limodzi ndi zamoyo zonse zomwe anazipanga modabwitsa zimene zimakhalamo zisathe.

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu sadzalola kuti anthu odzikonda apitirize kuwononga dzikoli komanso zamoyo. Onani nkhani yakuti “Mulungu Akulonjeza Kuti Dzikoli Lidzakhalanso Bwino,” patsamba 15.

a Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.